Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Chiwerengero cha maukwati amene akulembetsedwa ku boma ku England ndi ku Wales chatsika kwambiri kuyerekeza ndi pa nthawi imene anthu anayamba kulembetsa maukwati,” m’chaka cha 1862.—OFFICE FOR NATIONAL STATISTICS, BRITAIN.

Mabwana opitirira hafu ya mabwana onse a makampani ang’onoang’ono omwe sali m’manja mwa boma ku United States, “amayembekezera kuti chaka chilichonse antchito awo akhoza kuba chinthu chinachake cha ndalama zambiri [pakampanipo].”—REUTERS NEWS SERVICE, U.S.A.

Bungwe lina la boma ku China linanena kuti pasanathe ndi chaka chomwe kuchokera pamene akuluakulu a dzikolo anayamba ntchito “yotseka malo onse oonetsa zinthu zolaula pa Intaneti, anali atatseka malo okwana 60,000 oonetsa zolaula.”—CHINA DAILY, CHINA.

“Anthu oposa 215 miliyoni—yomwe ndi 3 peresenti ya chiwerengero cha anthu padziko lonse, anasamuka m’mayiko awo n’kumakakhala m’mayiko ena.”—UNITED NATIONS INTERNATIONAL FUND FOR AGRICULTURAL DEVELOPMENT, ITALY.

“Tsiku lililonse ku India, ana a sukulu okwana 19 amadzipha ndipo pa ana amenewa, ana 6 amadzipha chifukwa choopa mayeso.”—INDIA TODAY INTERNATIONAL, INDIA.

Juga Yapita Patsogolo Kwambiri

Ku Germany munthu wochita juga amawononga ndalama zambiri kuwirikiza ka 10 poyerekeza ndi munthu yemwe sachita juga. Nyuzipepala ina ya m’dzikolo (Süddeutsche Zeitung) inanena kuti anthu amene juga inawalowerera ndi “omwe akuchititsa kuti makampani a juga azipindula kwambiri.” Pofuna kuti azipeza phindu lalikulu, makampani a juga akupanga makina awo m’njira yakuti munthu akayamba kuchita juga asamafunenso kusiya. Makinawo amachita zinthu mofulumira kwambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti munthu akomedwe n’kumangodyedwa ndalama zambiri. Makampaniwa akuona kuti njira imeneyi ikuwathandiza kupeza ndalama zankhaninkhani. Akuti 56 peresenti ya ndalama zonse zimene makampaniwa amapeza zimachokera kwa anthu amene juga inawalowerera kwambiri. Ndipo 38 peresenti ya ndalama zimene makampaniwa akupeza zikuchokera m’malo ochitira juga amene iwo anakhazikitsa m’madera osiyanasiyana, ndipo 60 peresenti ikuchokera pamalo awo ochitira juga a pa Intaneti.

Nthawi Yabwino Yokakumana ndi Woweruza Milandu

Kodi mukudziwa kuti pali zinthu zina zimene zingachititse kuti milandu isaweruzidwe bwino? Akatswiri ena ku Israel anachita kafukufuku pa nkhaniyi. Iwo anafufuza milandu ya anthu oposa 1,000 amene anatulutsidwa m’ndende nthawi imene anawalamula isanathe. Ofufuzawo anapeza kuti milandu yambiri imene oweruza anagamula atangodya kumene chakudya chamasana kapena kumwa tiyi pa nthawi yopuma, sinakomere oimbidwa milandu. Akuti chiwerengero cha milandu imene inaweruzidwa mokomera anthuwo chinatsika ndi 65 peresenti. Kenako chiwerengerocho chinakweranso ndi 65 peresenti atachoka komwa tiyi pa nthawi inanso yopuma. Akatswiri ochita kafukufukuwa ananena kuti zimenezi zikusonyeza kuti si nthawi zonse pamene zigamulo zimaperekedwa mogwirizana ndi mmene mlandu ulili kapena motsatira malamulo. Iwo anafotokoza kuti zigamulo “zingaperekedwe mogwirizana ndi zinthu zina zosagwirizana ndi malamulo.”