Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 1

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 1

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 1

“Ine Ndidzatulutsa Mtundu Waukulu mwa Iwe”

Ino ndi nkhani yoyamba mwa nkhani 8 zimene zikhale zikutuluka mu Galamukani! Nkhanizi ndi zonena za maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo. Zikuthandizani kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Kuwerenga nkhanizi kukuthandizani kudziwa zoona zenizeni.

MASIKU ano anthu ambiri amakayikira zimene Baibulo limanena. Ndipo chomvetsa chisoni n’chakuti ena mwa anthu amenewa sanafufuze n’komwe zimene limaphunzitsa. Iwo amangokhulupirira zinthu zabodza zimene ena amanena. Tikukhulupirira kuti inuyo simuli m’gulu la anthu oterewa. Tsopano, tiyeni tikambirane zimene zinachitika kale kwambiri zomwe zimatsimikizira kuti Baibulo ndi buku lolondola.

Choyamba tikambirana za Abulahamu, * yemwe mpaka pano Akhristu, Ayuda komanso Asilamu amamulemekeza kwambiri. Abulahamu anali Mheberi ndipo anabadwa m’chaka cha 2018 B.C.E. n’kumwalira mu 1843 B.C.E. *

Ena mwa maulosi oyambirira a m’Baibulo amakhudza kwambiri Abulahamu, ndipo maulosi amenewa amakhudzanso tonsefe. (Onani bokosi lakuti  “‘Mitundu Yonse’ Idzapeza Madalitso.”) Malinga ndi zimene Baibulo limanena m’buku la Genesis, ena mwa maulosiwa ndi akuti: (1) Mbadwa za Abulahamu zidzakhala mtundu waukulu. (2) M’badwazo zisanafike pokhala mtundu waukulu zidzakhala akapolo m’dziko lina. (3) Mbadwazo zidzapulumutsidwa ku ukapolo n’kukakhala m’dziko la Kanani. Tiyeni tione mfundo zimenezi mwatsatanetsatane.

Maulosi Atatu Amene Anakwaniritsidwa

Ulosi woyamba: “Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe [Abulahamu].”—Genesis 12:2.

Kukwaniritsidwa kwake: Mbadwa za Abulahamu kudzera mwa Isaki ndi Yakobo (yemwe ankatchedwanso Isiraeli) zinadzakhala mtundu wa Isiraeli. Mtundu umenewu unali woima paokha ndipo unkalamuliridwa ndi mafumu.

Zimene mbiri imasonyeza:

● Baibulo limafotokoza mwatsatanetsatane mzera umene Abulahamu anabadwira komanso mbadwa zake zomwe zinachokera kwa Isaki, Yakobo ndi kwa ana 12 a Yakobo. Zina mwa mbadwazo ndi mafumu amene analamulira ku Isiraeli kapena ku Yuda. Pa mafumu amenewo, 17 anatchulidwa m’mabuku ena, osati a m’Baibulo. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti mbadwa za Abulahamu zinadzakhala mtundu waukulu kudzera mwa Isaki ndi Yakobo. *

Ulosi wachiwiri: “Mbewu yako [ya Abulahamu] idzakhala mlendo m’dziko la eni, ndipo idzatumikira eni dzikolo. . . . Koma m’badwo wachinayi udzabwerera kuno.”Genesis 15:13, 16.

Kukwaniritsidwa kwake: Chifukwa cha njala imene inali ku Kanani, mbadwa za Abulahamu zinasamukira ku Iguputo ndipo zinakhala kumeneko mpaka mbadwo wachinayi. Mwachitsanzo, tiyeni titenge mzera umodzi wobadwira wa mbadwa za Levi. Levi anali mdzukulu wa Abulahamu, ndipo anasamukira ku Iguputo ndi bambo ake omwe anali okalamba. Mibadwo inayi kuyambira pa Levi inali (1) Levi, (2) mwana wake Kohati, (3) mdzukulu wake Amuramu ndi (4) mdzukulutuvi wake, Mose. (Ekisodo 6:16, 18, 20) Poyamba iwo ankakhala ngati alendo koma kenako anakhala akapolo oumba njerwa zosakaniza dothi ndi udzu. M’chaka cha 1513 B.C.E., Mose anatsogolera mtundu wa Aisiraeli kutuluka m’dziko la Iguputo.—Onani bokosi lakuti  “Zaka Zokhudza Mbewu ya Abulahamu Komanso Ulendo wa Aisiraeli” ndi lakuti  “Baibulo Limanena Ndendende Nthawi Yomwe Zinthu Zinachitika.”

