Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitamba cha Njovu

Chitamba cha Njovu

Kodi Zinangochitika Zokha?

Chitamba cha Njovu

● Akatswiri ofufuza akupanga mkono wochita kuikirira womwe munthu azidzatha kuupinda mosavuta. Munthu wina yemwe amagwira ntchito pa kampani imene ikupanga mkono umenewu, ananena kuti “mkonowu upangidwa mwapamwamba kwambiri kuposa chilichonse chimene chapangidwa kale ndi makampani opanga zinthu za mtunduwu.” Kodi maganizo oti apange mkono wotere anabwera bwanji? Munthu uja ananena kuti maganizo oti apange mkonowo anabwera “potengera chitamba cha njovu.”

Taganizirani izi: Chitamba cha njovu chimalemera makilogalamu 140, ndipo anthu ena amanena kuti “chitamba cha njovu chimagwira ntchito zosiyanasiyana kuposa chiwalo chilichonse.” Chitambachi chimagwira ntchito ngati mphuno, kamwa yomwera madzi, mkono kapena dzanja. Komanso njovu imagwiritsa ntchito chitambachi ikafuna kulira mokweza.

Koma chitambachi chimagwiranso ntchito zina. Chili ndi minyewa pafupifupi 40,000, yomwe imathandiza kuti chizipindika mosavuta, moti njovu ikhoza kutola ndalama yachitsulo yaing’ono kwambiri pogwiritsa ntchito nsonga ya chitambacho. Komanso njovu imatha kunyamula katundu wolemera makilogalamu 270 pogwiritsa ntchito chitamba chake.

Akatswiri ofufuza akukhulupirira kuti akhoza kupanga zipangizo zapamwamba kwambiri potengera chitamba cha njovu. Akuti zipangizozi zingamathandize kwambiri m’mafakitale kapena m’nyumba za anthu. Munthu winanso yemwe amagwira ntchito pa kampani tainena poyambirira ija anati: “Chipangizo chimene tikupangachi n’chapamwamba kwambiri ndipo n’chosiyana kwambiri ndi zipangizo zina zomwe zilipo kale chifukwa anthu akhoza kuchigwiritsa ntchito popanda vuto lililonse.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti njovu ikhale ndi chitamba choterechi, kapena pali wina amene anachipanga?