Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Asakubereni pa Intaneti?

Kodi Mungatani Kuti Asakubereni pa Intaneti?

Kodi Mungatani Kuti Asakubereni pa Intaneti?

Bambo wina wa ku Florida, dzina lake William, analandira imelo yomwe ankaganiza kuti yachokera kukampani ya Intaneti. Imeloyo inali yomudziwitsa kuti fomu yake yokhudza ndalama zimene amalipira kukampaniyo yasowa. William anadzaza fomu ina n’kutumiza. Iye sanadziwe kuti akutumizira fomuyo munthu wakuba, dzina lake Shiva, yemwe amakhala mumzinda wa Queens, ku New York. Tsiku lotsatira, Shiva anagwiritsa ntchito zimene William analemba pa fomu ija kugulira pulinta pa Intaneti. Shiva anatumiza maimelo oterewa kwa anthu 100,000. Amene ankafufuza za nkhaniyi ananena kuti pafupifupi anthu 100 anayankha imeloyo n’kuberedwa.

Mayi wina wa zaka 56 wa ku Queensland, ku Australia, anayamba chibwenzi pa Intaneti ndi munthu wina poganiza kuti ndi wa ku Britain. Mayiyo anatumizira munthuyo ndalama zokwana madola 47,000. Koma kenako anadzatulukira kuti munthuyo ndi mnyamata wazaka 27 wa ku Nigeria ndipo ndi wakuba. *

ANTHU ambiri akuberedwa pa Intaneti. Lipoti lina la m’chaka cha 2010 lonena za Intaneti ku United States linati: “Chiwerengero cha anthu amene akuberedwa pa Intaneti chikuchuluka kwambiri moti ndalama zambiri zikupita. Komanso kuyambira chaka chatha, anthu 40 pa 100 alionse ku United States anatumiziridwa mapulogalamu owononga makompyuta ndipo ena anatumiziridwa mapulogalamu oterewa maulendo angapo.” Kodi inuyo mungapewe bwanji mavuto amenewa? Choyamba mufunika kudziwa njira zina zimene akubawa amagwiritsa ntchito.

Amaba Bwanji?

Anthu ambiri akafuna kuba pa Intaneti amagwiritsa ntchito imelo ngati imene William analandira. Imeloyo imafuna kuti munthu alembe nambala yake yachinsinsi yolowera pa kompyuta kapena zinthu zachinsinsi zokhudza akaunti yake ya kubanki, n’kutumiza ku adiresi yooneka ngati yabwinobwino koma ili yabodza. Nthawi zina anthu akuba amatha kugwiritsa ntchito pulogalamu yachinyengo yobera maadiresi a maimelo a anthu.

Pali maimelo ena amene sachita kulira kuti munthu alembe chilichonse. Kungotsegula imelo kokhako kumalowetsa pulogalamu yachinyengo m’kompyuta. Pulogalamu imeneyi imasunga zonse zimene mukuchita pa kompyuta yanu ndipo zimenezi zimathandiza mbava kuti zidziwe nambala yanu yachinsinsi yolowera pa kompyuta. Mapulogalamu ena amakupititsani ku adiresi ya anthu akuba. Ndiye kodi mungatani kuti musaberedwe?

Zimene Mungachite

Muzisamala ndi maimelo amene ali ndi zinthu zokaikitsa. Nthawi zina, anthu akhoza kulowetsa pulogalamu yowononga kompyuta yanu (Trojan horse) imene ingachititse kuti athe kupeza zinthu zanu zachinsinsi. Nthawi zinanso anthu akuba amatha kudziwa zinsinsi za anthu pogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, malo amene kumapezeka zinthu zolaula komanso malo amene amakhala ndi mapulogalamu osiyanasiyana a mu kompyuta. Komanso, musamayankhe maimelo amene amakulonjezani kupeza zinthu zabwino kwambiri koma zovuta kuzikhulupirira.

Mwina munalandirapo uthenga pa Intaneti wonena kuti “Kompyuta yanu ikhoza kuwonongeka. Tsegulani apa kuti muiteteze.” (Your computer is at risk! Click here to protect your computer!) kapena wakuti, “Zithunzi Zaulere Zoika pa Kompyuta. Tsegulani Apa.” (Free Screensavers. Click Here.) Muzipewa kutsegula mauthenga oterowo chifukwa amatha kukhala ndi pulogalamu imene ingasokoneze kompyuta yanu.

Ngati mukufufuza ntchito pa Intaneti, muyeneranso kusamala. Anthu akuba amatha kutsegula malo a pa Intaneti kuti anthu azitumizako ndalama zolipirira sukulu kapena azilembapo zinthu zawo zachinsinsi zokhudza ndalama.

