Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabanja a Ana Opeza Omwe Akuyenda Bwino

Mabanja a Ana Opeza Omwe Akuyenda Bwino

Mabanja a Ana Opeza Omwe Akuyenda Bwino

PANOPA TIMAGWIRIZANA KWAMBIRI

Philip ankakhala ndi mwana wake wamkazi wazaka 20, dzina lake Elise, ndipo mwanayu ndi amene ankagwira ntchito zambiri zapakhomo. Kenako Philip anakwatira mkazi wina, dzina lake Louise. Kodi zinthu zinkayenda bwanji pakati pa Elise ndi mayi ake opezawo?

Louise: Poyambirira zinthu zinkavuta kwambiri. Ineyo mwachibadwa ndimakonda kukhala pakhomo n’kumagwira ntchito.

Elise: Mayi anga atsopanowa anasinthasintha zinthu, ndipo anataya zinthu zambiri za m’nyumbamo zimene anazipeza. Tsiku lina ndikukonza m’nyumba, ndinaika zinthu zina pamalo olakwika chifukwa sindinkadziwa kuti ziyenera kukhala pati. Mayi angawo ataona zimenezi anakwiya. Tinakangana, moti tinatha mlungu umodzi tisakulankhulana.

Louise: Ndimakumbukira kuti nthawi ina ndinauza Elise kuti, “Zimene zikuchitika m’nyumba muno zanditopetsa. Sindingathe kukhala mmene tikukhaliramu.” Madzulo, Elise anabwera kudzapepesa chifukwa cha zimene zinachitikazo. Tinakumbatirana ndipo tonse tinalira.

Elise: Posintha zinthu, mayi angawo sanachotse zithunzi zanga zimene zinali pakhoma, komanso bambo anga sanachotse timagetsi tokongoletsera m’nyumba timene ndinatiika pamalo ochezera m’nyumbamo. Zimenezi zingaoneke zazing’ono, koma zinandithandiza kuona kuti kubwera kwawo sikunasinthe zinthu kwambiri. Ndimayamikiranso kwambiri kuona mmene mayi anga ondilerawo amasamalirira mchimwene wanga wamng’ono akabwera kudzacheza. Papita zaka ziwiri ndipo tsopano ndayamba kuwaona ngati mayi anga enieni.

Louise: Panopa timagwirizana kwambiri, monga munthu ndi mnzake osati ngati anthu ongokhala m’nyumba imodzi.

“KUGWIRIZANA N’KOFUNIKA KWAMBIRI”

Anton ndi Marelize anakwatirana zaka 6 zapitazo. Pa nthawiyi n’kuti aliyense ali ndi ana atatu.

Anton: Timachitira zinthu limodzi monga banja, ndiponso timayesetsa kupeza nthawi yocheza ndi mwana aliyense payekha. Zinatitengera zaka zingapo kuti tizolowerane bwinobwino koma panopa timagwirizana pa zinthu zambiri.

Marelize: Timaona kuti ndi bwino kumati “ana athu,” m’malo mwa “ana ako” kapena “ana anga.” Ndimakumbukira kuti nthawi ina ndinakhumudwa chifukwa choona ngati mwamuna wanga Anton anachita zinthu mokondera. Iye anadzudzula mwana wanga wamwamuna n’kumuuza mwana wake wamkazi kuti akakhale mpando wakutsogolo m’galimoto yathu, umene aliyense ankaukonda. Koma patapita nthawi ndinazindikira kuti kugwirizana n’kofunika kwambiri kuposa kukhala mpando wakutsogolo. Tsopano timayesetsa kuchita zinthu mosakondera ngakhale kuti n’zosatheka kuchitira zofanana mwana aliyense.

Ndiponso ndimapewa kulankhula za zinthu zomwe zinkandisangalatsa zokhudza banja langa lakale n’cholinga choti enawo asamaone ngati ndimakonda kwambiri banja lakalelo kuposa latsopanoli. M’malomwake, ndimayesetsa kuyamikira zinthu zabwino zokhudza banja lathu latsopanoli.

