Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitoliro Chimene Chimatulutsa Tinyimbo Tanthetemya

Chitoliro Chimene Chimatulutsa Tinyimbo Tanthetemya

Chitoliro Chimene Chimatulutsa Tinyimbo Tanthetemya

KWA zaka zambiri, anthu ena amene amakhala kumapiri a Alps ku Switzerland, akhala akugwiritsa ntchito zitoliro zamtundu winawake zopangidwa kuchokera ku mtengo akafuna kutumiza uthenga. Chitolirochi chimaoneka kuti ndi chovuta kunyamula chifukwa chimakhala chachitali, mwina kutalika kuposa munthu amene akuchiimba. Komabe munthu amatha kunyamula chitolirochi m’manja chifukwa chimapangidwa moti akhoza kuchigulula n’kuchiika m’chikwama. Chitolirochi chimatha kumveka pamtunda wamakilomita 10 m’mapiri a ku Alps.

Kapangidwe Kake

Chitolirochi chimapangidwa kuchokera ku mitengo inayake yomwe ndi yofala kwambiri m’mapiri a Alps. Mitengoyi imakhala yaikulu kutsinde chifukwa cha nyengo komanso malo amene imamera.

Opanga chitolirochi amati akapeza mtengo wabwino, amaudula kenako n’kuung’amba pakati. Mbali iliyonse amaigoba pakati kuti ikhale ndi chibowo ndipo amachita zimenezo pogwiritsa ntchito tchizulo. Ntchito yonseyi imatenga pafupifupi maola 80. Kenako amatikita mkati mwa chibowocho kuti mukhale mosalala. Akatero, amalumikiza mbali ziwirizo n’kuzimata ndi guluu komanso kuzikulunga ndi zingwe zangati chilambe. Amalumikizanso kathabwa kenakake kothandiza kuti chitolirocho chisamayendeyende pochiimba. Kenako amaika kachinthu kothandiza kuti akamauzira mpweya asamavutike. Pomaliza amakongoletsa chitolirocho ndi penti kapena kungojambulapo tizinthu tina n’kuchipaka vanishi.

Ntchito Yake

Kuyambira kale kwambiri, abusa akakhala ku ubusa ankaimba chitolirochi pofuna kudziwitsa mabanja awo kuti ali bwino. Koma nthawi zambiri ankaimba chitolirochi poitana ng’ombe kuti adzazikame mkaka. Alimi a ng’ombe za mkaka a ku Switzerland ankakhulupirira kuti ng’ombe zikamamva chitolirochi chikulira sizivuta kukama mkaka.

Akatsekera ng’ombe zawo m’khola m’nyengo yozizira, abusa ambiri ankatenga zitoliro zawo n’kumakaimba m’tawuni kuti anthu aziwapatsa ndalama. Zimenezi zinkawathandiza kuti azitha kusamalira mabanja awo. Koma nthawi zina ankaimba zitolirozi poitana anthu kuti apite ku nkhondo.

Kaimbidwe Kake

Mukangochiona chitolirochi, mungaganize kuti ndi chosavuta kuimba chifukwa chilibe mabowo, mabatani kapena zingwe zoimbira. Koma poimba chitolirochi ntchito imagona pa kupemerera mpweya woyenerera kuti uzitulutsa nyimbo yomveka bwino.

Chitolirochi chimatulutsa timawu tomveka mosiyanasiyana tokwana 12. Ngakhale kuti pangafunike zida zina kuti nyimbo imveke bwino, anthu aluso amatha kuimba nyimbo zabwino kwambiri pongogwiritsa ntchito chitolirochi basi.

Oimba ena otchuka aimbapo nyimbo zimene poyamba zinaimbidwa pogwiritsa ntchito chitolirochi. Mwachitsanzo, Leopold Mozart, omwe anali bambo ake a Wolfgang Amadeus Mozart, analemba nyimbo yawo yakuti “Sinfonia Pastorella” ndiponso yakuti corno pastoritio ndipo nyimbo imeneyi imamveka ngati inaimbidwa ndi chitolirochi. Munthu winanso, dzina lake Brahms, anaimba nyimbo pogwiritsa ntchito zitoliro, yomwe mamvekedwe ake anali ngati a chitolirochi. Ndiponso woimba wina wotchuka, dzina lake Beethoven, anaimba nyimbo yakuti Pastoral. Pofuna kuti nyimbo yake imveke ngati nyimbo zimene abusa ankaimba, iye anagwiritsa ntchito zida zotulutsa mawu ofanana ndi a chitolirochi.

Chitoliro chimenechi chinatchulidwa koyamba ku Switzerland m’chaka cha 1527, m’buku lofotokoza zachuma lomwe linali la kunyumba yokhala ansembe ya St. Urban. Tsopano papita zaka pafupifupi 500, koma nyimbo za chitolirochi zimamvekabe m’malo odyetsera ziweto kumapiri a Alps ku Switzerland.

[Chithunzi patsamba 15]

Munthu amatha kugulula chitolirochi n’kuchinyamula m’manja