Zimene mbiri imasonyeza:

● Malinga ndi zimene James K. Hoffmeier, yemwe ndi pulofesa wamaphunziro a Chipangano Chakale komanso katswiri wa zinthu zakale za ku Middle East, mabuku amene anapezeka ku Egypt komanso zinthu zakale zimene anazifukula kumeneko, zimasonyeza kuti pa nthawi imene m’dziko la Kanani munali njala, mbadwa za Semu (monga Aheberi) zinaloledwa kulowa m’dziko la Iguputo ndi ziweto zawo. Koma kodi Aisiraeli anadzakhaladi akapolo oumba njerwa?

● Ngakhale kuti zolemba za ku Egypt sizitchula Aisiraeli, koma zimene akatswiri apeza m’manda komanso m’mipukutu yosiyanasiyana kumeneko, zimasonyeza kuti Aiguputo anali ndi akapolo ochokera kudziko lina omwe ankaumba njerwa zosakaniza dothi ndi udzu. Komanso mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, zolemba za ku Iguputo zimasonyeza kuti anthu amene ankayang’anira akapolo oumba njerwawo, ankalemba chiwerengero cha njerwa zimene zaumbidwa. (Ekisodo 5:14, 19) Katswiri uja ananenanso kuti: “Mabuku ndi zinthu zina za ku Iguputo zimasonyeza kuti Aiguputo anali ndi akapolo ochokera ku dziko lina. . . . Ndipo imeneyi ndi nthawi yomwe Aisiraeli ankazunzidwa. Choncho, tinganene kuti mfundo yakuti Aheberi anasamukira ku Iguputo pa nthawi yanjala komanso kuti anadzakhala akapolo ndi yolondola.”

Ulosi wachitatu: “Ndidzalipereka kwa . . . mbewu yako. . . . Dziko lonse la Kanani.”—Genesis 17:8.

Kukwaniritsidwa kwake: Mose ndi amene anatulutsa mtundu wa Isiraeli m’dziko la Iguputo. Pa nthawiyo mtunduwu unali utangoyamba kumene. Koma Yoswa, mwana wa Nuni, ndi amene anatsogolera mtundu wa Isiraeli kulowa m’dziko la Kanani m’chaka cha 1473 B.C.E.

Zimene mbiri imasonyeza:

● Ngakhale kuti akatswiri a mbiri yakale amatchula madeti osiyanasiyana pa nkhaniyi, munthu wina yemwe anali pulofesa wa zinthu za ku Iguputo, dzina lake K. A. Kitchen, anati: “Pali umboni wokwanira wosonyeza kuti Aisiraeli analowa, n’kumakhala m’dziko la Kanani.”

● Baibulo limanena kuti Yoswa “anatentha mzinda wa Hazori ndi moto.” Mumzinda umenewu munkakhala Akanani. (Yoswa 11:10, 11) Malo amene kale panali mzindawu, akatswiri ofukula zinthu zakale anapezapo akachisi atatu a Akanani omwe anawonongedwa. Anapezanso umboni wosonyeza kuti mzindawo unawotchedwa m’zaka za m’ma 1400 B.C.E. Zimene akatswiriwa anapeza zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena.

