Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amakonda Kuwagwiritsa Ntchito?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amakonda Kuwagwiritsa Ntchito?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amakonda Kuwagwiritsa Ntchito?

PA njira zimene zili m’munsizi, kodi inuyo mwagwiritsa ntchito njira ziti pocheza ndi anthu m’mwezi wapitawu?

Kucheza pamasom’pamaso

Kulemba kalata kapena khadi

Kuimba foni

Kutumiza imelo

Kutumiza uthenga wapafoni

Kucheza pa Intaneti potumizirana mauthenga

Kucheza ndi anthu pa Intaneti koma mukuonana pogwiritsa ntchito kamera ya pa kompyuta

Kucheza pogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti

Masiku ano kuli njira zambiri zolankhulirana ndipo njira iliyonse ili ndi ubwino komanso kuipa kwake. Mwachitsanzo, taonani njira izi:

KUCHEZA PAMASOM’PAMASO

Ubwino wake: Anthu akamalankhulana pamasom’pamaso amatha kuona mmene munthuyo akumvera poyang’ana nkhope yake komanso mmene akulankhulira.

Vuto lake: Anthu olankhulanawo amafunika apeze nthawi yoti akumane.

KULEMBA KALATA KAPENA KHADI

Ubwino wake: Anthu amasangalala akalandira khadi kapena kalata.

Vuto lake: Zimatenga nthawi kulemba kalata komanso kuti munthu winayo ailandire.

IMELO

Ubwino wake: Siitenga nthawi kulemba komanso munthu winayo amailandira mofulumira.

Vuto lake: Siionetsa kwenikweni mmene munthu wolembayo akumvera ndiponso anthu ena akhoza kumva molakwika zimene zalembedwazo.

Njira yolankhulirana yomwe anthu ena akunena kuti ndi yabwino kwambiri ndi yogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. Pa Intaneti pali malo ambiri ochezera koma malo otchuka kwambiri ndi a Facebook, ndipo anthu pafupifupi 800 miliyoni amagwiritsa ntchito malo amenewa. Magazini ya Time inanena kuti: “Zikanakhala kuti Facebook ndi dziko, likanakhala dziko lachitatu pa mayiko amene ali ndi anthu ambiri pa dziko lonse, moti likanangoposedwa ndi dziko la China ndi India basi.” Kodi malo ochezera a pa Intaneti amagwira ntchito bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani anthu ambiri akuwagwiritsa ntchito masiku ano?

Malo ochezera a pa Intaneti ndi malo amene anthu amakambirana nkhani zosiyanasiyana ndi anzawo. Mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Jean, ananena kuti: “Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yochezera ndi anthu ndipo umatha kutumizira anzako zithunzi mosavuta.”

N’chifukwa chiyani anthu samangolemberana makalata? Ena amanena kuti kulemba kalata kumafuna nthawi yambiri ndipo ngati ukufuna kuikanso zithunzi m’kalatamo, umafunika ndalama zambiri kuti ukatsukitse zithunzizo. Nanga n’chifukwa chiyani anthu samangoimbirana mafoni? Foni nayonso imafuna nthawi, makamaka ngati ukufuna kuimbira anthu ambiri, ndipo ena sayankha foni pa nthawi imene ukuwafunayo. Nanga bwanji kutumiza imelo? Mtsikana wina wa zaka 20, dzina lake Danielle, ananena kuti: “Masiku ano, palibe amene amayankha ukamulembera imelo. Ndipo ngati angakuyankhe, pamakhala patadutsa milungu ingapo. Pomwe pamalo ochezera a pa Intaneti ndimangolemba zimene ndikuchita ndipo anzanga amalembanso zimene akuchita ndipo nthawi yomweyo aliyense amadziwa zimene mnzake akuchita.”

Komabe sikuti anthu amangogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti pokambirana nkhani zosafunika zokhazokha. Mwachitsanzo, pamene chivomezi komanso madzi osefukira anawononga madera ena ku Japan pa March 11, 2011, anthu ambiri anagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti kuti adziwe mmene abale awo komanso anzawo alili.

Benjamin amene amakhala ku United States ananena kuti: “Madzi atasefukira mafoni sankagwira. Mnzanga wina anandiuza kuti anatumizira imelo mnzathu wina wa ku Tokyo koma sanayankhe. Nthawi yomweyo, ndinangotenga foni yanga, kutsegula malo a mnzathuyo pa Intaneti. Patangopita kanthawi pang’ono, mnzathuyo analemba pamalo akewo kuti ali bwino ndipo ananena kuti atiuza zambiri nthawi ina.”

Benjamin anapitiriza kuti: “Kuti ndithe kulankhulana ndi anzanga amene ankamudziwa mnzathuyo, koma analibe malo awo ochezera a pa Intaneti, ndinafunika kuwalembera maimelo aliyense payekha. Zinanditengera nthawi kuti ndipeze adiresi ya aliyense. Ambiri anandiyankha patapita masiku angapo ndipo mnzanga wina anandiyankha patapita milungu iwiri. Anthuwo ankalandira maimelo ambiri moti zinali zovuta kuti andiyankhe mwamsanga. Zonsezi sizikanachitika zikanakhala kuti onsewa timalankhulana nawo pamalo ochezera a pa Intaneti chifukwa tikanadziwa mwamsanga mmene alili.”

Zimenezi zikusonyeza kuti malo ochezera a pa Intaneti ali ndi ubwino wake. Koma kodi alinso ndi kuipa kwake? Ngati ndi choncho, ndi oipa bwanji, ndipo tingatani kuti tidziteteze?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]

ZIMENE ZIMACHITIKA

1. Mumalemba uthenga pamalo anu ochezera a pa Intaneti.

2. Aliyense amene munamusankha kuti muzicheza naye amalandira uthenga wanu akangotsegula malo ake ochezera a pa Intaneti ndipo inunso mumalandira uthenga wake mukangotsegula malo anu.