Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyumba Zachitetezo za ku Terezín Zinalephera Kuteteza Anthu

Nyumba Zachitetezo za ku Terezín Zinalephera Kuteteza Anthu

Nyumba Zachitetezo za ku Terezín Zinalephera Kuteteza Anthu

TEREZÍN, ndi tawuni yomwe ili pakati pa mzinda wa Dresden ndi Prague ku Ulaya ndipo imadziwikanso ndi dzina lakuti Theresienstadt. Tawuniyi ili ndi nyumba zomwe zimagwiranso ntchito ngati mipanda ikuluikulu yachitetezo. Nyumbazi zinamangidwa pofuna kutchingira asilikali a mayiko ena kuti asadzalowe n’kulanda dzikolo. Komanso nyumbazi zinamangidwa pofuna kuteteza anthu amene ankakhala m’madera apafupi ndi tawuniyi.

Mfumu Joseph Yachiwiri ya ku Germany, yomwenso inkalamulira ufumu wa Roma, ndi imene inalamula kuti nyumbazi zimangidwe. Mfumuyi inalipo pa nthawi yomwe akatswiri ankayendera malo, komanso pa nthawi imene anayamba ntchito yomanga nyumbazi, chakumapeto kwa zaka za m’ma 1780. Nyumbazi zinamangidwa polemekeza amayi ake a mfumuyi, omwe dzina lawo linali Mfumukazi Maria Theresa. Choncho tawuniyi anaipatsa dzina la Chijeremani lakuti Theresienstadt, kutanthauza “Tawuni ya Theresa.” * Anthu ena amanena kuti nthawi zina pamalowa pankapezeka anthu okwana 14,000 ogwira ntchito yomanga. Mbali yaikulu ya ntchitoyi inatha patapita zaka zinayi.

Ntchito yomanga nyumba zachitetezo za ku Terezín inatha mu 1784 ndipo zinali zazikulu kwambiri kuposa nyumba zina zoterezi za m’madera onse a ku Hapsburg. Nyumbazi anazimanga mwapamwamba kwambiri kusiyana ndi nyumba zina zoterezi za pa nthawiyo. Komabe, pa nthawi yomwe nyumba zachitetezozi zinkamangidwa n’kuti zinthu zitasintha kwambiri pa nkhani ya kamenyedwe ka nkhondo.

Pa nthawi imeneyi, asilikali akafuna kulanda dziko sankalimbana ndi kugwetsa nyumba zachitetezo. Iwo ankangobwera m’midzi yapafupi n’kuyamba kupha anthu komanso kuwononga zinthu. Choncho pofika m’chaka cha 1888, tawuni ya Terezín siinalinso malo achitetezo pa nkhani ya nkhondo. Mipanda yake yakunja anaisandutsa mapaki okongola omwe anali ndi tinjira todutsamo komanso malo okhalapo.

Mmene Nyumbazi Zinamangidwira

Nyumba za ku Terezín zinamangidwa kuti ziziteteza dzikolo pa nthawi ya nkhondo. M’nyumbazi munkakhala asilikali ndi mabanja awo komanso anthu ena.

Pafupi ndi nyumba zikuluzikulu panali nyumba zazing’ono zomwe zinkagwira ntchito ngati ndende za asilikali. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800, adani a ufumu wa Hapsburg ankasungidwa ku ndende zimenezi. Kenako patatha zaka pafupifupi 100, akaidi achinyamata amene anapezeka ndi mlandu wopha Archduke Francis Ferdinand ku Sarajevo, m’chaka cha 1914, anaikidwanso m’ndende zimenezi. Achinyamatawa sanapatsidwe chilango cha imfa chifukwa anali asanakwanitse zaka 20. Koma pasanapite nthawi, ambiri mwa anyamatawa anafera m’ndendemo. Iwo ankazunzidwa kwambiri moti ena anachita misala. Gavrilo Princip, mnyamata amene anapha Ferdinand, anafera kundendeyi nkhondo yoyamba ya padziko lonse ili mkati.

