Chinyengo Chili Paliponse
Chinyengo Chili Paliponse
Danny, * yemwe amagwira ntchito pakampani inayake yaikulu ku Hong Kong, anapita ku fakitale ina yomwe inkafuna kuti izigulitsa katundu wake ku kampani ya Danny. Atayendera fakitaleyo, Danny ananena kuti akukayikira ngati katundu amene fakitaleyo imapanga angagwirizane ndi zofuna za kampani ya Danny. Kenako, panthawi ya chakudya chamadzulo, bwana wa fakitale ija anapatsa Danny envulopu. Mkati mwa envulopuyo munali ndalama zankhaninkhani zomwe anamupatsa ngati chiphuphu. Ndalamazi zinali zokwana pafupifupi ndalama zonse zimene Danny amalandira pachaka.
● Zimene Danny anakumana nazo si zachilendo. Chinyengo chili paliponse m’dzikoli. Mwachitsanzo, zikalata za khoti lina ku Germany, zinasonyeza kuti kuyambira m’chaka cha 2001 mpaka 2007, kampani ina yopanga katundu m’dzikolo inapereka ndalama zokwana madola 1.4 biliyoni za ziphuphu ku makampani ena n’cholinga choti kampaniyi izigulitsa katundu wake ku makampaniwo.
Ngakhale kuti posachedwapa nkhani za chinyengo chokhudza makampani akuluakulu zachititsa kuti pakhazikitsidwe malamulo okhwima, zikuoneka kuti chinyengo chikuwonjezerekabe. Kafukufuku amene bungwe lina linachita m’chaka cha 2010, anasonyeza kuti padziko lonse, “chiwerengero cha anthu ochita zachinyengo chawonjezereka kwambiri m’zaka zitatu zapitazi.”—Transparency International
N’chifukwa chiyani chinyengo chili paliponse masiku ano? Kodi kuchita zinthu mwachilungamo n’kothandiza? Ndipo kodi n’zothekadi kuchita zinthu mwachilungamo nthawi zonse? Kodi Baibulo lingatithandize pa nkhani imeneyi?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Mayina ena tawasintha.