Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Akulusa Kwambiri?

N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Akulusa Kwambiri?

N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Akulusa Kwambiri?

ZINTHU zimene zimachititsa kuti anthu azipsa mtima ndi zovuta kumvetsa. Ndipo ngakhale asayansi amavomereza kuti anthu ambiri sadziwa bwinobwino chimene chimachititsa kuti anthu azipsa mtima. Koma mfundo imene ngakhale azachipatala amavomereza ndi yakuti pali zinthu zinazake zimene zimachititsa kuti tonsefe tizipsa mtima.

Pali zinthu zambiri zimene zingachititse munthu kupsa mtima. Mwachitsanzo, akhoza kupsa mtima chifukwa chakuti anthu ena amuchitira zinthu zopanda chilungamo kapena amunyoza. Nthawi zinanso munthu akhoza kukwiya chifukwa choganiza kuti anthu ena akufuna kumulanda udindo kapena akufuna kuwononga mbiri yake.

Koma zinthu zimene zimachititsa anthu kupsa mtima zimasiyanasiyana potengera zaka za munthu kapena chikhalidwe. Zimatengeranso ngati ndi wamwamuna kapena wamkazi. Komanso zimene munthu amachita akapsa mtima zimasiyana. Ena sakwiya kawirikawiri ndipo amati akakwiya sachedwa kuiwala, pomwe ena sachedwa kukwiya ndipo akakwiya amakhalabe choncho kwa nthawi yaitali, mwina kwa masiku, milungu, miyezi kapena kuposerapo.

Masiku ano padzikoli pakuchitika zinthu zambiri zomwe zingachititse munthu kupsa mtima. Kuwonjezera pamenepo, anthu nawonso sakuchedwa kulusa poyerekeza ndi kale. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti anthu ambiri ndi odzikonda ndipo amachita zinthu mosaganizira ena. Baibulo limati: “Masiku otsiriza . . . anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, . . . odzitukumula ndiponso onyada.” (2 Timoteyo 3:1-5) Mukhoza kuvomereza kuti anthu ambiri ali ndi makhalidwe amenewa.

Kunena zoona, anthu odzikonda amapsa mtima akalephera kupeza zimene akufuna. Koma palinso zifukwa zina zimene zikuchititsa kuti anthu ambiri azipsa mtima. Taonani zina mwa zifukwa zimenezi.

Zimene Ana Amaona kwa Makolo Awo

Zimene makolo amachita zimakhudza kwambiri ana awo moti akamakula amatengera zomwezo. Dokotala wina, dzina lake Harry L. Mills, anati: “Anthu amakula ndi mtima wosachedwa kukwiya potengera zimene makolo awo ankachita.”

Ngati mwana waleredwera m’banja limene makolo ake amakonda kukangana ngakhale pa zinthu zazing’ono, amakula ndi maganizo akuti akakumana ndi vuto linalake njira yabwino yothetsera vutolo ndi kulusa. Tingayerekezere mwanayu ndi kambewu kamene kamathiridwa madzi oipa. Kambewuko sikangakule bwino. Khalidwe la makolo losachedwa kupsa mtima lili ngati madzi oipa, ndipo ana amene amakulira m’banja lotero amadzakhalanso osachedwa kupsa mtima.

Kukhala M’mizinda Yochuluka Anthu

M’chaka cha 1800, pafupifupi anthu atatu pa 100 alionse padziko lonse ankakhala m’madera a m’tawuni. Koma pofika m’chaka cha 2008, anthu 50 pa 100 alionse ankakhala m’tawuni ndipo zikuoneka kuti podzafika m’chaka cha 2050, anthu 70 pa 100 alionse azidzakhala m’tawuni. Kudzazana kwa anthu m’mizinda kukuchititsa kuti anthuwo azikhala ndi nkhawa ndiponso asamachedwe kulusa. Mwachitsanzo, mzinda wa Mexico City ndi umodzi mwa mizinda ikuluikulu padziko lonse ndipo uli ndi anthu ambiri. Chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto m’mimsewu ya mumzindawu, anthu sachedwa kulusa. Mtolankhani wina ananena kuti popeza mzinda wa Mexico City uli ndi anthu pafupifupi 18 miliyoni ndi magalimoto 6 miliyoni, “ndiye kuti anthu a mumzindawu amakhala ndi nkhawa kwambiri kuposa anthu a m’mizinda ina padziko lonse. M’misewu mumadzaza magalimoto ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu azilusa kwambiri.”

M’mizinda momwe muli anthu ambiri mumakhalanso mavuto ena monga kuwonongeka kwa mpweya, phokoso, kusowa kwa nyumba, kusiyana zikhalidwe komanso umbava ndi ziwawa. Chifukwa chakuti mavuto amenewa akuwonjezereka, anthu akumakhala ndi nkhawa ndipo sakumachedwa kupsa mtima.

Mavuto Azachuma

Mavuto azachuma amene ali padziko lonse akuchitisa kuti anthu azikhala ndi nkhawa kwambiri. Lipoti lina la bungwe loona zachuma padziko lonse (International Monetary Fund) ndiponso la nthambi ya United Nations yoona za anthu a pa ntchito (International Labor Organization) linanena kuti: “Zikuoneka kuti padziko lonse anthu oposa 210 miliyoni ali pa ulova.” Chomvetsanso chisoni n’chakuti ambiri mwa anthu amene anachotsedwa ntchito alibe njira iliyonse yopezera ndalama.

Komanso ngakhale anthu amene ali pa ntchito zinthu siziwayendera bwino kwenikweni. Malinga ndi lipoti la bungwe loona za anthu a pa ntchito lija, anthu ambiri padziko lonse amakhala ndi nkhawa chifukwa cha ntchito imene akugwira. Munthu wina yemwe amagwira ntchito yolangiza mabwana a makampani osiyanasiyana mumzinda wa Ontario ku Canada, dzina lake Lorne Curtis, anati: “Anthu amaopa kuchotsedwa ntchito, zimene zimachititsa kuti asamavomereze akalakwitsa zinthu komanso amakonda kukangana ndi mabwana awo kapena anzawo ogwira nawo ntchito.”

Tsankho Komanso Kupanda Chilungamo

Kodi mungatani mutakhala kuti mwalowa nawo mpikisano wothamanga ndiye mukuuzidwa kuti inuyo nokha muyenera kuthamanga mutamangidwa miyendo? Mwina mungakhumudwe chifukwa mungaone kuti akukusankhani. Ndi mmenenso anthu mamiliyoni ambiri amamvera anthu ena akamawasankha chifukwa cha mtundu wawo kapena zinthu zina. Iwo amapsa mtima akaona kuti anthu ena akuwalepheretsa kupeza ntchito, kukhala ndi nyumba, kuchita maphunziro enaake ndi zinthu zina zofunika.

Pali zinthu zinanso zopanda chilungamo zomwe sitinafotokoze zimene zingachititse munthu kupsa mtima. Ndipotu ambirife tinachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo zoterezi. Zaka zoposa 3,000 zapitazo, mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa, koma panalibe wowatonthoza.” (Mlaliki 4:1) Zinthu zopanda chilungamo zikachuluka, n’kusowanso munthu woti atithandize, zotsatira zake n’zakuti timakwiya.

Zosangalatsa Zimene Amaonera

Pachitika akafukufuku ambiri ofuna kudziwa mmene ana amakhudzidwira akamaonera zachiwawa pa TV ndi pa zipangizo zina. James P. Steyer, yemwe ndi mkulu wa bungwe linalake (Common Sense Media) anati: “Anthu amene akhala akuonera zinthu zachiwawa kuyambira ali ana amafika poona kuti zachiwawazo si zolakwika ndipo munthu wina akamazunzidwa samva chisoni.”

Ndi zoona kuti achinyamata ambiri amene amaonera zachiwawa sakhala zigawenga zoopsa akakula. Komabe, nthawi zambiri mafilimu amene amaonera amasonyeza kuti kupsa mtima komanso kuchita zinthu zachiwawa si kolakwika ndipo kumathandiza munthu kuthana ndi mavuto. Chifukwa cha zimenezi anthu ambiri amaona kuti kuchita zachiwawa si kolakwika.

