Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuyamikira Ena?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuyamikira Ena?

Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuyamikira Ena?

ANTHU ambiri amaona kuti sayamikiridwa ngakhale achite zabwino. Mwachitsanzo, nthawi zambiri anthu olembedwa ntchito amaona kuti mabwana awo sawayamikira. Ndipo anthu ambiri a pabanja amaona kuti amuna awo kapena akazi awo sawayamikira pa zabwino zimene amachita. Komanso ana ena amaona kuti makolo awo sawayamikira chifukwa choti makolowo amayembekezera kuti anawo achite zimene sangakwanitse. Kunena zoona, zikanakhala kuti aliyense amayesetsa kuyamikira zimene mnzake wachita, bwenzi zimenezi zisakuchitika.

Masiku ano anthu sakonda kuyamikirana, ndipo zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Baibulo linaneneratu kuti: “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, . . . osayamika, osakhulupirika.”—2 Timoteyo 3:1, 2.

Kodi munthu wina anayamba wakuyamikirani kuchokera pansi pa mtima? Ngati ndi choncho, munamva bwanji? Baibulo limanena kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.” (Miyambo 15:23) Kutsatira zimene zili m’Malemba Oyera kungatithandize kuti tizichitira ena zabwino, monga kuwayamikira.

Muziona Makhalidwe Abwino mwa Anthu Ena

Chifukwa chakuti Mulungu amatikonda kwambiri, amaona ndiponso amayamikira makhalidwe komanso zabwino zimene timachita. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Tikamamvera malamulo a Mulungu timasonyeza kuti timam’konda kwambiri ndipo iye amaona zimenezo.

Yehova Mulungu samangoyang’ana zinthu zimene timalakwitsa. Akanakhala kuti amachita zimenezo palibe amene akanaima pamaso pake. (Salimo 130:3) M’malomwake, Yehova ali ngati munthu amene amakumba pansi kuti apeze miyala ya mtengo wapatali. Iye akapeza ngakhale mwala umodzi amasangalala kwambiri. Mwalawo ukhoza kukhala wosaoneka bwino kwenikweni koma iye amaona kuti akaukonza, ukhoza kukhala wamtengo wapatali. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu akamafufuza mitima yathu amafuna aone zinthu zabwino osati zimene timalakwitsa. Iye akapeza zinthu zabwino amasangalala kwambiri. Amadziwa kuti ngati titapitiriza kuchita zinthu zabwinozo, tikhoza kukhala munthu wamtengo wapatali, kapena kuti mtumiki wokhulupirika ndiponso wodzipereka wa Yehova.

Zimene Mulungu amachitazi zimatiphunzitsa zinthu zambiri. Mwachitsanzo, nthawi zina tingamangoona zoipa za anthu ena. Koma ngati titamaona anthu ngati mmene Yehova amawaonera, tidzayesetsa kufufuza zinthu zimene amachita bwino. (Salimo 103:8-11, 17, 18) Tikazipeza zinthuzo, tingawayamikire. Kodi zotsatira zake zingakhale zotani? Mawu athu angawalimbikitse ndipo mwina angamayesetse kwambiri kuchita zabwino. Zikatero, ifeyo tidzasangalala podziwa kuti tawathandiza.—Machitidwe 20:35.

Ena Akachita Zabwino Tiziwayamikira

Nthawi zambiri Yesu ankaona zabwino zimene ena achita ndipo ankawayamikira. Mwachitsanzo, pa nthawi ina mayi wina wodwala anagwira chovala cha Yesu kuti achire. Yesu atazindikira zimenezi, mayiyo anachita mantha kwambiri koma iye anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”—Maliko 5:34.

Komanso pa nthawi ina, Yesu akuphunzitsa m’kachisi ku Yerusalemu anaona anthu ambiri olemera akuponya ndalama m’bokosi la zopereka. Kenako iye anaona mayi wina wamasiye, yemwe anali wosauka kwambiri, akuponya “timakobidi tiwiri tating’ono.” Ena anali ataponya ndalama zambiri kuposa mayiyu. Komabe, Yesu anayamikira mayi wamasiyeyo mochokera pansi pa mtima anthu onse akumva. Iye anati: “Kunena zoona, mkazi wamasiyeyu, ngakhale kuti ndi wosauka, waponya zochuluka kuposa onse amene aponya. Pakuti onsewa aponya zopereka zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.”—Luka 21:1-4.

Kodi tingatsanzire bwanji Yesu? Baibulo limati: “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”—Miyambo 3:27.

Kuyamikira Ena N’kofunika Kwambiri

Masiku ano, pomwe anthu ambiri m’dzikoli ndi osayamika, tonsefe timafuna kuti anthu azitikonda komanso kutiyamikira. Tikamayamikira ena mochokera pansi pa mtima, amalimbikitsidwa ndipo zimawathandiza kupitirizabe kuchita zabwino.—Miyambo 31:28, 29.

Baibulo limatilimbikitsa Akhristu tonse kuti ‘tiziganizirana kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.’ (Aheberi 10:24) Zinthu zikanakhala bwino kwambiri padzikoli ngati munthu aliyense akanati aziyesetsa kukonda anthu ena, kuona zabwino zimene iwo amachita komanso kuwayamikira. Kunena zoona kuyamikira ena n’kofunika kwambiri.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira ena akachita zabwino?—Miyambo 15:23.

● Kodi Yehova akamafufuza mumtima mwathu amafuna kuona chiyani?—2 Mbiri 16:9.

● Kodi tiyenera kuyamikira ena pa zinthu ziti?—Miyambo 3:27.

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mumaona komanso kuyamikira zabwino zimene ena achita?