Kodi Ndingatani Kuti Ndizisangalala Ndikamawerenga Baibulo?
Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndingatani Kuti Ndizisangalala Ndikamawerenga Baibulo?
N’chifukwa chiyani muyenera kuwerenga Baibulo? Taganizirani izi:
Baibulo lingakuthandizeni kupeza chinthu chamtengo wapatali. Buku limeneli, lomwe anthu ambiri ali nalo, lingakuthandizeni m’njira zotsatirazi:
● Kukonzekera kudzakhala ndi moyo wabwino m’tsogolo
● Kudziwa zam’tsogolo komanso zinthu zakale zimene simukanatha kuzidziwa
● Kudzidziwa mmene mulili komanso zimene mungachite kuti mukhale munthu wabwino *
KUPHUNZIRA Baibulo kumafuna khama koma n’kothandiza kwambiri. Kodi mukufuna kudziwa zimene achinyamata ena akuchita kuti aziphunzira Baibulo? Dulani tsamba lotsatirali n’kulipinda bwinobwino. Pepala la masamba anayi limeneli likuthandizani kudziwa zimene anzanu akuchita pothana ndi zinthu zimene zimawalepheretsa kuphunzira Baibulo komanso zimene akuchita kuti azipindula akamaphunzira Baibulo paokha.
“M’Baibulo muli mfundo zimene zingathandize munthu aliyense ndipo muli nkhani zambirimbiri moti munthu sangazidziwe zonse.”—Anatero Valerie. *
Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni pa zinthu zimenezi, funsani a Mboni za Yehova a m’dera lanu kapena lemberani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5.
^ ndime 9 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 19, 20]
ZIMENE MUNGACHITE POPHUNZIRA BAIBULO
Vuto: KUSAFUNA KUWERENGA
“Ndimagwa ulesi ndikaganiza zokhala pansi n’kumawerenga Baibulo mwina kwa ola limodzi.”—Anatero Lena.
Zimene mungachite: DZIWANI CHIFUKWA CHOWERENGERA
Kuti muzisangalala ndi kuwerenga Baibulo, muyenera kudzifunsa kuti, Kodi Baibulo lingandithandize bwanji? Dziwani kuti Baibulo lingakuthandizeni pa zinthu zambiri monga kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, kudziwa zinthu zambiri zimene zikuchitika padzikoli komanso chifukwa chimene zikuchitikira. Lingakuthandizeninso kukhala ndi makhalidwe abwino.
“Musamaone kuwerenga Baibulo ngati chintchito kapena ngati mukuwerenga za kusukulu. M’malomwake, muzikuona kuti ndi njira yokuthandizani kukhala pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu, yemwe sangafanane ndi mnzanu wina aliyense.”—Anatero Bethany.
“Nthawi yomwe mukuphunzira Baibulo ndi yofunika kwambiri chifukwa mumakhala ngati mukulankhula ndi Yehova Mulungu. Ngati mumangocheza ndi mnzanu makolo anu akakhalapo, kodi munganene kuti ndi mnzanudi kapena ndi mnzawo wa makolo anu? Mukamawerenga Baibulo panokha, Yehova amakhala mnzanu weniweni.”—Anatero Bianca.
Mfundo yoti muziikumbukira: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16) Baibulo lingakuthandizeni pa zinthu zimenezi.
“Ndikamawerenga Baibulo ndimayesetsa kuganizira phindu limene ndingapeze. Ngati ndili ndi khalidwe linalake limene ndifunika kusintha, ndimaona kuti kuwerenga Baibulo kumandithandiza kudziwa zimene ndingachite kuti ndisinthe.”—Anatero Max.
Zoti muganizire:
Kodi inuyo muli ndi zifukwa ziti zowerengera Baibulo?
Vuto: KUSOWA CHIDWI
“Pakangotha mphindi 10 ndikuwerenga Baibulo ndimatopa, zikamatha mphindi 20 ndimakhala kuti sindikufunanso kuwerenga, zikamatha mphindi 30 chidwi chonse chowerenga chimakhala chitatheratu.”—Anatero Allison.
Zimene mungachite: MUZICHITA ZINTHU ZOSIYANASIYANA
Muzisinthasintha nkhani zowerenga, mmene mumawerengera komanso malo owerengera.
“Pezani nthawi yofufuza mayankho a mafunso amene muli nawo. Mukawerenga nkhani imene mumafunitsitsa mutaidziwa bwino, mumasangalala.”—Anatero Richard.
“Mukawerenga nkhani inayake, muziyerekezera kuti inuyo munalipo pamene zimachitika. Muziyerekezera kuti ndinu mwininkhani kapena munthu wina amene akungoonera zochitikazo. Muziyerekezera kuti zimene mukuwerengazo mukuziona zikuchitikadi.”—Anatero Steven.
“Muzichita zinthu zoti muzisangalala powerenga Baibulo. Mwachitsanzo, mukhoza kutenga mpando wanu kukakhala panja pamalo pa phee n’kumawerenga Baibulo kwinaku mukudya kachakudya kenakake. N’zimene ine ndimachita ndikamawerenga Baibulo.”—Anatero Alexandra.
Mfundo yoti muziikumbukira: Ngati munthu alibe chidwi ndi zinazake, nthawi zambiri vuto limakhala mmene iye akuonera zinthuzo osati mmene zinthuzo zilili. Choncho, m’malo monena kuti “Kuwerenga Baibulo n’kotopetsa,” mwina mungachite bwino kumanena kuti “Ndatopa ndineyo.” Musamanamizire kuti kuwerenga Baibulo n’kotopetsa. Kudziwa mfundo imeneyi kungakuthandizeni kuganiza mofatsa n’kusintha.—Miyambo 2:10, 11.
“Kuwerenga Baibulo sikuyenera kukhala kotopetsa. Kuti kuwerenga Baibulo kuzikhala kosangalatsa zimangodalira mmene inuyo mukuonera zinthu.”—Anatero Vanessa.
Zoti muganizire:
Kodi inuyo mungamasinthe zinthu ziti kuti kuwerenga Baibulo kusamakutopetseni?
Vuto: KUSOWA NTHAWI
“Ndimafunitsitsa nditamawerenga Baibulo, koma chifukwa ndimatanganidwa kwambiri, ndimasowa nthawi yokhala pansi kumaliwerenga.”—Anatero Maria.
Zimene mungachite: DZIWANI ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI
Chinthu china chimene chimasonyeza kuti munthu akukula, ndi kudziwa “kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.
“Mayi anga anandithandiza kuzindikira kuti n’zosatheka kukhala ndi nthawi yapadera. Choncho ndinafunika kupatula nthawi kuti ndiziwerenga Baibulo. Nditayamba kukhala ndi chidwi chowerenga Baibulo ndinayambanso kupatula nthawi yoti ndiziliwerenga.”—Anatero Natanya.
“Mmene ndakulamu ndaona kuti ndi bwino kumapatula nthawi yophunzira Baibulo ndipo ndimayesetsa kuliwerenga nthawi imeneyo ngakhale patakhala zinthu zina zochita.”—Anatero Yolanda.
“Mukayamba kuwerenga Baibulo kenako n’kukachita zinthu zina zosangalatsa, ndikukutsimikizirani kuti mudzasangalala ndi kuwerenga Baibulo komanso simungamadziimbe mlandu kuti mwalephera kuchita zinthu zofunika.”—Anatero Diana.
Mfundo yoti muziikumbukira: Ngati simudziwa kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, mukhoza kumangowononga nthawi pa zinthu zosathandiza. Choncho mungachite bwino kumayesetsa kupatula nthawi kuti muziwerenga Baibulo.—Aefeso 5:15, 16.
“Ndine mwana wa sukulu wa kusekondale, ndipo n’zosavuta kutanganidwa ndi zinthu zina. Komabe ndimayesetsa kuti pa ndandanda yanga ya zinthu zoti ndichite, ndisalephere kuikapo nthawi yophunzira Baibulo.”—Anatero Jordan.
Zoti muganizire:
Kodi inuyo mungatani kuti muzipeza nthawi yowerengera Baibulo?
[Bokosi/Zithunzi patsamba 19]
MFUNDO ZOTHANDIZA ZIMENE ANZANU ANANENA
Zachary—Musamangowerenga zimene makolo anu kapena anzanu akuwerenga. Kuphunzira Baibulo panokha kumatanthauza kuphunzira zimene inuyo mukufunadi kuphunzira.
Kaley—Yambani ndi kuphunzira nthawi yochepa. Mukhoza kumaphunzira Baibulo kwa mphindi zisanu zokha, koma onetsetsani kuti mukuchita zimenezi tsiku lililonse. Kenako mungamawonjezere nthawi yophunzira, mwina mphindi 10 kapena 15 . . ndipo m’kupita kwa nthawi mudzayamba kusangalala ndi kuwerenga Baibulo.
Daniela—Musanayambe kuwerenga Baibulo muzisonkhanitsa zinthu monga zolembera ndi kabuku kolembamo mfundo zanu kapena mungakhale ndi faelo pa kompyuta yolembamo mfundo zimene mwapeza. Zinthu zochepa ngati zimenezi zingakuthandizeni kuti muzisangalala mukamawerenga Baibulo.
Jordan—Ndikasankha kuphunzira nkhani imene imandisangalatsa, ndimawerenga nthawi yaitali. Ndiponso ndimawerenga bwino ndikakhala pamalo opanda phokoso. Sindingathe kuwerenga ngati pomwe ndikuwerengerapo pali phokoso.
[Chithunzi patsamba 18]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Dulani Motsatira Mzere
Pindani