Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kukhala Bwenzi la Mulungu Ngakhale Utakalamba

N’zotheka Kukhala Bwenzi la Mulungu Ngakhale Utakalamba

N’zotheka Kukhala Bwenzi la Mulungu Ngakhale Utakalamba

Yosimbidwa ndi Olavi J. Mattila

“Kodi munayamba mwaganizirapo ngati zili zotheka kudziwa zolondola pa nkhani ya Mlengi?” Munthu wina wa Mboni za Yehova anandifunsa funso limeneli ndipo linandichititsa kuganiza kwambiri. Pa nthawi imeneyi n’kuti ndili ndi zaka zoposa 80. Ndinali nditadziwana ndi anthu ambiri otchuka, kuphatikizapo atsogoleri a ndale. Komabe ndinkayikira ngati n’zotheka kudziwa Mulungu komanso kukhala naye pa ubwenzi.

NDINABADWA mu October 1918, ku Hyvinkää m’dziko la Finland. Ndili wamng’ono ndinayamba kugwira ntchito zosiyanasiyana ku famu yathu. Banja lathu linkaweta ng’ombe, mahatchi, nkhuku ndi atsekwe. Ndinaphunzira kugwira ntchito mwakhama ndipo ndinkakonda kwambiri ntchito yanga.

Makolo anga ankandiuza kuti ndizilimbikira sukulu, choncho nditakula ndinayamba maphunziro a ku koleji. Ndili ku kolejiko ndinkakondanso kuchita nawo mpikisano wothamanga ndipo ndinadziwana ndi Urho Kekkonen, yemwe anali tcheyamani wa bungwe lina la zamasewera ku Finland. (Finnish Athletic Association) Koma pa nthawiyi sindinkaganizira n’komwe kuti Kekkonen adzakhala nduna yaikulu ya ku Finland ndipo kenako n’kukhala pulezidenti wa dzikolo kwa zaka pafupifupi 30. Komanso sindinkadziwa kuti ndidzaphunzira zinthu zambiri kwa munthu ameneyu.

Ndinali Munthu Wodziwika pa Ndale

M’chaka cha 1939, panabuka nkhondo pakati pa dziko la Finland ndi la Soviet Union. M’mwezi wa November chaka chomwecho ndinalowa usilikali. Poyamba ndinapatsidwa ntchito yophunzitsa gulu lina la asilikali kenako ndinakhala mkulu wa gulu la asilikali ogwiritsa ntchito mfuti zoopsa kwambiri. Nkhondoyi inkachitikira m’chigawo cha Karelia chomwe chili kumalire kwa dziko la Finland ndi la Soviet Union. M’chaka cha 1941, ndikumenya nawo nkhondo kufupi ndi tawuni ya Vyborg, ndinavulala ndi bomba limene linaphulika, ndipo ananditengera kuchipatala cha asilikali. Chifukwa chakuti ndinavulala kwambiri, ndinauzidwa kuti sindikuyeneranso kumenya nkhondo.

Mu September 1944, ndinasiya usilikali ndipo ndinabwereranso ku koleji kukapitiriza sukulu. Ndinapitirizanso kuchita nawo mipikisano yothamanga moti ndinawina mipikisano imeneyi katatu. Ndinapezanso digiri ya maphunziro a luso la zopangapanga ndi digiri ya maphunziro a zachuma.

Panthawiyi, Urho Kekkonen anatchuka kwambiri pa ndale ku Finland. M’chaka cha 1952, ali nduna yaikulu, anandipempha kuti ndikakhale kazembe wa dziko lathu ku China. Ndili kumeneko, ndinadziwana ndi akuluakulu angapo a boma kuphatikizapo pulezidenti wa dzikolo, Mao Tse-tung. Koma munthu wofunika kwambiri amene ndinakumana naye ndili ku China anali mtsikana wina, dzina lake Annikki, yemwe ankagwira ntchito mu ofesi ya unduna woona za ubale wa dziko la Finland ndi mayiko ena. Tinakwatirana mu November chaka cha 1956.

