Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadziwa Chikondi cha Mulungu

Anadziwa Chikondi cha Mulungu

Anadziwa Chikondi cha Mulungu

● Yesu anaphunzitsa mfundo imene imatithandiza kumvetsa kukula kwa chikondi cha Mulungu. Iye anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha [Yesu], kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kukula kwa chikondi cha Mulungu komanso chiyembekezo cha moyo wosatha chimene tili nacho chifukwa cha imfa ya Mwana wake, zafotokozedwa mwatsatanetsatane m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova.

Mayi wina wa ku Florida, m’dziko la United States, analemba kuti: “Nditawerenga mutu 5 wa bukuli, ndinagoma kwambiri ndi chikondi cha Yehova, nzeru komanso mphamvu zake. Ndipo ndinayamba kumukonda kwambiri nditaganizira mwakuya zinthu zimene iye analenga.” Mayi wina wa ku South Dakota, ku United States komweko, anafotokoza kuti: “Kwa zaka zoposa 30, zinkandivuta kwambiri kukonda anthu ena (kapena kuona kuti anthu ena amandikonda). Koma buku limeneli likundithandiza kwambiri kuposa buku lina lililonse.”

Buku lamasamba 320 lakuti Yandikirani kwa Yehova, limafotokoza makhalidwe anayi akuluakulu a Mulungu, omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru ndi chikondi. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi, n’kutumiza ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.