Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kuyamba Kuvomereza Khalidwe Logonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Kodi Tiyenera Kuyamba Kuvomereza Khalidwe Logonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Tiyenera Kuyamba Kuvomereza Khalidwe Logonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

MAYIKO ambiri ayamba kuvomereza khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha. Gulu lina la m’chipembedzo china cha ku United States likufuna kuti lamulo la m’Baibulo, loletsa kugonana amuna kapena akazi okhaokha, liunikidwenso kuti lizigwirizana ndi “mmene anthu akuonera zinthu masiku ano.” M’busa wina wa ku Brazil yemwe posachedwapa anakwatirana ndi mwamuna mnzake, ananenanso kuti “m’pofunika kuonanso bwinobwino zimene Baibulo limanena.” Iye ananena zimenezi pofuna kuti Baibulo lizigwirizana ndi mmene anthu a m’tchalitchi chake amaonera zinthu masiku ano.

Anthu amene sagwirizana ndi zoti amuna kapena akazi okhaokha azikwatirana, amaonedwa ngati anthu atsankho kapena odana ndi anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo. Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

Zimene Baibulo Limanena

Baibulo sililimbikitsa tsankho. Komabe, pa nkhani yokhudza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha limanena mosapita m’mbali kuti:

“Usagone ndi mwamuna mmene umagonera ndi mkazi. N’chonyansa chimenechi.”Levitiko 18:22.

Limeneli linali limodzi mwa malamulo a mu Chilamulo cha Mose chimene chinaperekedwa ku mtundu wa Isiraeli. Ngakhale zili choncho, mawu akuti “n’chonyansa chimenechi,” akusonyeza mmene Mulungu ankaonera anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha, kaya akhale Ayuda kapena ayi. Anthu a mitundu ina imene Aisiraeli anayandikana nayo ankagonana amuna kapena akazi okhaokha, ankagonana pachibale, ankachita chigololo ndi makhalidwe ena amene Chilamulo chinkaletsa. Choncho, Mulungu ankaona anthu a mitundu imeneyi kuti ndi odetsedwa. (Levitiko 18:24, 25) Kodi lamulo la Mulungu pa nkhani imeneyi linasintha Chikhristu chitayamba? Taganizirani lemba ili:

“Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zamanyazi za kugonana, popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo n’kumachita zosemphana ndi chibadwa. Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi n’kumatenthetsana okhaokha mwachiwawa m’chilakolako choipa, amuna ndi amuna anzawo, kuchitirana zonyansa.”—Aroma 1:26, 27.

N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndi chinthu chonyansa komanso chosemphana ndi chibadwa? Chifukwa chakuti kugonana kumeneku si kumene Mlengi wathu anafuna kuti anthu azichita. Komanso anthu amene amakwatirana amuna kapena akazi okhaokha sangabereke ana. Baibulo limayerekezera khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha ndi zimene angelo opanduka, omwe panopa amadziwika kuti ziwanda, anachita ndi akazi, Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. (Genesis 6:4; 19:4, 5; Yuda 6, 7) Mulungu amaona kuti zonsezi si zachibadwa.

Kodi Pali Zifukwa Zomveka Zovomerezera Khalidweli?

Ena anganene kuti, ‘Anthu ena amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo ali ndi zifukwa zomveka. Mwachitsanzo, ena amachita zimenezi chifukwa cha mmene anabadwira, mmene anakulira, mwinanso chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo pa moyo wawo, monga kugwiriridwa.’ Koma kodi zimenezi ndi zifukwa zomvekadi? Ayi. Taganizirani chitsanzo ichi: Munthu mwachibadwa angakhale ndi vuto longofuna kumwa mowa kapena angakulire m’banja limene aliyense ankaledzera. Munthu wotereyu atamamwa mowa anthu angamamumvetse. Komabe, zimenezi sizingakhale zifukwa zomveka zomulimbikitsira kuti apitirize kumwa mowa kapena kusiya kulimbana ndi vuto lakelo.

Mofanana ndi zimenezi, Baibulo silidana ndi anthu amene ali ndi vuto lofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo, koma silivomereza ngakhale pang’ono kuti anthuwo azichita zimenezi, kaya ali ndi zifukwa zotani. (Aroma 7:21-25; 1 Akorinto 9:27) Ndipo Baibulo lili ndi mfundo zolimbikitsa komanso zothandiza anthu oterewa kuti athe kulimbana ndi vuto lawolo.

Kodi Mulungu Amawaona Bwanji Anthu Amenewa?

Baibulo limanena kuti Mulungu amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Ngakhale kuti Baibulo limaletsa khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha, silimatilimbikitsa kuti tizidana ndi anthu amenewa.

Sitiyenera kuona mopepuka mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi. Pa lemba la 1 Akorinto 6:9, 10, Baibulo linanena momveka bwino kuti: “amuna ogona amuna anzawo,” ali m’gulu la anthu amene “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” Koma pavesi 11 pali mfundo yolimbikitsa yakuti: “Ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa, mwayesedwa olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.”

Apa n’zoonekeratu kuti anthu onse amene ankafunitsitsa kutsatira malamulo a Mulungu ankalandiridwa mumpingo wachikhristu oyambirira. N’chimodzimodzinso masiku ano. Anthu amene akufunitsitsa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu amafunika kusintha zochita zawo, m’malo mosintha malamulo a Mulungu kuti azigwirizana ndi zochita zawo.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha?—Aroma 1:26, 27.

● Kodi Baibulo limatilimbikitsa kuti tizidana ndi anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha?—1 Timoteyo 2:4.

● Kodi n’zotheka kusiya khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha?—1 Akorinto 6:9-11.

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi anthu ayenera kusintha malamulo a Mulungu pa nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha?