Kodi Kudya Mtedza wa Betel Kuli ndi Mavuto Otani?
Kodi Kudya Mtedza wa Betel Kuli ndi Mavuto Otani?
ANTHU a m’mayiko akum’mwera kwa Asia ndi ansangala. Koma umadabwa kuona kuti anthu ambiri akamamwetulira mano awo ndi othimbirira komanso mkamwa mwawo muli malovu ofiira ngati magazi. Anthuwo amakonda kulavula akamayenda ndipo pamene alavulirapo sungayang’anepo kawiri katatu. Zimenezi zimachitika chifukwa anthu ambiri kumeneko amakonda kudya mtedza winawake wotchedwa Betel.
Anthu omwe amadya mtedza umenewu ndi ochuluka kwambiri, mwina 10 pa 100 alionse. Anthuwa amapezeka m’mayiko monga kum’mawa kwa Africa, Pakistan, Papua New Guinea, Micronesia, India mpaka kukafika kumayiko akum’mwera chakum’mawa kwa Asia. Anthu ambiri amene amagulitsa mtedzawu amayala malonda awo m’misewu kapena m’misika. Ena amakongoletsa malo awo ogulitsira ndi timagetsi tinatake komanso amalemba ntchito atsikana omwe amavala mokopa kuti azigulitsa mtedzawu.
Padziko lonse anthu amapeza ndalama zambiri chifukwa chogulitsa mtedza wa Betel. Kodi mtedza umenewu ndi wotani kwenikweni? Nanga n’chifukwa chiyani anthu ambiri amaukonda? Kodi kudya mtedzawu kumakhudza bwanji thanzi lawo? Kodi anthu amene amadya mtedza umenewu saphwanya mfundo za m’Baibulo? Kodi munthu angatani kuti asiye chizolowezi chodya mtedza umenewu?
Kodi Mtedzawu Ndi Wotani Kwenikweni?
Mtedza umenewu umachokera ku mtengo winawake wotchedwa areca (kapena kuti betel) umene umapezeka m’madera otentha kumayiko a kunyanja ya Pacific ndi akum’mwera chakum’mawa kwa Asia. Anthu amene amakonda kudya mtedzawu amautenga n’kuukulunga m’masamba enaake, kenako amathira timadzi ta chipatso chimene chimakoma ngati mandimu. Chipatsochi chimachititsa kuti mtedzawu uzitulutsa timadzi towawasa. Ena amaika zinthu monga fodya kapena zokometsera zina kuti mtedzawo uzikoma kwambiri.
Zinthu zimenezi zimachititsa kuti munthu akamadya mtedzawu azitulutsa malovu ambiri omwe amakhala ofiira ngati magazi. N’chifukwa chake anthu amene amakonda kudya mtedzawu amalavulalavula, moti nthawi zina ngati amene akulavulayo ali m’galimoto amatha kulavulira anthu oyenda pansi.
Mtedzawu Umayambitsa Mavuto
Bungwe lina linati: “Mtengo umene kumachokera mtedzawu wakhala ukugwiritsidwa ntchito kuyambira kale kwambiri pa zinthu zokhudza chikhalidwe, chipembedzo komanso zikondwerero zina. Anthu ambiri amene amadya mtedzawu amaona ngati ulibe vuto lililonse ndipo amanena kuti amasangalala kwambiri. . . . Koma kafukufuku wasonyeza kuti mtedzawu umayambitsa mavuto ambiri.” (Oral Health) Kodi mavuto ake ndi otani?
Akuluakulu a zaumoyo amakhulupirira kuti zina mwa zinthu zimene zimapezeka mu mtedza umenewu zimachititsa kuti munthu akadya mtedzawu azingofunanso wina, moti ena amatha kudya mtedza wokwana 50 pa tsiku. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene munthu wayamba chizolowezi chodya mtedzawu, mano ake amayamba kuthimbirira ndipo kenako amayamba kudwala chiseyeye. Nthawi zambiri anthu omwe amakonda kudya mtedzawu amakhala ndi zilonda zamkamwa zomwe zimatuluka mafinya. M’kupita kwa nthawi akhozanso kuyamba
kudwala matenda oopsa a khansa ya mkamwa (yotchedwa oral submucous fibrosis).Kudya mtedza umenewu kumayambitsanso khansa yamtundu winanso imene imagwira kummero. Umboni wakuti mtedzawu umayambitsa khansa imeneyi ndi kuchuluka kwa anthu amene ali ndi matenda amenewa m’mayiko akum’mwera chakum’mawa kwa Asia. Mwachitsanzo, m’dziko la Taiwan anthu 85 pa 100 alionse amene ali ndi khansa ya mkamwa inayamba chifukwa chodya mtedza umenewu. Ndipotu lipoti lina linati: “Chiwerengero cha anthu odwala khansa ya mkamwa ku Taiwan chawonjezereka kanayi m’zaka 40 zapitazo. Matenda amenewa ndi amodzi mwa zinthu 10 zimene zimapha anthu ambiri pachilumbachi.”—The China Post.
Vuto lodya mtedzawu lilinso m’mayiko ena. Lipoti lina linati: “Anthu ambiri aku Papua New Guinea amakonda kudya mtedza wa Betel, koma mtedza umenewu ukupha anthu ambiri pafupifupi 2,000 pa chaka, komanso zimenezi zayambitsa matenda osiyanasiyana.” (Papua New Guinea Post-Courier) Dokotala wina yemwenso ndi wolemba mabuku anati: “Mavuto amene amabwera chifukwa chodya mtedza umenewu ndi ambiri ngati amene amabwera chifukwa chosuta fodya.” Ena mwa matenda amenewa ndi matenda a mtima.
Kodi Baibulo Limati Chiyani?
N’zoona kuti Baibulo si buku la zachipatala ndipo silinena nkhani yokhudza kudya mtedza wa Betel. Komabe, lili ndi mfundo zambiri zimene zimatithandiza kudziwa kufunika kokhala anthu aukhondo ndiponso kukhala ndi moyo wabwino komanso wathanzi. Taonani mfundo za m’Baibulo zotsatirazi komanso mafunso amene mungadzifunse.
“Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Kodi anthu amene amaipitsa thupi lawo chifukwa chodya mtedza wa Betel angakhale oyera kwa Mulungu?
“Chifukwa cha [Mulungu] tili ndi moyo.” (Machitidwe 17:28) “Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba.” (Yakobo 1:17) Moyo ndi mphatso yapadera yochokera kwa Mulungu. Kodi munthu amene ali ndi chizolowezi chochita zinthu zimene zingamuyambitsire matenda amasonyeza kuti amayamikira mphatso ya moyo?
“Kapolo sangatumikire ambuye awiri.” (Mateyu 6:24) “Sindidzalola kuti chinthu china chizindilamulira.” (1 Akorinto 6:12) Kodi munthu amene akufuna kukondweretsa Mulungu angalole kuti akhale kapolo wa zinthu zimene zingawononge moyo wake?
“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Maliko 12:31) “Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake.” (Aroma 13:10) Kodi anthu odya mtedza wa Betel anganene kuti amakonda anzawo ngati amalavulira m’misewu zinthu zonyansa monga malovu ofiira?
Mfundo yosatsutsika ndi yakuti, “chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7, 8) Choncho, ngati tili ndi chizolowezi choipa, tidzakololanso zomwezo. Koma ngati timachita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna, zomwe zikuphatikizapo kupewa chizolowezi choipa, tidzakolola zinthu zabwino ndipo tidzakhala osangalala. Ngati mumadya mtedza wa Betel, kodi mungatani kuti musiye n’kuyamba kuchita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo? Zinthu zitatu zotsatirazi zikhoza kukuthandizani.
Zinthu Zitatu Zimene Mungachite Kuti Muthane ndi Vutoli
1. Dziwani chifukwa chachikulu chosiyira khalidweli. Kuti musiye khalidwe linalake loipa mumafunika kudziwa chifukwa chachikulu chosiyira khalidwelo, osati kungodziwa kuti mungawononge thanzi lanu. Ndipotu anthu ambiri amakonda kudya mtedza wa Betel, kusuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ngakhale amadziwa kuti khalidwe lawolo lingawononge moyo wawo. Kuti mudziwe chifukwa chachikulu chosiyira, mungachite bwino kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zambiri zokhudza Mlengi wanu ndi chikondi chimene ali nacho pa inu. Lemba la Aheberi 4:12 limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”
2. Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni. Yesu Khristu ananena kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzam’tsegulira.” (Luka 11:9, 10) Yehova, yemwe ndi Mulungu woona akaona kuti mukupemphera kwa iye komanso kuti mumamudalira kuti akupatseni mphamvu, sangakunyalanyazeni. Lemba la 1 Yohane 4:8 limati: “Mulungu ndiye chikondi.” Munthu mmodzi amene anathandizidwa kwambiri ndi Mulungu anali mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.
3. Muzicheza ndi anthu amene angakuthandizeni. Anthu amene mumacheza nawo akhoza kuwononga khalidwe lanu kapena kukuthandizani kukhala ndi khalidwe labwino. Lemba la Miyambo 13:20 limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Ndiye muzisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Mwachitsanzo, mumpingo wachikhristu wa Mboni za Yehova, muli anthu ambiri amene poyamba ankakonda kudya mtedza wa Betel koma panopa anasiya. Iwo anasiya khalidwe limeneli chifukwa chothandizidwa ndi Akhristu anzawo komanso kuphunzira Baibulo.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 24, 25]
ANASIYA KUDYA MTEDZA WA BETEL
Olemba Galamukani! anafunsa anthu asanu omwe poyamba ankadya mtedza wa Betel. Tamvani zimene iwo ananena.
Munayamba bwanji kudya mtedza umenewu?
Pauline: Makolo anga ndi amene anandiyambitsa kudya mtedzawu ndili kamwana. M’mudzi wathu, womwe uli pachilumba china ku Papua New Guinea, aliyense ankadya mtedza umenewu.
