Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Ku England, makina a ATM amene anthu amatengerapo ndalama amakhala ndi tizilombo toyambitsa matenda tochuluka mofanana ndi tizilombo timene timapezeka pa zimbudzi zimene zimagwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri.—THE TELEGRAPH, BRITAIN.
“Nthawi zina asayansi amadabwa ndi zivomezi [ngati chomwe chinachitika chaka chino ku New Zealand, komanso chaka chatha ku Haiti] chifukwa zivomezizo zimachitika m’madera amene samayembekezera kuti mungachitike zivomezi . . . . Zimenezi zikubweretsa funso lodetsa nkhawa ili: Kodi ndi zivomezi zingati zimene zikhoza kuchitika m’tsogolomu m’madera amene anthu saganizira kapena sadziwa n’komwe kuti mungachitike zivomezi?”—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.
“Anthu anayi olemera kwambiri padziko lonse . . . ali ndi chuma choposa cha mayiko 57 osauka kwambiri.”—FOREIGN POLICY, January/February 2011, U.S.A.
Anthu 90 pa 100 alionse a bizinezi ku Poland ananena kuti antchito awo anawabera kapena kuwapusitsa m’njira inayake m’zaka ziwiri zapitazi.—GAZETA PRACA, POLAND.
Tchalitchi china cha Katolika ku Brazil chayamba kulipitsa anthu ofuna kukwatirana ndalama zokwana madola 300, ngati afika mochedwa kumalo odalitsira ukwati. Anthu okwatiranawo ayenera kulemba cheke mwambo wa ukwatiwo usanayambe ndipo amawabwezera chekecho ngati asunga nthawi.—G1, BRAZIL.
Papa Sangapereke Chiwalo kwa Munthu Wodwala
Nyuzipepala ya ku Italy yotchedwa La Repubblica inanena kuti pa nthawi yomwe Joseph Ratzinger anali kadinala wa tchalitchi cha Katolika ankaloledwa kupereka chiwalo kwa wodwala. Koma atangosankhidwa kukhala Papa Benedict wa nambala 16, sakuloledwanso kuchita zimenezi. Chifukwa chiyani? Malinga ndi zimene bishopu wina, dzina lake Zygmunt Zimowski,yemwenso ndi mmodzi wa akuluakulu a ku Vatican, ananena, “thupi la papa ndi la tchalitchi chonse. Choncho ndi bwino kuti papa akamwalira thupi lake lizikhala ndi ziwalo zonse chifukwa n’zotheka kuti m’tsogolo anthu angamadzalilambire.”
Kusinthanitsa Moyo ndi Ndalama
Kodi munthu angalolere kufa mofulumirirapo ndi chaka chimodzi kuti apatsidwe ndalama zankhaninkhani? Pa kafukufuku amene bungwe lina linachita ku Germany, mwamuna mmodzi pa amuna anayi alionse, komanso mkazi mmodzi pa akazi 6 alionse, ananena kuti angachite zimenezo. Pa kafukufukuyu, anthu ambiri amene anali ndi maganizo amenewa anali azaka zocheperapo. (Anthu 29 pa 100 alionse azaka zapakati pa 14 ndi 29 ananena kuti angalolere kupatsidwa ndalamazi, ndipo anthu 25 pa 100 alionse azaka zapakati pa 30 ndi 39 ananena kuti angalole kuchita zimenezi.) Koma kafukufukuyu anasonyeza kuti pamene munthu akukula, amaona kuti moyo ndi wofunika kwambiri. (Anthu 13 pa 100 alionse azaka zapakati pa 50 ndi 59, ananena kuti angalolere kupatsidwa ndalamazi, ndipo anthu 11 pa 100 alionse azaka zopitirira 60 ananena kuti angachite zimenezi.)