Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Vuto Lililonse Kukhala Wotchuka?

Kodi Pali Vuto Lililonse Kukhala Wotchuka?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Pali Vuto Lililonse Kukhala Wotchuka?

Malizitsani chiganizochi ndi mawu ali kumanjawa:

Kukhala munthu wotchuka ․․․․․.

A. ndi kwabwino nthawi zonse

B. ndi kwabwino nthawi zina

C. si kwabwino

YANKHO lolondola ndi “B.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti munthu wotchuka amakondedwa ndi anthu ambiri ndipo zimenezi si zolakwika. Baibulo linaneneratu kuti Akhristu adzakhala “kuwala kwa anthu a mitundu ina” ndipo anthu ena adzakopeka nawo. (Yesaya 42:6; Machitidwe 13:47) Chifukwa cha zimenezi, tinganene kuti Akhristu ndi otchuka.

Kodi mukudziwa? Yesu anali wotchuka. Baibulo limati ngakhale pamene anali mwana, “Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.” (Luka 2:52) Limanenanso kuti Yesu atakula, “makamu a anthu ambiri ochokera ku Galileya, ku Dekapole, ku Yerusalemu, ku Yudeya komanso ochokera kutsidya lina la Yorodano, anam’tsatira.”—Mateyu 4:25.

N’chifukwa chiyani kutchuka kumeneku sikunali kolakwika? Chifukwa chakuti Yesu sankachita zinthu n’cholinga choti atchuke basi kapena kufuna kuti azipatsidwa ulemu. Komanso sankachita zinthu kuti akondweretse anthu. Iye ankangochita zinthu zoyenera ndipo zimenezi zinkachititsa kuti anthu azikopeka naye. (Yohane 8:29, 30) Ndipotu Yesu ankadziwa kuti anthu sachedwa kusintha maganizo, akhoza kumukonda lero mawa n’kudana naye. Iye ankadziwanso kuti nthawi ina anthu omwewo adzamupha.—Luka 9:22.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Kutchuka kuli ngati chuma. Kukhala ndi chuma sikolakwika koma vuto ndi zimene anthu ena amachita kuti apeze chumacho. Mofanana ndi zimenezi, kukhala wotchuka nthawi zina si vuto, koma vuto ndi zimene anthu amachita kuti akhale otchuka kapena kuti apitirizebe kukhala wotchuka.

Kuipa kwake Achinyamata ambiri amalolera kuchita chilichonse pofuna kutchuka. Mwachitsanzo, ena amachita chilichonse chimene ena akuwauza pofuna kuti azikondedwa ndi anthu ambiri. Pamene enanso amazunza anzawo n’cholinga choti azipatsidwa ulemu ngakhale kuti owapatsa ulemuwo amachita zinthuzo chifukwa cha mantha. *

M’masamba otsatirawa, tikambirana njira ziwiri zolakwika zimene ena amatsatira pofuna kutchuka. Kenako tiona njira yachitatu yomwe ndi yoyenera.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Baibulo limanena za “amuna otchuka” otchedwa “Anefili” amene ankazunza anzawo. Cholinga chawo chachikulu chinali kufuna kutchuka komanso kuti anthu aziwapatsa ulemu.—Genesis 6:4.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 16, 17]

ZIMENE ENA AMACHITA POFUNA KUTCHUKA

KUTENGERA KHALIDWE LA ENA

Ndikufuna kuti anthu azindikonda.

Kuti zimenezi zitheke, ndiyenera kutengera khalidwe lawo.

“Ndinayesetsa kusintha khalidwe langa n’cholinga choti ndifanane ndi anzanga. Poyamba, zinkaoneka ngati zikugwira koma kenako ndinazindikira kuti munthu suyenera kusintha khalidwe lako kuti anthu azikukonda.”—Anatero Nicole.

Mfundo ya m’Baibulo: “Usamachite zinthu chifukwa chongoonera anthu. . . . Usalole kuti anthu amenewo akunyengerere kuti uzichita zinthu zoipa.”—Ekisodo 23:2, Holy Bible—Easy to Read Version.

KUZUNZA ENA

Anthu ambiri amandikonda ndipo ndikufuna kuti apitirizebe kundikonda.

Ndikhoza kuchita chilichonse kuti ndipitirizebe kukhala wotchuka ndipo ndilibe nazo ntchito ngakhale anthu ena azizunzika ndi zimenezi.

“Nthawi zambiri achinyamata samvera ena chisoni ndipo chifukwa chakuti amene amazunza anzawo amaoneka ngati ochenjera, wachinyamata yemwe ndi wamanyazi akhoza kumangokhulupirira kuti zonse zimene iwo akunena ndi zoona.”—Anatero Raquel.

Mfundo ya m’Baibulo: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31.

NJIRA YOYENERA

1 Dziwani mfundo zimene mumayendera. Baibulo limanena kuti anthu okhwima mwauzimu amadziwa “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”—Aheberi 5:14.

2 Musamalole kuphwanya mfundo zimene mumayendera. Muzikhala ngati Yoswa, amene ananena molimba mtima kuti: “Sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira. . . . Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.

3 Musamachite mantha ena akamatsutsa mfundo zimene mumayendera. Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Mulungu sanatipatse mzimu wamantha, koma wamphamvu.”—2 Timoteyo 1:7.

Kutsatira mfundo zitatu zimenezi kungachititse kuti musakhale wotchuka kwenikweni, komabe anthu amakhalidwe abwino angamakukondeni.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 16, 17]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU ANANENA

Melissa—Kumangotsatira zimene anzako a kusukulu akuchita n’kupusa. Koma kukhala ndi makhalidwe abwino monga Mkhristu kumachititsa kuti ukhale wosiyana ndi anthu ena ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu azikukonda m’malo mokuona ngati munthu wovuta kumumvetsa.

Ashley—Poyamba ndikakhala kusukulu ndinkaona kuti anthu samandikonda koma ndikapita kukasonkhana ndi Akhristu anzanga ndinkamva bwino chifukwa ndikamacheza nawo ndinkaona kuti amandikonda ndi mtima wonse. Zikatero, chidwi chonse chofuna kuti anzanga a kusukulu azindikonda chinkatha.

Phillip—Chinsinsi choti anthu azikukondani ndi kuyamba inuyo kuwakonda. Chaposachedwapa ndakhala ndikuyesetsa kuchitira anzanga tizinthu ting’onoting’ono ndipo zimenezi zachititsa kuti azindikonda kwambiri.