● Mzinda winanso wa Akanani umene tikambirane ndi wa Gibiyoni. Mzindawu uli pamtunda wamakilomita pafupifupi 10 kuchokera ku Yerusalemu. Akatswiri anazindikira mzindawo atapeza zigwiriro 30 za mitsuko zolembedwa dzina la mzindawo. Mosiyana ndi anthu a mumzinda wa Hazori, anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Yoswa. Chifukwa cha zimenezi iye anawapatsa ntchito ‘yotunga madzi.’ (Yoswa 9:3-7, 23) N’chifukwa chiyani anapatsidwa ntchito imeneyi? Zimene zimapezeka pa 2 Samueli 2:13 ndi pa Yeremiya 41:12 zimasonyeza kuti mzinda wa Gibiyoni unali wosasowa madzi. Choncho mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, buku lina lofotokoza za m’Baibulo linanena kuti: “Dera la Gibiyoni ndi lapadera kwambiri chifukwa ndi losasowa madzi. Kuli kasupe mmodzi wamkulu komanso ena ang’onoang’ono okwanira 7.”—Archaeological Study Bible, New International Version.

● Anthu ambiri amene anatchulidwa m’Baibulo amatchulidwanso m’mabuku ena ofotokoza mbiri yakale. Ena mwa anthu amenewa ndi mafumu 17 amene anali mbadwa za Abulahamu ndipo analamulira ku Isiraeli kapena ku Yuda. Mafumuwa ndi monga Ahabu, Ahazi, Davide, Hezekiya, Manase ndi Uziya. Umenewu ndi umboni wamphamvu wakuti panalidi mtundu wa Isiraeli ndiponso kuti mtunduwo unalowa n’kukakhala m’dziko la Kanani.

● M’chaka cha 1896, akatswiri ofufuza anapeza mwala wina wotchedwa Merneptah Stele mumzinda wa Thebes ku Egypt. Pamwala umenewu analembapo nkhondo imene Farao anamenya yolimbana ndi dziko la Kanani m’chaka cha 1210 B.C.E. Zimene zinalembedwa pamwalawo ndi umboni woyamba wosachokera m’Baibulo wosonyeza kuti kunalidi mtundu wa Isiraeli.

Limanena Zinthu Mwatsatanetsatane

Monga mmene taonera, Baibulo limafotokoza zinthu mwatsatanetsatane likamanena za anthu, malo komanso zochitika. Tikaona zimene Baibulo limanena n’kuonanso zimene mabuku ena akale amafotokoza, timadziwa kuti zimene Baibulo linalosera zinakwaniritsidwadi. Pa nkhani ya Abulahamu ndi mbewu yake, pali umboni wosonyeza kuti zimene Mulungu analonjeza zinakwaniritsidwa. Mwachitsanzo, mbewu ya Abulahamu inadzakhala mtundu waukulu, kenako iwo anakhala akapolo ku Iguputo ndipo patapita nthawi anakakhala ku Kanani. Zonsezi zikutikumbutsa zimene Petulo ananena. Iye modzichepetsa anati: “Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”—2 Petulo 1:21.

Patapita zaka zambiri kuchokera pamene Aisiraeli anakhazikika m’dziko la Kanani, zinthu zinasintha kwambiri moti Aisiraeli anakumana ndi mavuto aakulu. Nkhani yotsatira idzafotokoza zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitikira mtundu umenewu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 “B.C.E.” ndi chidule cha mawu akuti “Before the Common Era,” kutanthauza “Nyengo Yathu Ino Isanafike.”

^ ndime 5 Poyamba Abulahamu ankatchedwa Abulamu.

^ ndime 11 Werengani 1 Mbiri 1:27-34; 2:1-15; 3:1-24. Pamene Rehobowamu, yemwe anali mwana wa Mfumu Solomo, ankalamulira, mtundu wa Isiraeli unagawanika n’kukhala maufumu awiri, wina unali kumpoto ndipo wina unali kum’mwera. Kuyambira nthawi imeneyo, mtundu wa Isiraeli unkalamuliridwa ndi mafumu awiri pa nthawi imodzi.—1 Mafumu 12:1-24.