Ndende zimenezi zinali zoopsa kwambiri kuposa ndende ina iliyonse ku Austria-Hungary. Nthawi zambiri akaidi ankakhala pa malo ozizira komanso onyansa atamangidwa unyolo. Ndipo pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, kundendezi ankazunzirako komanso kupherako anthu.

Kodi M’tawuni ya Terezín Munkachitika Zotani?

Dziko la Germany litalanda dziko limene masiku ano limadziwika kuti Czech Republic, linayamba kugwira Ayuda m’chaka cha 1941 n’kumakawasunga m’tawuni ya Terezín. Akuluakulu a chipani cha Nazi anasintha tawuniyi n’kukhala mudzi wa Ayuda okhaokha. Iwo ankanena kuti Ayuda asamakhale pamodzi ndi anthu ena n’cholinga choti pasamakhale mikangano. Chipani cha Nazi chinkanamiza anthu kuti tawuni ya Terezín ndi mudzi wa Ayuda komanso malo othandizira Ayudawo. Komabe, cholinga chenicheni cha chipanichi chinali kupha Ayuda onse.

Komanso chipani cha Nazi chinali chitakhazikitsa kale ndende zopherako Ayuda chakum’mawa kwa Ulaya ndipo chinkapherako Ayuda amene awatenga m’tawuni ya Terezín ndi madera ena. * Ngakhale kuti cha mu 1935 anthu ankadziwa kuti kuli ndende zimenezi, chipani cha Nazi chinayesetsa kuchita zinthu zoti anthu aziganiza kuti ndendezo ndi malo ongothandizira anthu kusintha khalidwe. Koma kenako kunayamba kumveka mphekesera zoti anthu akuzunzidwa kwambiri kundende zimenezi. Choncho, anthu ankafunitsitsa kuti akuluakulu a chipani cha Nazi akayankhe milandu. Chifukwa cha zimenezi, chipani cha Nazi chinakonza zoti chifotokozere mayiko zimene zimachitika ku ndende zimenezi. Kodi akuluakulu a chipanichi anatani?

M’chaka cha 1944 ndi 1945, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ili m’kati, akuluakulu a bungwe la Red Cross anaitanidwa kuti akaone okha zimene zinkachitika m’tawuniyo. Koma pofuna kupusitsa akuluakuluwo kuti aziganiza kuti palibe choopsa chilichonse chomwe chinkachitika kumalowa, akuluakulu a chipani cha Nazi anakongoletsa malowo.

Anachotsa manambala a zipinda za ndende n’kuika mayina a misewu ochititsa chidwi. Anakonzanso bwinobwino nyumba zina kuti zizioneka ngati banki, sukulu ya mkaka komanso mashopu. Anatsegulanso lesitilanti pakati penipeni pa tawuniyi. Anakonzanso nyumba zakale kuti zizioneka ngati zatsopano, anabzala maluwa okongola m’mapaki ndiponso anakonza malo amene oyimba angamabwere kudzaimba.

Kenako, akuluakulu a Red Cross anaitanidwanso kuti adzayendere malowa. Achipani cha Nazi ananamiza akuluakulu a Red Cross kuti Ayuda ankaloledwa kudzilamulira okha m’tawuniyo ndipo akuluakuluwo analoledwa kulankhula ndi omwe ankati ndi anthu oimira boma la Ayudawo. Koma anthu amenewa anasankhidwa ndi akuluakulu a Nazi ndipo anachita kuwauza zoti akayankhe akakafunsidwa mafunso. Kwa maulendo awiri, achipani cha Nazi anakwanitsa kupusitsa akuluakulu a Red Cross omwe anadzayendera malowo. M’lipoti limene analemba, akuluakulu a Red Cross analemba zinthu zosalondola zoti Ayuda a m’tawuni ya Terezín akukhala mwamtendere ndipo akusamalidwa bwino. Koma a Red Cross atangochoka, achipani cha Nazi anapitiriza kuzunza ndiponso kupha Ayuda ndipo ena ankafa ndi njala. Ndi Ayuda ochepa okha amene anapulumuka n’kuona kutha kwa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse.