Masiku ano, ngakhale akuba ali kutali, akutha kusokoneza makompyuta a makampani kapena a mabanki n’kuba ndalama. Mwachitsanzo mu January, 2007, akuba ku United States anasokoneza makompyuta a sitolo inayake yaikulu, n’kuba zinthu zambiri zachinsinsi zokhudza makasitomala a sitoloyo. Ku Nigeria, zigawenga zinasokoneza makompyuta a mabanki angapo n’kuba manambala a chinsinsi a anthu oposa 1.5 miliyoni. Iwo ankafuna kugwiritsa ntchito manambalawo kuti abe ndalama za anthuwo. Ndipotu panopa anthu ena ayamba bizinezi yotentha yobera anthu. Anthu ogwira ntchito m’mabanki akumaba manambala achinsinsi a anthu n’kukawagulitsa kwa anthu obera anzawo pa Intaneti ndipo iwo akugwiritsa ntchito manambala amenewa pobera anthu ndalama zawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Magazini ya Galamukani! yakhala ikuchenjeza za kuopsa kopeza chibwenzi pa Intaneti. Mwachitsanzo onani Galamukani! ya May 8, 2005, tsamba 24 mpaka 26, ndi ya June 8, 2005, tsamba 28 mpaka 30.

[Bokosi patsamba 11]

Imelo yachinyengo: Imelo imene imafuna kuti munthu atumize nambala yake yachinsinsi yolowera pa kompyuta kapena zinthu zake zachinsinsi zokhudza akaunti yake ya kubanki ku adiresi yabodza

Pulogalamu yachinyengo: Pulogalamu imeneyi imasunga zonse zimene mukuchita pa Intaneti

Vailasi (Trojan horse): Pulogalamu imeneyi ikalowa m’kompyuta imaoneka ngati ikugwira ntchito yabwino koma ikusokoneza zinthu zonse zoteteza kompyuta yanu

[Bokosi/Zithunzi patsamba 12, 13]

Chenjerani!

KUTI ASAKUBERENI PA INTANETI, YESANI IZI:

1 Muzionetsetsa kuti mapulogalamu onse oteteza kompyuta yanu akugwira ntchito.

2 Muzionetsetsa kuti pakapita nthawi mwasunga mafaelo anu a m’kompyuta pazinthu monga ma CD, n’cholinga choti ngati kompyuta yanu itawonongeka kapena mafaelowo atasowa mukompyutayo, mukhale nawobe.

3 Muziganiza kaye musanachite zinthu. Musamangokhulupirira zilizonse zimene mukuuzidwa kuchita pa Intaneti. Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”

4 Pewani mtima wofuna kukhala ndi zinthu zambiri. (Luka 12:15) Musamakopeke ndi zinthu zaulere kapena zotchipa zimene zimatsatsidwa pa Intaneti. Ikhoza kukhala njira yofuna kukuberani.

5 Muzipewa kutsegula maimelo kapena mauthenga amene amangobwera mwadzidzidzi, makamaka ngati akufuna kuti mulembe n’kutumiza zinthu zanu zachinsinsi.—Miyambo 11:15.

6 Nambala yanu yachinsinsi yolowera mu kompyuta izikhala yoti anthu ena sangaitulukire mwachisawawa. Pakapita nthawi muzisintha nambalayo ndipo musamaigwiritse ntchito pazinthu zina zachinsinsi.

7 Musamangotumiza ku adiresi iliyonse zinthu zanu zachinsinsi zokhudza akaunti yanu ya ku banki.

8 Mukamatumiza zinthu zanu zachinsinsi ku adiresi ina, mwachitsanzo ku adiresi ya kubanki, muzionetsetsa ku mwalemba adiresi yolondola, chifukwa kungolakwitsa pang’ono, zimene mwalembazo zikhoza kupita kwa anthu achinyengo.

9 Mukamatumiza zinthu zanu zachinsinsi, muzionetsetsa kuti anthu ena asatulukire zinthu zanuzo ndipo muzikumbukira kutseka chilichonse patsamba limene munatsegulalo musanatuluke.

10 Mukalandira chikalata chokuuzani mmene mwagwiritsira ntchito ndalama zanu, muzichiwerenga bwinobwino. Mukangoona kuti palembedwa ndalama zina zimene zinachotsedwa mosadziwika bwino, muzipita kukampani kapena kubankiyo kukawafunsa.

11 Muzisamala mukamagwiritsa ntchito Intaneti imene sifuna kuti mulowetse nambala yachinsinsi (Wi-Fi) chifukwa mbava zikhoza kukuberani mosavuta zinthu zanu zachinsinsi kapena kukupititsani ku adiresi ya anthu achinyengo.

12 Muziyankha kuti ayi pakabwera uthenga wokufunsani kuti “Kodi mukufuna kuti kompyuta izikumbukira nambala yanu yachinsinsi?” (Remember this password?) Anthu obera anzawo pa Intaneti akhoza kuba nambala yanu yachinsinsi ngati mutalola kuti kompyuta yanu izikumbukira nambalayo.