Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusefukira kwa Madzi ku Japan Zimene Anthu Opulumuka Anafotokoza

Kusefukira kwa Madzi ku Japan Zimene Anthu Opulumuka Anafotokoza

Kusefukira kwa Madzi ku Japan Zimene Anthu Opulumuka Anafotokoza

Nkhaniyi ikunena za anthu amene anapulumuka chivomezi komanso madzi osefukira ku Japan m’chaka cha 2011.

LACHISANU pa March 11, 2011, nthawi ili 2:46 masana, ku Japan kunachitika chivomezi chachikulu. Chivomezi chimenechi ndi chachinayi pa zivomezi zazikulu kwambiri zimene zachitikapo padziko lonse. Chivomezichi chinachititsa kuti madzi asefukire m’madera ambiri. Chitatha panachitikanso zivomezi zina zing’onozing’ono kwa milungu ingapo. Anthu amene anafa kapena kusowa, onse pamodzi anali pafupifupi 20,000. M’nkhaniyi anthu ena amene anapulumuka afotokoza zimene zinachitika.

Pa nthawi imene chivomezichi chinayamba, Tadayuki ndi mkazi wake, Harumi, anali kunyumba kwawo ku Ishinomaki, mumzinda wa Miyagi. Pasanapite nthawi yaitali, nyumba yawo inayamba kugwedezeka mwamphamvu. Iwo anati: “Titathamangira panja tinachita mantha kuona nthaka ikung’ambika. Kenako nyumba yathu inayamba kugwedezeka mpaka makoma ake anagwa ndipo panali fumbi lokhalokha.”

Malo enieni amene chivomezichi chinachitikira anali pa mtunda makilomita 129 kuchokera ku Miyagi. Chivomezicho chitachitika, madzi anasefukira dera lalikulu makilomita 670. M’madera ena mafunde amene ankafika kumtunda ankakhala aatali mpaka mamita 15, ndipo madziwo anakokolola zinthu zonse zimene zinali pafupi ndi nyanja pa mtunda wa makilomita 40.

Zimenezi zitangochitika, kunalibe magetsi, madzi, komanso gasi wophikira. Mafakitale, mashopu ndiponso nyumba pafupifupi 160,000, zinakokoloka komanso kuwonongekeratu. Pa nthawi ina, zinafika poti anthu oposa 440,000 ankakhala m’zisakasa zokwana 2,500 zomwe zinamangidwa m’masukulu ndi m’malo ena. Anthu ambiri amene nyumba zawo zinakokoloka ankasungidwa ndi anzawo kapena abale awo. Anthu masauzande ambiri anafa ndipo ena mitembo yawo sinapezekenso.

Linali Tsoka Lalikulu Kwambiri

Madzi osefukira ndi amene anapha anthu ambiri kuposa chivomezi. Yoichi, yemwe ankakhala ku Rikuzentakata, mumzinda wa Iwate, atangozindikira kuti kukuchitika chivomezi anadziwa kuti madzi asefukira posachedwa ndipo anasamutsira makolo ake pamsasa wina wapafupi. Kenako anapita kukaona anthu oyandikana nawo nyumba, koma popeza ankaderabe nkhawa makolo ake, Yoichi ndi mkazi wake, Yatsuko, anaganiza zobwereranso kukaona makolo ake koma anauzidwa kuti madzi osefukira aja ayandikira kwambiri.

Mwamsanga anathawira pamsasa wina koma analephera kulowa mkati chifukwa polowera panali patadzaza zinyalala. Kenako anaona chipupa cha nyumba ina yopalira matabwa chitatengedwa ndi madzi. Yatsuko anakuwa kwambiri kuti, “Thawani!”

Kenako iwo anakafika pasukulu inayake yomwe inamangidwa pamalo okwera kwambiri. Ali pamalo amenewa, anaona madzi osefukirawo akukokolola nyumba zonse. Munthu wina ananena kuti: “Nyumba yanga ikugwa,” Pafupifupi mudzi wonse wa Rikuzentakata unawonongedwa ndipo ngakhale makolo a Yoichi anatengedwa ndi madzi. Mtembo wa mayi ake unapezeka koma wa bambo ake sunapezeke.

