Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Koma Ndiye Chimphunotu!”

“Koma Ndiye Chimphunotu!”

“Koma Ndiye Chimphunotu!”

ANTHU amakonda kunena mawu amenewa akangoona koyamba anyani amtundu winawake amphuno yaitali kwambiri. * Anyani ena aamuna amakhala ndi mphuno yaitali masentimita 18, yomwe ndi pafupifupi 25 peresenti ya kutalika kwa thupi lake lonse. Amakhalanso ndi mphuno yaitali kwambiri yoti imatchinga pakamwa ndipo imalendewera mpaka kuchibwano moti akamadya amafunika kukankha kaye mphunoyo. Akanakhala munthu ndiye kuti mphuno yake bwenzi ikulendewera mpaka kufika pachifuwa.

Kodi kutalika kwa mphunozi kumathandiza bwanji anyani amphongo? * Anthu amanena zinthu zosiyanasiyana. Ena amati mwina mphunoyi imathandiza kuti nyaniyo asamatenthedwe kwambiri kapena imathandiza kuti mawu ake azimveka patali. Ena amanena kuti anyani aamuna amagwiritsa ntchito mphunoyi poopsezera mphongo zinzawo. Mwina zimenezi n’zoona chifukwa nyani wamwamuna akalusa kapena akasangalala, mphuno yake imafufuma komanso imafiira. Ena amanenanso kuti mphunoyi imathandiza kuti anyani aamuna azikopa anyani aakazi. Zimenezi zikusonyeza kuti mphunoyi imagwira ntchito zosiyanasiyana ndipo n’kutheka kuti zina sitizidziwa n’komwe.

Alinso ndi Mimba Zikuluzikulu

Anyani onse, aamuna ndi aakazi omwe, ali ndi mimba zikuluzikulu moti zimene nyani mmodzi amadya zikhoza kukwana 25 peresenti ya kulemera kwa thupi lake lonse. Chifukwa cha zimenezi, anyani onse aamuna ndi aakazi amangooneka ngati ali ndi bere. N’chifukwa chiyani anyaniwa amakhala ndi mimba zikuluzikulu chonchi?

Nthawi zonse chifu cha anyaniwa chimakhala ndi madzi enaake osakanikirana ndi zakudya komanso mabakiteriya omwe amathandiza kugaya chakudya komanso kuchotsa zinthu zapoizoni zomwe zimapezeka m’zakudya zina. Chifukwa cha zimenezi anyaniwa amatha kudya masamba, zipatso zina zowawa, mtedza, nyemba ndi zomera zina zimene anyani ena sangakwanitse kudya.

Komabe, zimenezi zili ndi mavuto ake chifukwa anyaniwa amafunika kupewa kudya zipatso zotsekemera kwambiri, zomwe sizichedwa kusasa. Ngati nyani atadya zakudya zimenezi angafe chifukwa mimba yake ingafufume, n’kuphulika.

Chifukwa chakuti zakudya zimene anyaniwa amadya zimakhala ndi zinthu zambiri zofunika kugayidwa bwinobwino, anyaniwa amafunika kukhala nthawi yaitali akupuma kuti chakudyacho chigayike. Choncho, akadya chakudya cha m’mawa amagona kwa maola angapo, nthawi zina kwa maola ambiri asanadyenso chakudya china.

Amakonda Kukhala M’magulu

Nthawi zambiri anyaniwa amakonda kukhala m’magulu akamadya kapena akamapuma. Kawirikawiri nyani wamwamuna amayang’anira gulu la anyani aakazi, mwina akazi 8 ndi ana awo. Nyani wamwamuna akangokula amamuthamangitsa kuti azikadzisamalira yekha. Ana aamunawo akathamangitsidwa amakapezana ndi anzawo n’kupanga gulu lawo lomwe limayang’aniridwa ndi nyani wamkulu m’modzi kapena awiri. Munthu wosawadziwa akaona gulu la anyani amenewa amaona ngati palinso anyani aakazi.

