Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Zithunzizi Zikusiyana Pati?

Kodi mungatchule zinthu zitatu zimene zikusiyana pakati pa chithunzi A ndi chithunzi B? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yesaya 6:1-8.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. Kodi chithunzi cholondola n’chiti, A kapena B?

KAMBIRANANI:

Kodi Yesaya anali ndi maganizo abwino otani? Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu wodzichepetsa komanso wodzipereka?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 110:3; Mateyu 28:19, 20.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Aliyense m’banja mwanu afufuze ntchito zimene angelo amagwira. Kenako afotokoze zimene wapeza. Mwachitsanzo, kodi ntchito zina za angelo ndi zotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 34:7; Aheberi 1:14; Chivumbulutso 14:6, 7.

Kodi angelo amagwira ntchito m’magulu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 103:19-21.

Kodi angelo ndi odzichepetsa komanso ofunitsitsa kuthandiza ena?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Oweruza 13:17, 18; Luka 22:43; Chivumbulutso 22:8, 9.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 12 YESAYA

MAFUNSO

A. Ndani anapita ndi Yesaya kokapereka uthenga kwa Mfumu Ahazi?

B. Kodi Yesaya anayankha bwanji Yehova atafunsa kuti “Kodi nditumiza ndani?”

C. Yesaya analosera kuti: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi . . . ”

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa Anakhala ndi Baibulo

kwa Adamu moyo cha m’ma linamalizidwa

700 B.C.E. kulembedwa

[Mapu]

Ankakhala ku Yerusalemu

Yerusalemu

YESAYA

ANALI NDANI?

Anali mneneri wokhulupirika, yemwe ankathandiza banja lake kulambira Mulungu. Ankasonyeza banja lake chitsanzo chabwino pochita utumiki wake mokhulupirika. Mkazi wake analinso “mneneri.” (Yesaya 7:3; 8:3, 18) Yesaya anatumikira Mulungu kwa zaka zoposa 46. Dzina lake limatanthauza “Chipulumutso cha Yehova.”

MAYANKHO

A. Mwana wake, Seari-yasubu.—Yesaya 7:3.

B. “Ine ndilipo! Nditumizeni.”—Yesaya 6:8.

C. “. . .anthu odziwa Yehova.”—Yesaya 11:9.

Anthu ndi Mayiko

5. Mayina athu ndi Abigail ndi Jeriah ndipo tili ndi zaka 9 ndi 7. Timakhala ku India. Kodi mukudziwa kuti ku India kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 31,500; 59,600 kapena 86,000?

6. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la India.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti, “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa Webusaiti ya www.pr418.com.

● “Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 20

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Mngelo wa pa chithunzi chimodzi ali ndi mapiko 6 koma mngelo wa pa chithunzi china ali ndi mapiko anayi okha.

2. Mngelo wa pa chithunzi chimodzi ali ndi chopanira pamene mngelo wa pa chithunzi chinacho ali ndi lupanga.

3. Pa chithunzi chimodzi khala lakhudza pakamwa pa Yesaya koma pa chithunzi chinacho lakhudza dzanja lake.

4. B.

5. 31,500.

6. B.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

La Voz de Galicia/Fotógrafo: Víctor Mejuto