Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Pa kafukufuku wina amene anachitika ku Germany, anthu 76 pa 100 alionse achikulire ananena kuti kukopana “kulibe vuto ngakhale pang’ono,” ndiponso ananena kuti “kukopana sikutanthauza kuti anthuwo ali ndi maganizo ofuna kuchita zachiwerewere.” Pafupifupi hafu ya anthu onse amene anafunsidwa ananena kuti palibe cholakwika ngati munthu wapabanja akukopana ndi munthu wina.—APOTHEKEN UMSCHAU, GERMANY.
Pakafukufuku wina amene anachitika m’dziko lonse la Russia, anapeza kuti anthu 48 pa 100 alionse m’dzikolo amaona kuti uchigawenga wafika “pongozolowereka” ndipo ndi “zochitika za tsiku ndi tsiku.”—KOMMERSANT, RUSSIA.
Anthu ozembetsa mankhwala osokoneza bongo m’dziko la Mexico chaposachedwapa apeza njira ina yotulutsira mankhwala m’dzikolo mozembera boma. Njirayi ndi “yofanana ndi zimene kalelo asilikali ankachita akafuna kulanda mzinda.” Anthuwa akumatenga mankhwala n’kuwaika pa “chilegeni chachikulu” chimene amachimangirira kungolo yokhala ndi lamba wamphamvu wotamuka kwambiri. Akatero akumakoka chilegenicho kuti adumphitse mankhwalawo mpanda wamalire a dziko la United States ndi Mexico.—REUTERS NEWS SERVICE, U.S.A.
“Akazi awiri pa asanu alionse oyembekezera” ku New York City amachotsa mimba. Akuti chiwerengerochi si chachilendo kwenikweni chifukwa “zimenezi zakhala zikuchitika kuyambira zaka 10 zapitazo.”—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.
Anthu opha tizilombo a mumzinda wa London anadabwa kwambiri ataitanidwa kuti akagwire nkhandwe imene inali m’nyumba ina yosanja yosamaliza, m’chipinda cha nambala 72 kuchokera pansi. Kuti ikhalebe ndi moyo, nkhandweyo “inkadya zinyenyeswa za zakudya zomwe anthu omanga nyumbayo ankasiya.” Nkhandweyo inachokera m’dera lapafupi ndi nyumbayo.—THE TELEGRAPH, LONDON.
Ansembe a Tchalitchi cha Orthodox Ali ndi Ufulu Woima pa Chisankho
Bungwe lina lofalitsa nkhani ku Russia linati: “Bungwe la ma Bishopu a tchalitchi cha Orthodox ku Russia lavomereza kuti ansembe a tchalitchichi azilowa ndale, n’kuima nawo pa chisankho zinthu zikavuta.” Bungweli linanena kuti ansembewo ayenera kulowa nawo ndale “n’cholinga choteteza tchalitchicho kwa anthu ofuna kubweretsa chisokonezo.” Malinga ndi chikalata chimene mabishopuwa anatulutsa, ansembe angafunike kuchita zimenezi ngati zikuoneka kuti “anthu ena akufuna kugawanitsa tchalitchicho kapena kugwiritsa ntchito udindo wawo wa ndale kulimbana ndi tchalitchi cha Orthodox.”
Mavuto Atsopano pa Nkhani ya Malamulo
Njira zothandiza kuti anthu osabereka akhale ndi ana, zomwe poyamba zinkaoneka kuti n’zosatheka, zayamba kubweretsanso mavuto. Nyuzipepala ina (The Wall Street Journal) inanena kuti: “Chaka chilichonse, ana ambiri akubadwa pogwiritsa ntchito mluza kapena umuna umene umasungidwa kwa miyezi ingapo kapena zaka zingapo. Nthawi zina mwanayo amabadwa kholo lake limodzi litamwalira kale, ndipo nthawi zambiri kholo lomwaliralo limakhala bambo a mwanayo.” Ku United States, ana ena amasiye amalandira ndalama kuchokera ku boma. Koma malamulo a m’dzikolo amasiyanasiyana pa nkhani imeneyi mogwirizana ndi dera. M’madera ena, amaona kuti mwana amene wabadwa kholo lake limodzi litamwalira sayenera kulandira ndalama zoterezi. Loya wina wa ku Minnesota, dzina lake Sonny Miller, anati: “Masiku ano sayansi yapita patsogolo kwambiri moti n’zovuta kwambiri kugwiritsa ntchito malamulo pa nkhani zina.”