Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Bukuli Ndi Labwino Kwambiri”

“Bukuli Ndi Labwino Kwambiri”

“Bukuli Ndi Labwino Kwambiri”

● Kodi mungakonde kuwerenga zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa komanso mafanizo osaiwalika amene ankawagwiritsira ntchito? Buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako likhoza kukuthandizani.

Munthu wina amene anawerenga bukuli anati: “Bukuli ndi labwino kwambiri chifukwa linalembedwa mosavuta kumva komanso limafotokoza mwatsatanetsatane moyo wa Ambuye ali padziko lapansi.”

Malinga ndi zimene tikudziwa zokhudza Baibulo, nkhani zimene zinalembedwa m’bukuli zinalembedwa motsatira nthawi imene zinachitika. Nkhani za m’bukuli zinatengedwa m’mabuku anayi ouziridwa, amene analembedwa ndi anthu omwe anakhala ndi moyo pa nthawi ya Yesu. Anthuwa anali Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Mateyu ndi Yohane anali atumwi komanso ankayenda ndi Yesu. Maliko anali mnzake kwambiri wa Petulo, yemwe anali mtumwi wa Yesu. Ndipo Luka, yemwe anali dokotala, ankayenda ndi mtumwi Paulo.

Ngati mungafune buku lokhala ndi zithunzi zokongola limeneli, lembani zofunika m’munsimu ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.