Zimene Zinkachitika ku Nyumba Zing’onozing’ono Zija

Zina mwa nyumba zing’onozing’onozi zinkagwiritsidwa ntchito ngati ndende. M’ndende zimenezi anthu ankazunzidwa kwambiri ngati mmene zinalili m’ndende zina. Anthu ambirimbiri amene ankaikidwa m’ndende zimenezi ankangosungidwa kwa kanthawi chabe poyembekezera kuti awasamutsire kundende zikuluzikulu za m’madera amene ankalamulidwa ndi dziko la Germany.

Pafupifupi a Mboni za Yehova okwana 20, ochokera m’mizinda ya Prague, Pilsen ndi madera ena, anatsekeredwa m’ndendezi. Kodi anthu amenewa anapalamula mlandu wotani? Anakana kulowa usilikali komanso sankalowerera ndale. Ngakhale kuti ntchito yolalikira inali italetsedwa, Mboni za Yehova zinapitirizabe kuuza ena uthenga wabwino wa m’Baibulo. Ena mwa iwo anaphedwa kapena kuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Nkhaniyi?

Baibulo limati: “Musamakhulupirire anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso. Mzimu wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.” (Salimo 146:3, 4) Nyumba zachitetezo za ku Terezín ndi umboni wosatsutsika wosonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yolondola.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mfumukaziyi inalinso mayi ake a Marie Antoinette, amene anadzakhala mfumukazi ya ku France.

^ ndime 12 Mukafuna kudziwa zambiri pa nkhaniyi, werengani Galamukani! ya September 8, 1995, tsamba 3 mpaka 15, ndi ya April 8, 1989, tsamba 3 mpaka 20.

[Bokosi patsamba 20]

MBONI ZA YEHOVA M’NDENDE YA KU TEREZÍN

Mboni za Yehova zambiri zimene zinkaikidwa m’ndende ya ku Terezín, zinkafunsidwa kaye mafunso ndi apolisi achinsinsi a Gestapo, ku likulu lawo lomwe linali mumzinda wa Prague. Nthawi zambiri ankati akawasunga kundende ya ku Terezín kwa kanthawi, ankawatumiza kundende zosiyanasiyana za ku Germany. A Mboni za Yehova ankakumana ndi mavuto aakulu m’ndende zimenezi komanso ankaikidwa kwaokha. Ndiye kodi ankapirira bwanji mavuto amenewa?

Mayi wina wa Mboni, amene anaikidwa m’ndende ya ku Terezín, ananena kuti: “Ndinkawerenga Baibulo pafupipafupi chifukwa sindinkafuna kuiwala zimene limaphunzitsa. Akandisamutsira kundende ina, ndinkafufuza a Mboni anzanga ndipo ndikawapeza ndinkayesetsa kumacheza nawo. Komanso ndikapeza mpata ndinkalalikira kwa ena.”

Kuchita zimenezi kunamuthandiza kwambiri mayiyu. Iye anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu pa nthawi yonse yomwe anali kundende komanso atatuluka.

[Chithunzi patsamba 18]

Chidindo chosonyeza nyumba zachitetezo za ku Terezín pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse

[Chithunzi patsamba 19]

Akaidi atsopano ankaperekezedwa kokagwira ntchito. Mawu amene ali pakhomopo ndi a Chijeremani akuti: “Arbeit Macht Frei” (Ntchito Imapatsa Mtendere)

[Chithunzi patsamba 19]

Mabedi osanjikizana m’ndende ya azimayi

[Chithunzi patsamba 20]

Polowera popita kunyumba zazing’ono zomwe ankazigwiritsa ntchito ngati ndende

[Mawu a Chithunzi patsamba 19]

Both photos: With courtesy of the Memorial Terezín