Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chenjerani Ndi Zigawenga za pa Intaneti

Chenjerani Ndi Zigawenga za pa Intaneti

Chenjerani Ndi Zigawenga za pa Intaneti

YEREKEZERANI kuti mukuona gulu la mbava zaluso kwambiri pobera anthu pa Intaneti. Mbavazo zikugwiritsa ntchito mwakuba makompyuta ambirimbiri a anthu ena omwe ali pa Intaneti. Makompyuta omwe mbavazo zikugwiritsa ntchito akutumiza mapulogalamu oopsa ku makompyuta a dziko lina. Kanthawi kochepa chabe, makompyuta a gulu la nkhondo la dzikolo, mabanki komanso makompyuta ena a mabungwe a zachuma akuwonongeka. Makina otengera ndalama kubanki (ATM) komanso mafoni akusiya kugwira ntchito. Ndege zasiya kuuluka ndiponso magetsi m’dziko lonselo athima. Kodi mukuganiza kuti anthu angamve bwanji? Kodi angatani? Kodi inuyo mungatani?

Ena anganene kuti zimenezi sizingachitike. Koma malinga ndi zimene ananena Richard A. Clarke, yemwe anali mkulu wa nthambi ya boma yoona za chitetezo ku America, zinthu zangati zimenezi zikhoza kuchitika. Ndipotu pali umboni wosonyeza kuti uchigawenga wa pa Intaneti * ukuchitikadi. Mwinanso inuyo zimenezi zinakuchitikiranipo.

Koma n’chifukwa chiyani anthu amachita zinthu zoipa chonchi? Kodi zigawengazi zimatani zikafuna kusokoneza makompyuta? Ndiponso, popeza kuti uchigawenga wa pa Intaneti ndi wofala masiku ano, kodi mungatani kuti mudziteteze?

Nkhondo ya pa Intaneti

Anthu amachita zauchigawenga pa Intaneti pa zifukwa zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, zigawenga kapena mayiko ena amasokoneza makompyuta a adani awo n’cholinga choti abe zinthu zawo zachinsinsi. M’chaka cha 2010, wachiwiri kwa nduna ya zachitetezo m’dziko la America, dzina lake William J. Lynn III, ananena kuti “adani” anaba kangapo konse zinthu zambiri zachinsinsi za dziko la America, kuphatikizapo malangizo okhudza kapangidwe ka zida za nkhondo, mapulani a dzikolo okhudza nkhondo, ndiponso zinthu zina za ukazitape.”—Onani bokosi lakuti,  “Zitsanzo Zaposachedwapa za Uchigawenga wa pa Intaneti.”

Zigawenga za pa Intaneti zimagwiritsa ntchito njira ngati zimenezi zikafuna kuba ndalama kapena kukopera zinthu za makampani ndi za anthu wamba. Malipoti akusonyeza kuti mbava zimaba ndalama zambirimbiri chaka chilichonse pogwiritsa ntchito Intaneti.

Zigawenga za pa Intaneti zimagwiritsa ntchito makompyuta ambirimbiri a anthu ena kuti zichite zofuna zawo. M’chaka cha 2009, kampani ina yoona za chitetezo cha pa Intaneti, inalepheretsa gulu la zigawenga zina zomwe zinkagwiritsa ntchito makompyuta pafupifupi 2 miliyoni. Ambiri mwa makompyutawo anali a anthu osati a makampani. Bungwe lina loona za chuma cha mayiko osiyanasiyana (Economic Cooperation and Development) posachedwapa linanena kuti pa makompyuta atatu alionse omwe alumikizidwa pa Intaneti, mbava zimakhala zikusokoneza kapena kugwiritsa ntchito kompyuta imodzi eniake asakudziwa. Nanga bwanji kompyuta yanu? Kodi ndi yotetezeka kapena ena amatha kulowa mosavuta?