Chaka chotsatira ananditumiza ku Argentina kukakhala kazembe wa dziko la Finland. Tili kumeneko, mkazi wanga anabereka ana awiri aamuna. M’chaka cha 1960, tinabwerera ku Finland. Pasanapite nthawi mwana wathu wachitatu anabadwa ndipo anali wamkazi.

Ndinapatsidwa Maudindo m’Boma

Ngakhale kuti ndinali ndisanakhalepo m’chipani chilichonse, mu November 1963, pulezidenti Kekkonen anandisankha kuti ndikhale nduna yoona zamalonda. M’zaka 12 zotsatira, ndinakhala nduna maulendo 6, ndipo kawiri konse ndinakhala nduna yoona za ubale wa dziko lathu ndi mayiko ena. Nthawi imeneyi ndinkakhulupirira kuti anthu angakwanitse kuthetsa mavuto amene ali padzikoli. Koma kenako ndinadzazindikira kuti anthu amangofuna maudindo basi m’malo mothandiza anthu. Ndinaonanso kuti anthu amakonda kukayikirana komanso kuchitirana nsanje.—Mlaliki 8:9.

Komabe ndinaonanso kuti pali atsogoleri ambiri amene amayesetsa kuchita zinthu zabwino ngakhale kuti amalephera kuzikwaniritsa.

M’chaka cha 1975, atsogoleri a mayiko okwana 35 anakumana ku Helsinki, ku msonkhano wokambirana za chitetezo ndi mgwirizano wa mayiko a ku Ulaya. Pa nthawi imeneyo n’kuti ndili nduna yoona za ubale wa dziko lathu ndi mayiko ena komanso ndinali mlangizi wa pulezidenti Kekkonen. Ndinapatsidwa ntchito yokonza zonse zokhudza msonkhanowo ndipo ndinadziwana ndi atsogoleri onse obwera ku msonkhanowu.

Pa masiku ochepa amene msonkhanowu unachitika, ndinaona kuti ntchito yanga inali yovuta kwambiri. Zinali zovuta ngakhale kungowauza atsogoleriwo malo oti akhale. Komabe, ndinaona kuti msonkhanowo komanso misonkhano ing’onoing’ono imene inachitika pambuyo pake, inalimbikitsa ufulu wa anthu komanso inathandiza kuti mayiko amphamvu kwambiri azigwirizana.

Kuzindikira Zosowa Zanga Zauzimu

M’chaka cha 1983 ndinasiya ntchito ndipo ndinasamukira ku France, kumene mwana wanga wamkazi ankakhala. Ndili kumeneko ndinakumana ndi mavuto aakulu. Mu November 1994, mkazi wanga Annikki anapezeka ndi khansa ya m’mawere. M’chaka chomwecho ndinapezekanso ndi mlandu wakatangale. M’mbuyo monsemu ndinkayesetsa kuti ndikhale ndi mbiri yabwino koma pa nthawi imeneyi ndinapezeka kuti mbiri yanga yonse yaipa chifukwa chochita zinthu mosaganiza bwino.

Ndakhala ndikukumana ndi anthu a Mboni za Yehova moyo wanga wonse ndipo ndinkawayamikira chifukwa chocheza nane moti ndinkalandira magazini awo. Komabe ndinkatanganidwa kwambiri moti ndinalibe nthawi yokambirana nawo zinthu zauzimu. Pofika m’chaka cha 2000 ndinali ndikusamalirabe mkazi wanga Annikki. Mu September 2002, munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwanga ndipo anandifunsa funso limene lili kumayambiriro kwa nkhani ino. Ndinadzifunsa kuti, ‘Koma kodi n’zothekadi kudziwa zolondola pa nkhani ya Mulungu komanso kukhala bwenzi lake?’ Ndinali nditasiya kalekale kuwerenga Baibulo koma ndinakafufuza pamene ndinalisiya, n’kuyamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova.