Pa nthawi imene chivomezichi chimachitika, Toru anali akugwira ntchito pa fakitale inayake mumzinda wa Ishinomaki. Mphamvu ya chivomezi itayamba kuchepa, anatenga galimoto yake n’kuyamba kuiyendetsa mothamanga kwambiri. Anakuwa kwambiri pochenjeza anthu kuti athawe chifukwa ankadziwa kuti sipapita nthawi yaitali madzi asanasefukire.

Toru anati: “Choyamba ndinaganiza zopita kunyumba yanga, yomwe ili m’dera lokwererapo, koma mumsewu munali magalimoto ambiri. Kenako ndinamva akulengeza pa wailesi kuti madzi osefukirawo afika kale mumzinda wapafupi. Ndinatsegula windo la galimoto yanga n’cholinga choti ngati madziwo afika kale, ndingotuluka n’kuthawa. Pasanapite nthawi yaitali ndinaona madzi ambiri amatope okhaokha akubwera poteropo. Kenako madziwo anakokolola magalimoto onse amene anali kutsogolo kwanga ndi galimoto yanga yomwe n’kukatitayira kumtunda.

“Ndinatuluka m’galimoto yangayo kudzera pawindo koma movutikira kwambiri, ndipo nditangotuluka ndinakokolokanso ndi madzi omwe ankanunkha mafuta okhaokha. Madziwo anakanditaya kunyumba inayake komwe amakonzako magalimoto. Kuti ndipulumuke ndinagwira zitsulo za nyumbayo, yomwe inali yosanja, mpaka kukafika kusiteya yachiwiri. Ndinakwanitsa kupulumutsa anthu atatu koma anthu ambiri anapita ndi madzi osefukira komanso anafa ndi chisanu.”

Chivomezichi chisanachitike, Midori, yemwe amakhala ku Kamaishi, mumzinda wa Iwate, anapita kokaona agogo ake aamuna ndi aakazi. Iye anali atangomaliza kumene sukulu ya sekondale ndipo anapita kukasonyeza agogo akewo satifiketi yake. Iwo anasangalala kwambiri moti anawerenga mokweza mawu a pa satifiketipo. Koma chisangalalocho chinali chosakhalitsa, chifukwa patangotha masiku asanu kunachitika chivomezi.

Chivomezichi chitachitika, Midori ndi mayi ake a Yuko, anauza agogowo kuti asamukire kudera lina chifukwa iwo ankadziwa kuti madzi osefukira afika m’deralo. Koma agogowo anakana chifukwa ankaganiza kuti madziwo sangasefukire mpaka kufika kumene amakhala. Popeza kuti agogowo sankakwanitsa kuyenda, Midori ndi mayi ake anayesetsa kuwanyamula koma sanawakwanitse. Kenako anayamba kufufuza anthu oti awathandize. Koma pa nthawiyi n’kuti madzi osefukira atafika kale. Anthu ena omwe amakhala paphiri lina lapafupi anakuwa kuti: “Fulumirani! Thamangani!” Pa nthawiyi n’kuti nyumba zitayamba kumira. Midori anayamba kulira kuti: “Agogo! Agogo!” Agogo ake aamuna ndi aakazi anafa ndi madzi osefukirawo, ndipo mtembo wa agogo aakaziwo sunapezeke.

Kupereka Chithandizo

Boma la Japan mwamsanga linatumiza apolisi, asilikali ndiponso anthu ozimitsa moto kumadera konse komwe kunasefukira madzi. M’kanthawi kochepa chabe, anthu oposa 130,000 anayamba kugwira ntchito yofufuza ndi kupulumutsa anthu. Kenako, mayiko ndi mabungwe ena anayamba kutumiza madokotala ndi anthu ogwira ntchito zosiyanasiyana kudzathandiza. Anthuwa ankagwira ntchito yofufuza ndi kupulumutsa anthu, kuthandiza anthu amene avulala komanso kuchotsa zinyalala.

Magulu osiyanasiyana, kuphatikizapo a Mboni za Yehova, anathandiza anthu awo amene anakhudzidwa ndi vutoli. Kutangochitika chivomezi komanso madzi atayamba kusefukira, a Mboni za Yehova anayamba kufufuza kuti aone ngati anthu amene amalambira nawo limodzi akhudzidwa ndi vutoli. Koma zinali zovuta kuwapeza chifukwa misewu yambiri inali itawonongekeratu, kunalibe magetsi komanso matelefoni samagwira ntchito. Choncho, zinali zovuta kwambiri kudziwa anthu amene akhudzidwa.

