Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Gwiritsani Ntchito Maso Anu Mwanzeru

Gwiritsani Ntchito Maso Anu Mwanzeru

Gwiritsani Ntchito Maso Anu Mwanzeru

● Diso la munthu linapangidwa mogometsa ndipo ndi lamphamvu kwambiri. Buku lina lonena za mmene diso linapangidwira linati: “Pafupifupi hafu ya minyewa yonse ya diso, yomwe inalumikizidwa ku ubongo, ndi yochokera kumbali imene imatithandiza kuona.”—Visual Impact, Visual Teaching.

M’pake kuti Yesu Khristu ananena kuti diso ndi “nyale ya thupi.” Pofotokoza tanthauzo la mawu amenewa, iye anati: “Ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi [lopanda chinyengo, ngati limayang’ana zinthu zabwino], thupi lako lonse lidzakhala lowala. Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzachita mdima.” (Mateyu 6:22, 23) Ndi mawu amenewa, Yesu akutithandiza kumvetsa mphamvu imene diso lili nalo. Zimene timaona zimakhudza zimene timaganiza, mmene timamvera komanso zimene timachita. Maganizo abwino amathandiza kuti munthu akhale ndi moyo wabwino pomwe oipa amachititsa kuti zinthu zisamamuyendere bwino.

Mwachitsanzo, ganizirani mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 5:28, 29 omwe amati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Ngati munthu akuyang’anitsitsa mkazi kapena mwamuna mpaka kulakalaka kuchita naye zachiwerewere, pamapeto pake akhoza kuchitadi zimene akulakalakazo. Zimenezi zingachititse kuti asakhalenso pa ubwenzi ndi Mulungu.—Yakobo 1:14, 15.

N’chifukwa chake tifunika kudziletsa, ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta ngati kukolowola diso. Ndiponso kodi ndi nzeru kutaya mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha chifukwa chongofuna kusangalala kwa kanthawi kochepa?

Zimene timaona zingachititsenso kuti tikhale ndi mtima wadyera. N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti ‘chilakolako cha maso . . . sichichokera kwa Atate, koma kudziko. Ndiponso, dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.’—1 Yohane 2:16, 17.

Kodi pamenepa tinganene kuti Baibulo likungokhwimitsa zinthu? Ayi. Ndipo kunyalanyaza malamulo ake n’kudziitanira mavuto ndipo kungachititse kuti munthu azikhala wosasangalala. (Agalatiya 6:7, 8) Koma kutsatira Mawu a Mulungu, omwe akuphatikizapo malangizo okhudza kugwiritsa ntchito diso mwanzeru, kungatithandize kuti tizikhala osangalala. Yesu ananena kuti: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” (Luka 11:28) Anthu amene amatsatira malangizo amenewa ali ndi mwayi wodzakhala padziko lapansi kwamuyaya, pomwe anthu amene amagwiritsa ntchito maso awo poona zinthu zosayenera komanso kuchita zinthu mwadyera sakhala osangalala komanso alibe mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha.