Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kaya Ndinaneneranji Zimene Zija?

Kaya Ndinaneneranji Zimene Zija?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kaya Ndinaneneranji Zimene Zija?

Nkhaniyi ikuthandizani kudziwa

CHIFUKWA chimene mumalankhulira zokhumudwitsa ena

ZIMENE mungachite mukalankhula zokhumudwitsa ena

MMENE mungapewere kulankhula zokhumudwitsa ena

“Ndimayesetsa kwambiri kuti ndisalankhule zokhumudwitsa ena, koma nthawi zina ndimapezeka kuti ndanena zinthu zimene sindimafuna kunena ndipo zikatero ndimachita manyazi.”​—Chase

“Nthawi zina ndimanena zinthu zomwe anthu enanso akuganiza koma zoti n’zosayenera kunena pagulu.”​—Allie

CHIFUKWA CHIMENE MUMALANKHULIRA ZOKHUMUDWITSA ENA

Lemba: “Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2) Kodi mfundo ya palembali ndi yotani? Palibiretu munthu ndi mmodzi yemwe amene angathe kulamulira lilime lake nthawi zonse. Anthu ambiri angavomereze zimene Annette ananena kuti: “Nthawi zambiri zimachitika n’zakuti zimene ndalankhula si zimene ndimaganiza.” *

Zochitikadi: “Mnzanga wina ankafuna kuti ndim’patse zovala zimene ndinkafuna kuzitaya. Mosaganizira, ndinayankha kuti, ‘Sizingakukwane.’ Iye anandifunsa kuti, ‘Wati chiyani? Ukutanthauza kuti ndine duntu?’”—Anatero Corrine.

Kuti mudziwe chifukwa chimene nthawi zina munganenere zinthu zimene simumayembekezera, chitani izi:

● Zindikirani vuto lanu.

․․․․․ Sindimalankhula bwino ndikakwiya

․․․․․ Ndimalankhula ndisanaganizire kaye

․․․․․ Ndimalankhula ndisanamve kaye zimene munthu wina akunena

․․․․․ Zifukwa zina ․․․․․

Chitsanzo: “Ndili ndi vuto lokonda kwambiri nthabwala, ndipo nthawi zina anthu amandimva molakwika.”—Anatero Alexis.

Kodi mumakonda kulankhula zolakwika mukakhala ndi ndani?

․․․․․ Makolo anu

․․․․․ Azibale anu

․․․․․ Anzanu

․․․․․ Anthu ena ․․․․․

Chitsanzo: Mtsikana wina wa zaka 20, dzina lake Christine, ananena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti anthu amene ndimawakonda kwambiri ndi amenenso sindichedwa kuwakhumudwitsa. Ndikuganiza kuti ndimachita zimenezi chifukwa chakuti ndikakhala ndi anthu amenewa ndimamasuka kwambiri.”

ZIMENE MUNGACHITE MUKALANKHULA ZOKHUMUDWITSA ENA

Lemba: “Titsatire zinthu zobweretsa mtendere.” (Aroma 14:19) Njira imodzi yobweretsera mtendere ndi kupepesa.

Zochitikadi: “Mayi anga anamwalira ndili ndi miyezi 10 ndipo sindinakule ndi bambo anga. Ndinaleredwa ndi amayi anga aakulu ndi amuna awo. Tsiku lina, ndili ndi zaka mwina 10 kapena 11, ndinakwiya komanso kukhumudwa kwambiri chifukwa choganizira kwambiri za imfa ya amayi anga ndipo ndinkangofuna kuphwetsera mkwiyo wangawo pa wina wake. Ndiye pamene mayi anga aakuluwo anandiuza kuti ndigwire ntchito inayake, ndinangoyamba kulankhula mokalipa kenako ndinangopezeka ndanena kuti ‘Mumandinyansa’ komanso ‘Sindinu mayi anga.’ Mayi angawo anadabwa kwambiri moti anasowa chonena. Anangochoka, kukalowa kuchipinda kwawo n’kutseka chitseko n’kuyamba kulira. Ndinaona kuti ndalakwitsa kwambiri chifukwa iwo ndi amene ankandisamalira komanso kundichitira chilichonse. Amuna awo atamva za nkhaniyi, anandifunsa zimene zinachitika ndipo anandiwerengera malemba ofotokoza za kulamulira lilime. Kenako, ndinawapepesa mayi angawo mochokera pansi pa mtima.”—Anatero Karen.