Mphamvu ya Ziwanda

Baibulo limanena kuti pali mphamvu inayake imene imachititsa anthu kuti azikhala olusa. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Kale Mulungu atangolenga anthu, mngelo wina woipa anapandukira Mulungu Wamphamvuyonse. Mngelo woipa ameneyu ndi Satana, dzina la Chiheberi lomwe limatanthauza “Wotsutsa” kapena “Mdani.” (Genesis 3:1-13) Kenako, Satana anachititsanso kuti angelo ena apandukire Mulungu.

Angelo osamverawo, amene amadziwikanso kuti ziwanda kapena mizimu yoipa, anaponyedwa kudziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Ndiponso “ali ndi mkwiyo waukulu” podziwa kuti atsala ndi kanthawi kochepa. Choncho, ngakhale kuti sitingathe kuona mizimu yoipa imeneyi, timatha kuona zochita zawo. Kodi timaziona m’njira yotani?

Satana ndi ziwanda zake amapezerapo mwayi pa kupanda ungwiro kwathu n’kumachititsa “udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, . . . maphwando aphokoso, ndi zina zotero.”—Agalatiya 5:19-21.

Pewani Kupsa Mtima

Tikaganizira za mavuto onse amene anthu akukumana nawo, kupanikizika ndiponso nkhawa zimene ali nazo, tikhoza kumvetsa chifukwa chake masiku ano anthu ambiri sakuchedwa kupsa mtima.

Nthawi zambiri munthu akaputidwa chimene amafuna n’kubwezera basi. Nkhani yotsatira itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizipewa kupsa mtima kwambiri.

[Bokosi patsamba 5]

KODI MUNGADZIWE BWANJI KUTI MULI NDI VUTO LOPSA MTIMA?

▶ Ngati mumakwiya chifukwa chodikira nthawi yaitali pamzere.

▶ Ngati nthawi zambiri mumakangana ndi anzanu kuntchito.

▶ Ngati nthawi zambiri mumasowa tulo chifukwa choganizira zinthu zimene zakukhumudwitsani tsiku limenelo.

▶ Ngati zimakuvutani kukhululukira anthu amene akulakwirani.

▶ Ngati simuchedwa kukhumudwa komanso mumangodandaula nthawi zonse.

▶ Ngati nthawi zambiri mumachita manyazi kapena kudziimba mlandu mukakwiya. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 36 Mfundozi zachokera ku bungwe lina limene adiresi yake ya pa Intaneti ndi MentalHelp.net.

[Bokosi patsamba 6]

ZOTSATIRA ZA KAFUKUFUKU WOKHUDZA KUPSA MTIMA

Bungwe lina la zachipatala ku London, ku England, (Mental Health Foundation) linatulutsa lipoti lofotokoza zotsatira za kafukufuku amene linachita. Zina mwa mfundo zikuluzikulu zimene anapeza ndi izi:

Anthu 84 pa 100 alionse amaona kuti ntchito yawo imawapanikiza kwambiri kuposa mmene ankaonera zaka zisanu zapitazo.

Anthu 65 pa 100 alionse ogwira ntchito analusapo wina atawapsetsa mtima kuntchito.

Anthu 45 pa 100 alionse ogwira ntchito amapsa mtima kawirikawiri kuntchito.

Anthu 60 pa 100 alionse amajomba kuntchito chifukwa cha nkhawa.

Anthu 33 pa 100 alionse a ku Britain anadana ndi anthu oyandikana nawo nyumba moti salankhulana.

Anthu 64 pa 100 alionse amavomereza kuti masiku ano anthu padziko lonse akupsa mtima kwambiri.

Anthu 32 pa 100 alionse ananena kuti ali ndi mnzawo kapena wachibale amene ali ndi vuto lopsa mtima kwambiri.

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi khalidwe la makolo losachedwa kupsa mtima lingakhudze bwanji ana awo?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi mafilimu amene mumakonda amachititsa kuti musamachedwe kupsa mtima?