Mapulogalamu Owononga Mwachinsinsi

Tayerekezeraninso kuti mukuona zochitika izi: Chigawenga chikutumiza pulogalamu yowononga makompyuta pa Intaneti. Pulogalamuyo ikulowa mu kompyuta yanu ndipo ikusokoneza zinthu zonse zimene zimateteza kompyutayo. Ikufufuzanso zinthu zanu zofunika kwambiri mu kompyutayo. * Pulogalamu yoipawo ikusintha kapena kufufuta zonse zimene zili mu kompyuta mwanu. Ikutumizanso kwa anthu ena maimelo omwe inu simunalembe. Kenako ikutumiza kwa chigawengacho zinthu monga, nambala yanu yachinsinsi yolowera pa kompyuta, zinthu zokhudza akaunti yanu ya kubanki kapena zinthu zina zachinsinsi.

Anthu oipawa amathanso kupusitsa munthu kuti alowetse yekha pulogalamu yoipa mu kompyuta yake. Kodi amachita bwanji zimenezi? Munthu angathe kulowetsa pulogalamu yoipa mu kompyuta yake ngati atatsegula imelo yooneka ngati yabwinobwino, ngati atatsegula adiresi inayake pa kompyuta, ngati atakopera zinthu kapena kuika pulogalamu yaulere mu kompyuta yake. Akhozanso kulowetsa pulogalamu yoipa atalumikiza kachipangizo kotengera zinthu pa kompyuta komwe kali ndi pulogalamu yoipayi. Kuwonjezera pa zimenezi, angalowetsenso pulogalamu yoipa mu kompyuta yake ngati atapita tsamba lolakwika, losayenera Akhristu. Choncho, munthu ayenera kusamala kuti anthu achinyengo asagwiritse ntchito kompyuta yake m’njira zimene tachulazi.

Kodi mungadziwe bwanji ngati mu kompyuta yanu mwalowa pulogalamu yachinyengo? Nthawi zambiri zimavuta kudziwa. Koma mwina mungadziwe ngati kompyuta kapena Intaneti ikuchedwa kutsegula, ngati mapulogalamu ena sakutsegula, ngati pa kompyuta yanu pakumabwera mauthenga oti mulowetse pulogalamu inayake mu kompyuta yanu. Nthawi zinanso kompyuta yanu ingamachite zinthu zina zachilendo. Mukaona zizindikiro ngati zimenezi, muziitana munthu wodziwa bwino za makompyuta kuti aione.

‘Muziganizira Mmene Mukuyendera’

Masiku ano anthu komanso mayiko akugwiritsa ntchito kwambiri makompyuta. Chifukwa cha zimenezi, tiyembekezere kuti uchigawenga wa pa kompyuta uzichitika kawirikawiri. Pozindikira zimenezi, mayiko ambiri akuyesetsa kuika zinthu zoteteza makompyuta awo. Koma mkulu wa dipatimenti ya makompyuta m’bungwe lofufuza milandu la FBI ku America, dzina lake Steven Chabinsky ananena kuti ngakhale maboma akuchita zimenezi, “zigawenga zikhozabe kusokoneza makompyuta ngati zitakhala ndi nthawi yokwanira, ndalama zogwirira ntchitoyi komanso ngati patakhala zinthu zinazake zomwe zigawengazo zikuzifuna kwambiri.”

Ndiye kodi mungatani kuti muteteze kompyuta yanu? Ngakhale kuti n’zosatheka kutetezeratu kompyuta yanu, ndi nzeru kutsatira malangizo amene angathandize kuchepetsa vutoli. (Onani bokosi lakuti “Tetezani Kompyuta Yanu”) Baibulo limati: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Amenewa ndi malangizo abwino kwambiri kuwatsatira mukamagwiritsa ntchito Intaneti.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Anthu amene amachita uchigawenga wa pa Intaneti amasokoneza kapena kuwononga mwadala makompyuta a anthu ena omwe alumikizidwa pa Intaneti. Zigawengazi zimawononga zinthu zofunikira zokhudza mwini kompyutayo kapena mapulogalamu a pa kompyutayo.—U.S. National Research Council.

^ ndime 10 Akuti mu 2011, anthu akuba pa Intaneti ankadziwa mavuto oposa 45,000 okhudza makompyuta, ndipo zimenezi zikanawathandiza kuba mosavuta. Chifukwa chodziwa mavuto amenewa, nthawi zambiri mbava zimatumiza pulogalamu yachinyengo yobera kapena kuwononga zinthu m’makopyuta a anthu, eniake asakudziwa.

