Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Choonadi Chingatimasule’ Bwanji?

Kodi ‘Choonadi Chingatimasule’ Bwanji?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi ‘Choonadi Chingatimasule’ Bwanji?

ANTHU mamiliyoni ambiri amaona kuti ali pa ufulu, koma kwenikweni sizili choncho. Mwachitsanzo, anthu ambiri amakhala mwamantha chifukwa choopa zamizimu. Ena amaopa anthu akufa ndipo amayesa kuwasangalatsa powapatsa mphatso zamtengo wapatali. Komanso ena amaopa kwambiri imfa chifukwa sadziwa chimene chimachitika munthu akamwalira. Anthu oterewa amakhala ndi nkhawa komanso amawononga ndalama zambiri. Kodi angamasuke ku mavuto amenewa? Inde, ndipo mawu a Yesu Khristu amasonyeza kuti choonadi ndi chimene chingathandize munthu kuti amasuke. Koma kodi choonadi n’chiyani?

Yesu anatipatsa yankho la funso limeneli. Iye anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, . . . mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) “Mawu” a Yesu komanso zimene ankaphunzitsa zimapezeka m’Baibulo.

Ponena kuti “choonadi chidzakumasulani,” kwenikweni Yesu ankatanthauza kumasulidwa ku uchimo ndi imfa. Komabe, kudziwa choonadi cha Mawu a Mulungu kumatimasulanso ku zinthu monga kukhulupirira zamizimu, kuopa akufa komanso kuopa imfa. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

1. Timamasuka ku zikhulupiriro zamizimu. Anthu ena amakhulupirira kuti zinthu zina kapena manambala ena angachititse mphumi. Anthu enanso asanasankhe zochita amapita kaye kwa asing’anga kukaombeza.

Mmene choonadi cha m’Baibulo chimatimasulira: Kalelo atumiki ena a Mulungu anayamba kukhulupirira zamizimu, ndipo anafika polambira “mulungu wa Mwayi” komanso “mulungu wa Zokonzedweratu,” kapena kuti wodziwitsa za m’tsogolo. Kodi Yehova Mulungu ankaona bwanji nkhani imeneyi? Iye anawauza kuti: “Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga.” (Yesaya 65:11, 12) Mulungu ankakhumudwanso anthu akamapita kwa asing’anga kukaombeza kuti adziwe za m’tsogolo. Baibulo limanena kuti: “Aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu . . . ndi wonyansa kwa Yehova.”—Deuteronomo 18:11, 12.

Kukhulupirira zamizimu komanso kupita kwa asing’anga kukaombeza ndi koipa chifukwa ndi “zochita zachinyengo za Mdyerekezi,” yemwe Yesu anamutchula kuti “tate wake wa bodza.” (Aefeso 6:11; Yohane 8:44) Kodi inuyo mungapite kwa munthu wabodza kuti akakupatseni malangizo pa nkhani inayake yofunika? N’zachidziwikire kuti simungatero. Choncho, ndi nzeru kupewa chilichonse chogwirizana ndi “tate wake wa bodza.”

Chinthu chofunika kwambiri kuti tizisankha zinthu mwanzeru ndi kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kudziwa cholinga cha Mulungu. Lemba la Miyambo 2:6 limati: “Yehova amapereka nzeru. Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.”

2. Sitiopanso akufa. Anthu ambiri amakhulupirira kuti “mizimu” ya anthu akufa ingawathandize kapena kuwabweretsera mavuto. Iwo amakhulupirira kuti ayenera kupereka nsembe kuti mizimu imeneyi izisangalala, ndipo amaona kuti ngati sachita zimenezi mizimuyo ikwiya. Chifukwa cha zimenezi, ena amakhalira kupereka nsembe komanso kuchita miyambo yosiyanasiyana yofuna ndalama zambiri, zomwe zimachititsa kuti azivutika ndi ngongole.

Mmene choonadi cha m’Baibulo chimatimasulira. Baibulo limatiuza zolondola pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti akufa “ali m’tulo.” (Yohane 11:11, 14) Kodi iye ankatanthauza chiyani? Yankho la funso limeneli lili pa lemba la Mlaliki 9:5, lomwe limati: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” Akufa amakhala ngati agona tulo tofa nato, moti sadziwa chilichonse. Iwo kulibe, choncho sangachite chilichonse, kaya chabwino kapena choipa.

Komabe anthu ena amanena kuti anakumanapo kapena kulankhula ndi munthu amene anamwalira. Kodi zimenezi n’zotheka? Baibulo limayankha kuti kale kwambiri, angelo ena anapandukira Mulungu. (2 Petulo 2:4) Angelo amenewa amatchedwa ziwanda ndipo amafuna kuti azipusitsa anthu. (1 Timoteyo 4:1) Njira imodzi yomwe amachitira zimenezi n’kunamizira kuti ndi anthu amene anamwalira, ndipo zimenezi zimalimbikitsa bodza lakuti munthu akafa amakakhalabe ndi moyo kwinakwake.

3. Sitiopanso imfa. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, imfa ndi mdani. (1 Akorinto 15:26) Choncho, n’zosadabwitsa kuti palibe amene amafuna kufa. Komabe, sitiyenera kuopa imfa.

Mmene choonadi cha m’Baibulo chimatimasulira: Baibulo limanena zoona zenizeni za mmene akufa alili komanso limasonyeza kuti Mulungu ali ndi cholinga chodzaukitsa akufa. Yesu ananena kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake [a Khristu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

Kodi “adzatuluka” ndi thupi lotani? Zomwe zinachitika Yesu ataukitsa anthu angapo akufa zikusonyeza mmene zidzakhalire akamadzaukitsa akufa m’tsogolo. Munthu aliyense amene Yesu anamuukitsa, anauka ndi thupi lomwe anali nalo asanamwalire. (Maliko 5:35-42; Luka 7:11-17; Yohane 11:43, 44) Zimenezi zikugwirizana ndi mawu akuti “kuuka,” omwe amatanthauza “kuimirira.” Polankhula ndi mtumiki wake Danieli, yemwe anali wokalamba, Mulungu anati: “Udzapuma [kapena kuti udzamwalira]. Koma udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Danieli 12:13) Mawu amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Danieli ndipo anamuthandiza kuti asaope imfa.

Chifukwa china chimene Yesu anabwerera padziko lapansi chinali “kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo,” amene amaphunzitsidwa zinthu zabodza. (Luka 4:18) Zimene Yesu ankaphunzitsa zimapezeka m’Baibulo ndipo anthu akawerenga zimenezi amamasuka. Sitikukayikira kuti inunso mungamasuke mutadziwa choonadi cha m’Baibulo.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

Kodi choonadi cha m’Baibulo chimatimasula bwanji pa zinthu izi?

● Kukhulupirira zamizimu—Yesaya 8:19, 20; 65:11, 12.

● Kuopa akufa—Mlaliki 9:5; Yohane 11:11, 14.

● Kuopa imfa—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Choonadi cha m’Baibulo chimamasula anthu ku zikhulupiriro zamizimu, kuopa akufa komanso kuopa imfa