Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
“Kukhala pulezidenti n’kovuta moti nthawi zina umafunika kupemphera.”—BARACK OBAMA, PRESIDENT OF THE UNITED STATES OF AMERICA.
Atafunsidwa kuti anene njira yabwino yosonyezera kuti amakonda dziko lawo, anthu 56 pa 100 alionse ku Argentina azaka zapakati pa 10 ndi 24 ananena kuti angasankhe kuvala yunifomu ya timu ya mpira ya dzikolo.—LA NACIÓN, ARGENTINA.
Kafukufuku wina anasonyeza kuti “padziko lonse pafupifupi 33 peresenti ya zakudya zimene zimapangidwa kuti anthu azidya zimawonongeka kapena kutayidwa. Zakudya zimenezi zimakwana matani 1.3 biliyoni pachaka.”—FOOD AND AGRICULTURE ORGANIZATION OF THE UNITED NATIONS, ITALY.
“Masiku ano, nkhondo komanso nkhani zokhudza nkhondo zili paliponse. Choncho asilikali a dziko lathu ayenera kukhala okonzeka kuteteza anthu ndi zinthu zonse zopatulika kwambiri kuti adani asaziwononge.”—PATRIARCH KIRILL, HEAD OF THE RUSSIAN ORTHODOX CHURCH.
Ngozi zambiri za pamsewu zimene anthu anakanena ku kampani ya inshuwalansi ya ku Germany m’chaka cha 2010 zinachitika pakati pa 7 koloko ndi 8 koloko m’mawa. Mmodzi wa mabwana a pakampaniyi ananena kuti: “Njira imodzi yopewera ngozi ndi kukhala ndi nthawi yokwanira yokonzekera popita kuntchito m’mawa.”—PRESSEPORTAL, GERMANY.
Mpikisano Wokopa Achinyamata ku Malaysia
Ku Malaysia kuli mpikisano wotchuka wa pa TV womwe cholinga chake ndi kusankha m’tsogoleri wabwino wachisilamu. Mpikisanowu umadziwika kuti “Imam Muda,” kutanthauza “M’tsogoleri Wachinyamata.” Mpikisanowu umaulutsidwa ku maofesi a TV omwe ali mumzinda wa Kuala Lumpur. Anthu olowa mpikisanowu amakhala azaka zapakati pa 18 ndi 27 ochokera m’madera osiyanasiyana. Munthu amene wapambana mpikisanowu amatha kulandira mphoto monga ndalama, galimoto yatsopano komanso amalembedwa ntchito ngati mtsogoleri wachinyamata wachisilamu. Amapatsidwanso mwayi wokaphunzira ku Saudi Arabia komanso amamulipilira ndalama za ulendo wopita ku Mecca. Anthu olowa mpikisanowa amafunika kudziwa bwino ntchito za m’tsogoleri wachisilamu, kudziwa bwino nkhani zokhudza chipembedzo ndi nkhani zina zimene zikuchitika padziko, komanso kuloweza mavesi a Koran. Akuti munthu amene anayambitsa mpikisanowu cholinga chake ndi “kukopa achinyamata” kuti alowe Chisilamu.
Kusaganiza Bwino Pogwiritsa Ntchito Intaneti
Anthu ambiri amene amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti sazindikira kuti kuika zinthu zawo zachinsinsi pamalowa kungawabweretsere mavuto m’tsogolo. Malinga ndi zimene mphunzitsi wina, dzina lake Timothy Wright, ananena mu nyuzipepala ya ku Australia yotchedwa Sydney Morning Herald, “Masiku ano, ngati munthu walankhula mosaganiza bwino pa Intaneti, walemba zinthu zonyoza ena, waika chithunzi chosayenera kapena kuulula zinsinsi za munthu wina, zinthu zimenezi zimakhalapobe mpaka kalekale moti munthu aliyense akhoza kumaziona.” Zimenezi zikutanthauza kuti “ngati munthu atalemba kapena kuika zinthu zosayenera pa Intaneti ali ndi zaka 15, ndiyeno patadutsa zaka 10 n’kuyamba ntchito, abwana ake akhoza kuzionabe.”