[Mawu Otsindika patsamba 26]

Zigawenga za pa Intaneti zimagwiritsa ntchito makompyuta ambirimbiri a anthu ena

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Malinga ndi bungwe la OECD , pa makompyuta atatu alionse omwe alumikizidwa pa Intaneti, mbava zimakhala zikusokoneza kapena kugwiritsa ntchito kompyuta imodzi, eniake asakudziwa

[Bokosi patsamba 27]

 ZITSANZO ZAPOSACHEDWAPA ZA UCHIGAWENGA WA PA INTANETI

Mu 2003: Anthu ena anatumiza pa Intaneti pulogalamu ya pa kompyuta yomwe inasokoneza makompyuta pafupifupi 75,000 m’mphindi 10 zokha. * Pulogalamuyi inachititsa kuti Intaneti izichedwa kwambiri, malo ambiri a pa Intaneti komanso makina otengera ndalama a ATM asiye kugwira ntchito. Zinachititsanso kuti ndege zisiye kuuluka komanso kuti makompyuta ndi zinthu zina zoteteza malo ena opangira mphamvu za nyukiliya zisokonezeke.

Mu 2007: Zigawenga za pa Intaneti zinasokoneza makompyuta a boma, a mabungwe ofalitsa nkhani komanso a mabanki m’dziko la Estonia. Makompyuta ambiri analandira pulogalamuyo kuchokera ku makompyuta a anthu ena amene ankagwiritsidwa ntchito ndi zigawenga za pa Intaneti. Chifukwa cha zimenezi, makompyuta oposa 1 miliyoni m’mayiko 75 ankatumizira makompyuta ena mauthenga achinyengo.

Mu 2010: Pulogalamu ina yotchedwa Stuxnet, inasokoneza makompyuta a malo opangira mphamvu za nyukiliya ku Iran.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Mapulogalamu oipawa amadzichulukitsa okha, n’kufalikira m’makompyuta ambirimbiri amene alumikizidwa pa Intaneti. Pulogalamu iliyonse imakhala ndi dzina lakelake, mwachitsanzo ikhoza kukhala ndi dzina lakuti Slammer.

[Bokosi patsamba 28]

TETEZANI KOMPYUTA YANU

1. Ikani mu kompyuta yanu pulogalamu yoteteza kuti musalowe mavailasi kapena mapulogalamu ena amene angawononge kompyutayo. Muzionetsetsa kuti mapulogalamuwo akugwira ntchito komanso kuti ili ndi zinthu zatsopano zoteteza kompyutayo.

2. Muziganizira kaye musanatsegule tsamba lililonse pa Intaneti kapena imelo iliyonse imene mungalandire ngakhale yochokera kwa anzanu. Muzisamala kwambiri ndi ma imelo ochokera kwa anthu osawadziwa. Ma imelo amenewa amafuna kuti mupereke zinthu zanu zachinsinsi kapena nambala yanu yolowera pa kompyuta.

3. Musamakopere kapena kuika mu kompyuta yanu pulogalamu imene simukudziwa kumene yachokera.

4. Nambala yanu yachinsinsi izikhala ndi zilembo zosachepera 8. Zilembozo zikhoza kukhala manambala ndi zizindikiro zina ndipo muzizisintha pakapita nthawi. Muzigwiritsa ntchito manambala achinsinsi osiyanasiyana pa zinthunso zosiyanasiyana zimene mumachita pa Intaneti.

5. Muzichita bizinezi pa Intaneti ndi makampani odalirika okhaokha, omwe ma adiresi awo amakhala otetezedwa. *

6. Musamapereke zinthu zachinsinsi zokhudza inuyo kapena akaunti yanu ya kubanki mukamagwiritsa ntchito malo apa Intaneti osatetezeka.

7. Mukamaliza kugwiritsa ntchito kompyuta yanu muziithimitsa.

8. Muzionetsetsa kuti zinthu zimene mwazisunga mu kompyuta yanu, mwazisunganso pazinthu monga ma CD.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 36 Ma adiresi a pa Intaneti omwe ndi otetezeka amakhala ndi chizindikiro cha loko komanso adiresi yake imayamba ndi “https://” ndipo “s” amaimira secure, kutanthauza kuti tsambalo ndi lotetezedwa.

[Chithunzi patsamba 28]

Yesetsani kuteteza kompyuta yanu mukamagwiritsa ntchito Intaneti