Komabe Takayuki, yemwe ndi mkulu mumpingo wa Mboni za Yehova ku Soma, mumzinda wa Fukushima, anakwanitsa kuyendera mabanja ochepa a Mboni za Yehova madzulo a Lachisanu limene chivomezichi chinachitika. Iye anati: “Ndinakonza zoti ndiyendere mabanja ena tsiku lotsatira. Ndinalawira m’mbandakucha kuyamba ulendo woyendera mabanja osiyanasiyana pagalimoto kenako ndinayamba kuyenda pansi, moti ndinafika madzulo ndikuyendabe. Ndinafufuza anthu a Mboni m’malo osiyanasiyana okwana 20, ndi m’misasa momwe. Ndikawapeza, ndinkawalimbikitsa powawerengera malemba komanso ndinkapemphera nawo limodzi.”

Shunji, yemwe ndi wa ku Ishinomaki, anafotokoza kuti: “Tinakhazikitsa magulu ofufuza Akhristu anzathu. Titafika kudera kumene kunachitika tsokali, tinali ndi chisoni kwambiri. Tinaona magalimoto atatsakamira m’mitengo ya magetsi, nyumba zitagweranagwerana komanso nyumba zambiri zinali zitakwiririka ndi zinyalala. Pamwamba pa galimoto ina tinaonapo munthu wakufa, ndipo n’kutheka kuti anafa ndi chisanu. Pakati pa nyumba zina ziwiri, tinaona galimoto itatembenuzika ndipo mkati mwake munali munthu wakufa.”

Shunji anasangalala atapezana ndi Akhristu anzake omwe anali m’misasa. Iye anati: “Nditawapeza, ndinkamva bwino kwambiri mumtima mwanga.”

“Sitimadziwa Kuti Mubwera Mofulumira Chonchi!”

Atsikana awiri a Mboni, Yui ndi Mizuki, ankakhala nyumba zoyandikana ku Minamisanriku, mumzinda wa Miyagi. Chivomezichi chitachitika, onse anathawira kumalo enaake okwera. Pasanathe ndi mphindi 10 zomwe, anaona nyumba zawo ndi tawuni yawo yonse ikukokoloka ndi madzi.

Pamene Yui ndi Mizuki anakumana ndi anzawo a Mboni pamsasapo anasangalala kwambiri ndipo anapemphera limodzi. M’mawa wotsatira, anthu a mumpingo wawo komanso ena a m’mipingo yapafupi anadutsa njira za m’mapiri n’cholinga choti adzawapatse chakudya. Anthu a mumpingo wina wa pafupi anawabweretseranso chakudya ndi zinthu zina. Yui ndi Mizuki ananena kuti: “Timadziwa kuti mubwera koma sitimadziwa kuti mubwera mofulumira chonchi.”

Hideharu, yemwe ndi mmodzi wa akulu mumpingo wa Mboni za Yehova wa ku Tome, anayendera msasawu. Iye anati: “Tinatha usiku wonse tikufufuza anzathu omwe ankakhala kufupi ndi kugombe. Kenako nthawi ili 4 koloko m’mawa tinalandira uthenga wotiuza kuti abale ena athawira pasukulu inayake. Mmene nthawi imati 7 koloko m’mawa, anthu pafupifupi 10 tinayamba kuphika chakudya ndipo anthu atatu tinanyamula chakudyacho pagalimoto kuti tikapereke kwa abale athu amene anali pasukuluyo. Koma misewu yambiri inali itawonongekeratu moti tinafika pasukulupo movutikira kwambiri. Ngakhale anthu amene nyumba zawo zinawonongeka, anatithandiza pa ntchito yopereka chithandizo kwa ena.”

Kuthandiza Anthu Mwauzimu

Mboni za Yehova zimakumana kawirikawiri n’cholinga chophunzira Baibulo ndipo mpingo wa ku Rikuzentakata umakumana Lachisanu madzulo, lomwe ndi tsiku limenenso kunachitika chivomezichi. Ngakhale kuti Nyumba ya Ufumu inali itakokoloka ndi madzi, anthu a mumpingo umenewu anachitabe misonkhano yawo. Munthu wina wa Mboni anauza anzake kuti: “Ndikuona kuti tichitebe misonkhano.” Choncho anasankha nyumba inayake imene sinawonongeke kwambiri kuti achitiremo misonkhanoyo, ndipo kenako anawadziwitsa anthu za malowo.