[Bokosi patsamba 17]

 “MITUNDU YONSE” IDZAPEZA MADALITSO

Mulungu analonjeza kuti anthu a “mitundu yonse” adzapeza madalitso kudzera mu mbewu ya Abulahamu. (Genesis 22:18) Cholinga chachikulu chimene Mulungu anasankhira mbadwa za Abulahamu kuti zikhale mtundu waukulu chinali chakuti mtunduwu udzatulutse Mesiya amene adzapereke moyo wake kuti apulumutse anthu onse. * Zimenezi zikutanthauza kuti zimene Mulungu analonjeza Abulahamu zimakhudzanso inuyo. Lemba la Yohane 3:16 limanena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 34 Magawo 3 ndi 4 a nkhani zino adzafotokoza maulosi onena za mmene anthu adzadziwire Mesiya.

[Bokosi patsamba 17]

 BAIBULO LIMANENA NDENDENDE NTHAWI YOMWE ZINTHU ZINACHITIKA

Pa lemba la 1 Mafumu 6:1 pali chitsanzo chosonyeza kuti Baibulo limanena ndendende nthawi yomwe zinthu zinachitika. Lembali limanena za nthawi imene Mfumu Solomo inayamba ntchito yomanga kachisi ku Yerusalemu. Limati: “Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Anayamba kuchita zimenezi m’chaka cha 480 [patatha zaka 479] kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi wachiwiri wa Zivi. Ichi chinali chaka chachinayi cha ulamuliro wake monga mfumu ya Isiraeli.”

Baibulo limasonyeza kuti chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomo chinali 1034 B.C.E. Tikawerengetsera chobwerera m’mbuyo, zaka 479 zikutifikitsa m’chaka cha 1513 B.C.E., chaka chomwe Aisiraeli anatuluka mu Iguputo.

[Bokosi patsamba 18]

UMBONI WAKUTI ABULAHAMU ANAKHALAKODI

● Mapale enaake adongo a m’zaka za m’ma 1700 ali ndi mayina a mizinda omwe ndi ofanana ndi mayina a abale ake a Abulahamu. Ina mwa mizindayi ndi Pelegi, Serugi, Nahori, Tera, ndi Harana.—Genesis 11:17-32.

● Palemba la Genesis 11:31 timawerenga kuti Abulahamu ndi banja lake anasamuka kuchoka “mumzinda wa Akasidi wa Uri.” Akatswiri ofufuza zinthu zakale anapeza malo amene kale panali mzinda umenewu, kum’mwera chakumadzulo kwa dziko la Iraq. Baibulo limanenanso kuti bambo ake a Abulahamu, a Tera, anamwalirira ku Harana. N’kutheka kuti panopo dera limeneli lili m’dziko la Turkey. Lembali limanenanso kuti Sara, yemwe anali mkazi wa Abulahamu, anamwalirira ku Heburoni womwe ndi umodzi mwa mizinda yakale kwambiri ya ku Middle East, komwe kumakhalabe anthu mpaka pano.—Genesis 11:32; 23:2.

[Tchati pamasamba 16, 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

 ZAKA ZOKHUDZA MBEWU YA ABULAHAMU KOMANSO ULENDO WA AISIRAELI

Mibadwo inayi ya mbadwa za Abulahamu

Levi

Kohati

Amuramu

Mose

(B.C.E.)

1843 Kumwalira kwa Abulahamu

1728 Yakobo anasamukira ku Iguputo ndi banja lake

1711 Kumwalira kwa Yakobo

1657 Kumwalira kwa Yosefe

1593 Kubadwa kwa Mose

1513 Mose anatsogolera Aisiraeli kuchoka ku Iguputo

1473 Kumwalira kwa Mose. Yoswa anatsogolera Aisiraeli kulowa m’dziko la Kanani

Nthawi ya Oweruza

1117 Samueli anadzoza Sauli kukhala mfumu yoyamba ya Isiraeli

1107 Kubadwa kwa Davide

1070 Davide anakhala mfumu ya Isiraeli

1034 Solomo anayamba ntchito yomanga kachisi

[Chithunzi patsamba 17]

Mwala uwu analembapo mawu akuti “Nyumba ya Davide” ndipo ndi umodzi mwa zinthu zimene zimatchula mafumu omwe anali mbadwa za Abulahamu, amene analamulira ku Isiraeli kapena ku Yuda

Mawu a Chithunzi

© Israel Museum, Jerusalem/The Bridgeman Art Library International