Mu June 2004, mkazi wanga anamwalira ndipo ndinatsala ndekha. N’zoona kuti ana anga ankanditonthoza, komabe ndinali ndi mafunso ambiri okhudza zimene zimachitika munthu akamwalira. Ndinayesa kufunsa ansembe awiri a tchalitchi cha Lutheran koma ankangondiyankha kuti, “Mafunso amenewatu ndi ovuta.” Zimene ankandiyankha sizinkandigwira mtima. Ndinazindikira kuti ndili ndi zosowa zauzimu.

Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo pang’onopang’ono ndinayamba kudziwa zinthu zolondola. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti Baibulo limanena kuti munthu akafa sadziwa chilichonse, amakhala ngati ali mtulo ndiponso kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi. (Yohane 11:25) Zimenezi zinandilimbikitsa komanso kundipatsa chiyembekezo.

Pasanapite nthawi ndinamaliza kuwerenga Baibulo lonse. Lemba lina limene linandigwira mtima kwambiri ndi la Mika 6:8 limene limati: “Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” Lembali linandikhudza kwambiri chifukwa cha malangizo ake anzeru komanso osavuta kumva. Linandithandizanso kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi komanso wachilungamo.

Ndikuyembekezera Zinthu Zabwino

Pamene ndinapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Mulungu, ndinayamba kumukhulupirira kwambiri komanso kumudalira. Ubwenzi wanga ndi Mlengiyu unayamba kukula. Ndinachita chidwi ndi mawu ake opezeka pa Yesaya 55:11 amene amati: “Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga. Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi zimene ine ndikufuna ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.” Mulungu wakhala akukwaniritsa malonjezo ake ndipo apitirizabe kukwaniritsa malonjezo ake m’tsogolo muno. Iye adzakwaniritsa zimene maboma a anthu alephera kukwaniritsa. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 46:9 limasonyeza kuti Mulungu adzathetsa nkhondo. Lembali limati: “Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”

Kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova kwandithandiza kwambiri. Pa misonkhano imeneyi ndimaona chikondi chenicheni chachikhristu, chomwe ndi chizindikiro chodziwira otsatira a Yesu. (Yohane 13:35) Chikondi chimenechi chimachititsa kuti anthu asamasankhane chifukwa chosiyana mayiko. Ndipo chikondi chimenechi n’chosowa kwambiri m’dziko limene anthu amangokonda zandale ndi zamalonda basi.

Mwayi Wamtengo Wapatali

Panopa ndili ndi zaka zoposa 90, ndipo ndimaona kuti mwayi waukulu umene ndakhala nawo ndi kukhala wa Mboni za Yehova. Ndilibenso njala yauzimu chifukwa ndadziwa cholinga cha moyo komanso ndadziwa zinthu zolondola pa nkhani ya Mulungu.

Ngakhale ndine wokalamba, ndimasangalala kuti ndimakwanitsa kugwira nawo ntchito yolalikira komanso kupezeka pamisonkhano. Ngakhale kuti pa moyo wanga ndakumana ndi anthu ambiri otchuka komanso ndakhalapo ndi maudindo akuluakulu, ndikuona kuti zimenezi sizingafanane ndi mwayi wodziwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, ndiponso mwayi wokhala bwenzi lake. Ndimathokoza komanso kutamanda kwambiri Mulungu chifukwa chondipatsa mwayi wokhala ‘wantchito mnzake.’ (1 Akorinto 3:9) Ndaona kuti ngakhale utakalamba, n’zotheka kukhala bwenzi la Mlengi wathu, Yehova Mulungu.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi pulezidenti Kekkonen ndi pulezidenti Ford wa ku America pa msonkhano wa ku Helsinki m’chaka cha 1975

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi pulezidenti Kekkonen komanso Brezhnev yemwe anali mtsogoleri wa dziko la Soviet

[Chithunzi patsamba 26]

Ndikugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Lower left: Ensio Ilmonen/Lehtikuva; lower right: Esa Pyysalo/Lehtikuva