Popeza kuti kunalibe magetsi, anagwiritsa ntchito jeneleta. Pamsonkhanowu panafika anthu 16. Mnyamata wina dzina lake Yasuyuki, yemwe nyumba yake inakokoloka ndi madzi, anati: “Tinasangalala kwambiri mpaka kufika pogwetsa misozi. Amenewa anali malo abwino kwambiri othawirako.” Munthu winanso, dzina lake Hideko, anati: “Pa nthawi ya msonkhanowu pankachitikabe tizivomezi ting’onoting’ono, komabe chifukwa chakuti tinali pamodzi, mantha amene ndinali nawo poyamba anandithera.”

Pa nthawi yonseyi, anthu a mumpingowu akhala akuchita misonkhano yawo yonse popanda kuphonya. Patapita masiku awiri kuchokera pamene chivomezichi chinachitika, pampingopo panakambidwa nkhani yakuti: “Ubale wa Padziko Lonse Udzapulumuka Tsoka.”

Ntchito Yopereka Thandizo

Nthambi zosiyanasiyana za boma zinayamba ntchito yopereka chithandizo kwa anthu amene nyumba zawo zinakokoloka ndi madzi. Nayonso ofesi ya Mboni za Yehova yomwe ili ku Ebina, pafupi ndi mzinda wa Tokyo, inachita chimodzimodzi. Tsiku lotsatira, ofesiyo inagawa dera limene linakhudzidwa ndi tsokalo m’magawo atatu. Lolemba lake, anthu atatu ochokera ku ofesiyi anayendera dera lonselo.

Ntchito yopereka chithandizo inachitika kwa miyezo ingapo. Mboni za Yehova zinapereka zinthu zambiri zothandizira anthu amene anakhudzidwa ndi vutoli. Pa nthawi ina, chithandizochi chinkaperekedwa m’malo akuluakulu atatu ndi malo enanso ambiri. Panalinso malo oposa 21 osungiramo zinthu zachithandizo. M’miyezi iwiri yoyambirira, anthu ongodzipereka anagawa zakudya, zovala ndi zinthu zina zokwana matani 250. Mboni za Yehova zambiri zinkagawana zinthu ngati zimenezi ndi anthu ena amene anakhudzidwanso.

Anthu a mumpingo wa Mboni za Yehova wa ku Rikuzentakata ndi wa ku Ofunato anakonzanso Nyumba ya Ufumu yawo ndipo akumachitiramo misonkhano imene cholinga chake n’kulimbikitsa anthu mwauzimu. Zimenezi zithandiza anthu a m’deralo kupirira mavuto amene akukumana nawo komanso kuti asataye mtima kwambiri chifukwa cha tsoka limene anakumana nalo. Pa anthu a Mboni za Yehova okwana 14,000 a m’derali, 12 anafa ndipo awiri sanapezekebe.

Anthu ambiri a Mboni za Yehova amene anakhudzidwa ndi tsokali, ananena mawu ofanana ndi amene banja lina linanena. Banjali linati: “Pamene tinkathawa, tinangonyamula zinthu zochepa chabe. Koma okhulupirira anzathu anatipatsa zosowa zathu zonse.” N’zosangalatsa kwambiri kuti atumiki a Mulungu woona, Yehova, akusonyezana chikondi chimene Yesu ndi atumwi ake ankaphunzitsa. Chikondi chimenechi sichingasokonekere chifukwa cha kusefukira kwa madzi kapena vuto lina lililonse.—Yohane 13:34, 35; Aheberi 10:24, 25; 1 Petulo 5:9.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

KUPHULIKA KWA FAKITALE YA KU FUKUSHIMA

Nkhani yakuti madzi osefukira anawononga fakitale ya mpweya wa nyukiliya ya ku Fukushima, inadziwika padziko lonse. Poizoni wochokera m’fakitale imeneyi, anafalikira ku Japan komanso m’mayiko ena oyandikana nawo. Anthu ambiri anasamutsidwa chifukwa chakuti poizoni ameneyu ndi woopsa kwambiri.

Megumi anafotokoza kuti: “Nyumba yathu inali pafupi ndi fakitale imeneyi. Tinadziwa kuti fakitaleyi yaphulika patatha tsiku limodzi kuchokera pamene chivomezi chija chinachitika ndipo zitatero tinauzidwa kuti tisamuke.” Mchemwali wake, Natsumi, anati: “Tinkaona ndege zikuuluka m’mwamba zikuliza masayilini, ndiponso anthu a m’ndegezo ankatichenjeza kuti tithawe.” Milungu yotsatira anthu a m’derali anawasamutsira kumadera ena osiyanasiyana okwana 9. Patapita nthawi atsikana awiriwa anawalola kuti abwerere kwawo kukatenga katundu wawo koma anauzidwa kuti achite zimenezi m’maola awiri okha.

Mayi wina wazaka za m’ma 60, dzina lake Chikako, anali ali ku Namie, mumzinda wa Fukushima, komwe kunaphulika fakitaleyi. Iye anati: “Chivomezichi chitachitika, ndinathawira kumsasa wina wapafupi umene anakonzera anthu omwe anakhudzidwa ndi tsokali. Ine ndi ana anga awiri tinagona kumsasawu koma tulo sitinkabwera chifukwa chakuti kunkachitikabe tizivomezi ting’onoting’ono. Tsiku lotsatira, nthawi ili 7 koloko m’mawa, tinauzidwa kuti tithawire kumsasa wa mumzinda wina mwamsanga.

“Koma m’misewu munali mutadzaza magalimoto, ndipo chifukwa cha zimenezi tinakafika kumsasa winawo 3 koloko masana. Tili kumeneko tinamva za kuphulika kwa fakitaleyi. Tinkaganiza kuti tibwerera kunyumba posachedwa, choncho popita kumsasawu sitinatenge chilichonse.” Mayiyu ndi banja lake ankangosamukasamuka mpaka pamene anapeza nyumba kutali kwambiri ndi kwawo.

[Mawu a Chithunzi]

Photo by DigitalGlobe via Getty Images

[Chithunzi patsamba 20]

ZIMENE TONSEFE TINGAPHUNZIREPO

Yoichi, yemwe tamutchula kale uja, katundu wake wambiri anakokoloka ndi madzi. Iye anati: “Kunena zoona, ndaona kuti katundu sachititsa munthu kukhala wosangalala.” Mfundo imeneyi yakhala ikunenedwanso ndi atumiki ambiri a Mulungu, makamaka amene anamvetsa zimene Yesu ankaphunzitsa. Yesu anafotokoza kuti chuma sichithandiza kwenikweni poyerekeza ndi kudalitsidwa ndi Mulungu komanso kukhala naye pa ubwenzi.—Mateyu 6:19, 20, 33, 34.

Chinthu china chimene tikuphunzirapo pa nkhani imeneyi n’chakuti tizimvera tikachenjezedwa za tsoka limene likubwera. Mwachitsanzo, chivomezi chitachitika ku Japan anthu ambiri amene anathawira mwamsanga kumalo okwera anapulumuka, pamene anthu amene anazengereza kapena kunyalanyaza chenjezo anafa.

[Mapu/Zithunzi patsamba 16]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

JAPAN

TOKYO

Kamaishi

Rikuzentakata

Ishinomaki

Minamisanriku

Soma

Fakitale ya ku Fukushima

Ebina

Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Japan

[Zithunzi]

Rikuzentakata, Iwate

Soma, Fukushima

Ishinomaki, Miyagi

Kamaishi, Iwate

Minamisanriku, Miyagi

[Chithunzi patsamba 14]

Harumi ndi Tadayuki

[Chithunzi patsamba 15]

Yoichi ndi Tatsuko

[Chithunzi patsamba 17]

Toru

[Chithunzi patsamba 17]

Galimoto imene Toru ankayendetsa

[Chithunzi patsamba 17]

Yuko ndi Midori

[Chithunzi patsamba 17]

Takayuki

[Chithunzi patsamba 18]

Shunji

[Chithunzi patsamba 19]

Mizuki ndi Yui

[Chithunzi patsamba 19]

Hideharu

[Chithunzi patsamba 19]

Anthu akugwira ntchito yongodzipereka

[Chithunzi patsamba 20]

Nyumba ya Ufumu ya ku Rikuzentakata itawonongeka ndi madzi

[Chithunzi patsamba 20]

Ntchito yomanganso Nyumba ya Ufumu, patapita miyezi itatu

[Chithunzi patsamba 20]

Nyumba ya Ufumu itamalizidwa

[Chithunzi patsamba 14]

JIJI PRESS/AFP/Getty Images