Betty: Bambo anga anayamba kundipatsa mtedzawu ndili ndi zaka ziwiri zokha. Ndili wachinyamata, ndinkakonda kuyenda ndi mtedza wambiri moti zinkangokhala ngati ineyo ndi mtengo wa mtedzawo. Ndinafika pokonda kwambiri mtedzawu moti ndinkangoti kukangocha, chinthu choyamba kuchita chinali kudya mtedza.
Wen-chung: Ndinayamba kudya mtedzawu ndili ndi zaka 16. Nthawi imeneyo munthu wodya mtedzawu ankaoneka kuti ndi wozindikira komanso wanzeru. Ndinayambanso kudya mtedzawu kuti anzanga azindikonda.
Jiao-Lian: Ndinkagulitsa mtedza wa Betel n’cholinga choti ndizipezako ndalama. Kuti zinthu zizindiyendera bwino, ndinkafunika kugulitsa mtedza wabwino kwambiri ndipo kuti ndidziwe kuti ndi wabwino ndinkafunika kuulawa. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe chizolowezi chodya mtedzawu.
Kodi zimenezi zinakhudza bwanji thanzi lanu?
Jiao-Lian: Mkamwa, mano komanso milomo yanga zinathimbirira kwambiri ndipo zinkaoneka zofiira ngati magazi. Ndimachita manyazi ndikaona zithunzi zanga za nthawi imeneyo. Mpaka pano milomo yanga imachitabe zilonda.
Pauline: Nthawi imene ndinkadya mtedza umenewu milomo yanga inkatuluka zilonda, ndinkamva chizungulire komanso ndinkatsegula m’mimba kawirikawiri.
Betty: Pamene ndinkadya mtedzawu ndinkalemera makilogalamu 35 okha ngakhale kuti ndinali munthu wamkulu. Mano anga sankaoneka bwino moti nthawi zambiri ndinkawatsuka komanso kuwapukuta ndi waya.
Sam: Nthawi zambiri ndinkatsegula m’mimba komanso ndinkachita chiseyeye. Panopa ndili ndi dzino limodzi lokha. Ndimaona kuti kutsuka mano anga ndi waya kunandiwonjezera mavuto.
N’chiyani chinakuchititsani kuti musiye kudya mtedzawu?
Pauline: Nditawerenga m’Baibulo pa 2 Akorinto 7:1, ndinapeza mfundo yakuti Mulungu amafuna kuti “tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.” Ndinaganiza zosiya khalidweli kuti ndizikondweretsa Mlengi wanga.
Sam: Ndinkafuna kuti mzimu woyera wa Yehova Mulungu uzigwira ntchito m’moyo wanga. Choncho ndinkapempha Yehova kuti andithandize kusiyiratu kudya mtedza umenewu. Iye anayankha mapemphero anga moti panopa ndatha zaka pafupifupi 30 ndisanadye mtedzawu.
Jiao-Lian: Mmene ndinkawerenga Baibulo, ndinapeza mfundo yakuti, “Yeretsani manja anu ochimwa inu.” (Yakobo 4:8) Mawu amenewa anandikhudza kwambiri. Ndinadzifunsa kuti, kodi ndi bwino kumadya komanso kugulitsa mtedzawu ngakhale ndikudziwa kuti ukhoza kuwononga thanzi langa? Kungoyambira pamenepo ‘ndinayeretsa manja anga’ n’kusiyiratu khalidweli.
Kodi kusiya kudya mtedzawu kwakuthandizani bwanji?
Wen-Chung: Ndinayamba kudya mtedzawu n’cholinga choti ndiyambe kukondedwa ndi anzanga. Koma panopa ndimakondedwa kwambiri ndi Yehova komanso abale ndi alongo anga auzimu.
Sam: Panopa ndili ndi thanzi labwino komanso ndine woyera mwauzimu. Ndipo chifukwa chakuti sindiwononga ndalama zambiri kugulira mtedzawu, ndimakwanitsa kusamalira banja langa.
Pauline: Panopa ndimaona kuti ndinamasuka komanso ndili ndi thanzi la bwino. Mano anga ndi oyera komanso olimba. Pakhomo panga ndi paukhondo chifukwa sipapezekanso makoko amtedza kapena zotsalira za malovu ofiira ngati magazi.
Betty: Ndili ndi chikumbumtima choyera komanso ndili ndi thanzi labwino kuposa kale. Ndipotu ndimagwira ntchito ya uphunzitsi komanso ndimagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino nthawi zonse.
[Zithunzi]
Betty
Pauline
Wen-Chung
Jiao-Lian
Sam
[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kudya mtedza wa Betel kwa nthawi yaitali kungayambitse matenda oopsa osiyanasiyana
Mano othimbirira komanso chiseyeye
Zilonda zakummero zomwe zimatulutsa mafinya
Zilonda zamkamwa zomwe zimatulutsa mafinya
[Chithunzi patsamba 22]
Mtedza wa “Betel” utakulungidwa patsamba la mtengo wa “Betel”