Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani 1 Samueli 1:24-28; 2:11. Kenako yang’anani chithunzichi. Tchulani zinthu zimene zikusowekapo. Lembani mayankho anu m’munsimu. Malizitsani kujambula chithunzichi polumikiza timadonthoto, ndipo chikongoletseni ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni)

KAMBIRANANI:

Kodi makolo a Samueli ankafuna kuti iye adzachite chiyani pa moyo wake? Kodi Yehova anadalitsa bwanji Samueli?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 3:19-21.

Kodi mungakhale ndi zolinga zotani kuti mulemekeze Yehova?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mlaliki 12:13; 1 Timoteyo 4:6-8, 12, 13.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Popanda kutulutsa mawu, munthu wina m’banja lanu ayerekezere kuti ndi mmodzi wa anthu a mu nkhani ya m’Baibulo ili pamwambayi. Ena nonsenu muone ngati mungathe kudziwa munthu amene akumuyerekezerayo.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 14 SAMUELI

MAFUNSO

A. Makolo a Samueli anali ․․․․․ ndi ․․․․․ .

B. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito Samueli kulemba mabuku a m’Baibulo ati?

C. Malizitsani mawu a m’Baibulo awa: “Mwanayo Samueli anapitiriza . . . ”

[Tchati]

4026  B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

Anakhala ndi moyo cha m’ma 1100 B.C.E.

1 C.E.

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

Anabadwira ku Rama—n’kusamukira ku Silo

Rama

Silo

Yerusalemu

SAMUELI

ANALI NDANI?

Makolo ake ‘anam’pereka kwa Yehova’ ndipo anamulimbikitsa kuti atumikire Yehova kwa moyo wake wonse. (1 Samueli 1:24, 28) Ngakhale kuti Samueli ankaona ansembe achinyengo akubera anthu pa kachisi, iye anapitirizabe kuchita zinthu mokhulupirika, mwachilungamo komanso molimba mtima.—1 Samueli 2:22-26; 3:18, 19; 12:2-5, 17, 18.

MAYANKHO

A. Elikana ndi Hana.—1 Samueli 1:19, 20.

B. Oweruza, Rute ndi mbali ina ya 1 Samueli.

C. “. . . kukula, akukondedwa ndi Yehova.”—1 Samueli 2:21.

Anthu ndi Mayiko

4. Mayina athu ndi Oskar ndi Saskia. Tili ndi zaka 10 ndi 7. Timakhala m’dziko la Estonia. Kodi mukudziwa kuti ku Estonia kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 2,400; 4,200, kapena 6,800?

5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko, ndipo kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi dziko la Estonia.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Kuti musindikize masamba ena a nkhani yakuti “Zoti Banja Likambirane,” pitani pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 11

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Ng’ombe yoperekera nsembe.

2. Ufa.

3. Mtsuko waukulu wa vinyo.

4. 4,200.

5. B.