“TIMAYAMIKIRANA KAYE”

Francis anakwatirana ndi Cecelia zaka zinayi zapitazo. Pamene amakwatirana n’kuti Cecelia ali ndi ana atatu, atsikana awiri ndi mnyamata mmodzi, ndipo Francis anali ndi mwana mmodzi wamwamuna.

Francis: Ndimayesetsa kuti ana anga azimasuka nane komanso ndimapewa kumangokhumudwa ndi zilizonse. Nthawi zambiri timadyera limodzi ndipo pa nthawi imeneyi timakambirana zinthu zokhudza banja lathu. Ndimayesetsanso kulimbikitsa aliyense m’banja mwathu kuti azigwira ntchito zapakhomo.

Cecelia: Ndimapatula nthawi yocheza ndi mwana aliyense kuti ndidziwe mavuto amene akukumana nawo. Tikakumana kuti tikambirane nkhani za pabanja pathu, timayamikirana kaye, kenako timakambirana mbali zimene aliyense ayenera kusintha. Ndipo ndikalakwitsa ndimavomereza n’kupepesa mochokera pansi pa mtima.

ANALEREDWA NDI MAKOLO OMUPEZA OKHAOKHA

Yuki, yemwe ali ndi zaka 20, analeredwa ndi mayi ake okha kuyambira ali ndi zaka zisanu. Kenako mayi akewo anakwatiwa ndi mwamuna wina, dzina lake Tomonori. Koma Yuki ali ndi zaka 10, mayi akewo anamwalira. Patapita zaka zina zisanu, bambo ake omupezawo anakwatira mkazi wina, dzina lake Mihoko. Zimenezi zinachititsa kuti Yuki aleredwe ndi makolo omupeza okhaokha.

Yuki: Nditazindikira kuti bambo anga ondilerawo akufuna kukwatiranso, sindinagwirizane nazo. Ndinkaona kuti sindikufunikira mayi ena atsopano chifukwa panali zinthu zambiri zimene zinali zitasintha kale m’banja mwathu. Zinandivuta kwambiri kuvomereza moti atakwatira sindinkagwirizana ndi mayiwo.

Mihoko: Ngakhale kuti mwamuna wanga sankandikakamiza kuti ndizimukonda Yuki ngati mmene iye amamukondera, ndinkayesetsa kuti ndizigwirizana naye kwambiri. Tinkaonetsetsa kuti tisasinthe zinthu zimene iye ankakonda kuchita, monga zinthu zauzimu, zosangalatsa komanso kucheza madzulo alionse tikamaliza kudya. Ndinayambanso kumumvetsa kwambiri atandiuza mmene amamvera akaganizira za imfa ya amayi ake.

Ndili woyembekezera, tinkada nkhawa kuti zimukhudza bwanji Yuki. Tinkafuna kuti iye azionabe kuti ndi mwana wathu. Mwanayo atabadwa, Yuki ankamudyetsa, kumusambitsa ndiponso kumusintha thewera. Tinkamuyamikira Yuki pamaso pa anthu chifukwa cha zimenezi. Panopa mwanayo, yemwe dzina lake ndi Itsuki, amakondana kwambiri ndi Yuki. Iye asanaphunzire n’komwe mawu akuti “bambo” kapena “mayi,” anali atayamba kale kumutchula Yuki kuti niinii, kutanthauza achimwene.

Yuki: Monga mwana wopeza, nthawi zina ndimadzimva ngati mlendo. Ukamafotokozera anthu ena mmene ukumvera, amaoneka kuti sakukumvetsa kwenikweni. Komabe, Akhristu anzanga akhala akundithandiza kwambiri ndikakhala ndi nkhawa. Panopa ndimagwirizana kwambiri ndi mayi anga ondipezawo. Iwo amandipatsa malangizo othandiza kwambiri ndipo ndimawauza zakukhosi kwanga.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

N’zotheka kuti mabanja a ana opeza azikhala osangalala komanso kuti zinthu ziziwayendera bwino. Chofunika n’kudekha