Lembani m’munsimu chinthu chimene chingakulepheretseni kupepesa.

․․․․․

Kodi kupepesa kungakuthandizeni bwanji?

․․․․․

Zokuthandizani: Ganizirani mfundo zimene zili pa Miyambo 11:2 ndi pa Mateyu 5:23, 24.

Ndipotu, ndi bwino kupewa kulankhula zinthu zina mwachisawawa n’kudzapepesa pambuyo pake. Kodi mungapewe bwanji zoterezi?

MMENE MUNGAPEWERE KULANKHULA ZOKHUMUDWITSA ENA

Lemba: “Aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobo 1:19) Onani mfundo zotsatirazi zimene zingakuthandizeni kutsatira malangizo a palembali:

Werengani malemba otsatirawa ndipo kenako gwirizanitsani lemba lililonse ndi mfundo zimene zili kumanjaku.

Miyambo 12:16

Miyambo 17:14

Miyambo 26:20

Mlaliki 7:9

Afilipi 2:3

1 “Kuti mupewe kumangokhumudwa ndi zilizonse, ndi bwino kuti musamadzione kuti ndinu ofunika kwambiri.”—Anatero Danette.

2 “Ndikakhumudwa, ndimangochokapo kaye n’kukapondaponda. Zimenezi zimandithandiza kuti mtima ukhale pansi.”—Anatero Brielle.

3 “Ndili mwana ndinkaganiza kuti nthawi zonse munthu akandiputa ndizimubwezera. Koma panopa ndimaona kuti nthawi zina anthu akakuchitira zinazake ndi bwino kungoiwala.”—Anatero Celia.

4 “Munthu akamakulalatira n’kuona kuti iwe sukubwezera, amagwa ulesi chifukwa chakuti sukuyankha. Muzingoleza mtima. Musamakolezere moto.”—Anatero Kerrin.

5 “Nthawi zina anthu akandikhumudwitsa ndimafuna nditangowamasula basi. Koma kenako ndikaganizira mwakuya, ndimaona kuti zimene ndikanawalankhula sizikanathandiza. Panopa ndazindikira kuti sibwino kuchita zinthu mwaphuma.”—Anatero Charles.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mayina ena tawasintha m’nkhaniyi.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 22]

Allie—Ndisanalankhule chilichonse, ndimayamba ndadzifunsa kaye kuti, ‘Kodi zimene ndikufuna kunenazi n’zothandiza? Nanga zikhudza bwanji winayo?’ Ngati mukukayikira ndi bwino kungokhala chete.

Chase—Ndisananene chinachake ndimaganizira kaye mmene anthu ena ziwakhudzire. Ndikuona kuti pamene ndikukula ndikuyesetsa kulamulira lilime langa. Ndaona kuti munthu ukamakula umaphunzira zambiri.

[Bokosi patsamba 23]

FUNSANI MAKOLO ANU

Mogwirizana ndi zimene Yakobo ananena, palibe amene salakwitsa ndipo “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” Funsani makolo anu zimene ankakumana nazo poyesetsa kulamulira lilime lawo.—Yakobo 3:2.

[Chithunzi patsamba 22]

“Mankhwala otsukira m’mano akangotuluka m’chubu chake zimavuta kuwabwezeretsa. N’chimodzimodzinso ndi zimene timalankhula. Tikalankhula zinthu zolakwika n’zosatheka kuzibweza.”—Anatero James.