Anyaniwa amachita zinthu zochititsa chidwi kwambiri chifukwa magulu awo akakumana kumtsinje amasakanikirana n’kumacheza. Nthawi zina anyani aamuna amachita zinthu zosonyeza mphamvu akazindikira kuti nyani wamwamuna wa gulu linalo akufuna akazi a m’gulu lake. Kawirikawiri m’tsogoleri wagulu, yemwe nthawi zina amalemera makilogalamu 20, amaima ndi miyendo yonse inayi atatsegula kukamwa n’kumayang’anitsitsa moopseza mdani wakeyo. Buku lina linanena kuti: “Nyani wamwamunayo akaona kuti zimene akuchitazo sizikuthandiza, amayamba kudumphira m’mitengo kwinaku akupanga phokoso loopseza. Nthawi zambiri amadumphira nthambi zouma zomwe zimathyoka n’kumawonjezera phokoso lija.” (Proboscis Monkeys of Borneo) Nthawi zina anyaniwa amatha kuchita ndewu koma si kawirikawiri.

Bukuli linanenanso kuti: “Sikuti anyaniwa amangochititsa chidwi kuwaona, koma amapanganso phokoso lodabwitsa.” Mwachitsanzo, anyani amenewa amalira mosiyanasiyana makamaka akakumana m’mbali mwa mtsinje madzulo. Pa nthawi imeneyi anyani amene ali ndi ana amatanganidwa ndi kudyetsa komanso kupesa ana awo. Kunja kukayamba kuda anyaniwa amakwera n’kugona m’mitengo italiitali kumtsinje komweko.

Ali ndi Mapazi Ngati a Bakha

Kuwonjezera pa kukhala ndi mphuno yaitali, anyaniwa ali ndi mapazi ngati a bakha. Mapazi amenewa amawathandiza kusambira komanso kuyenda mosavuta m’madera ambiri momwe mitengo imamera m’madzi. Nthawi zambiri m’malo amenewa mumakhalanso ng’ona. Koma kodi anyaniwa amatani kuti asadyedwe ndi ng’onazo?

Zina zimene amachita ndi zoti amalowa m’madzi mwakachetechete n’kumasambira atandandalikana mumzere umodzi ndipo amaonetsetsa kuti posambirapo asavundule madzi kwambiri. Koma mtsinje ukakhala kuti si wotambalala, anyaniwa amapeza nzeru ina. Amakwera mumtengo wautali n’kudumpha kuchoka panthambi, mwina pa mtunda wa mamita 9, n’kugwera m’madzi. Akatero amasambira mwamsangamsanga kufika tsidya lina la mtsinjewo. Anyaniwa amachitanso zimenezi ngakhale atanyamula ana. Nthawi zina gulu lonse la anyani limadumphira m’madzimo nthawi imodzi n’kusambira mofulumira kukafika tsidya lina. Komabe si kuti mdani wamkulu wa anyaniwa ndi ng’ona.

Anyaniwa Atsala Pang’ono Kutha

Anyaniwa ali m’gulu la nyama zimene zatsala pang’ono kutha moti panopo angotsala ochepa kwambiri. Chiwerengero cha anyaniwa chikupitirira kuchepa makamaka chifukwa cha anthu. Anthu amaotcha tchire, kudula mitengo, kuyenda mwachisawawa m’madera amene mumakhala anyaniwa komanso kudula kwambiri mitengo ya mgwalangwa pofuna mafuta. Vuto linanso ndi ulenje. Anthu ena amapha anyaniwa pongofuna kusangalala basi. Ndipo ena amapha anyaniwa kuti akachite ndiwo kapena mankhwala. Zimakhala zosavuta kuti anyaniwa aphedwe ndi anthu osaka chifukwa nthawi zambiri amakhala akugona m’mitengo mphepete mwa mtsinje. M’dera lina, limene alenje amapita kawirikawiri ndi maboti awo, chiwerengero cha anyaniwa chinatsika ndi 50 peresenti m’zaka zisanu zokha.

Anthu osamalira nyama akuyesetsa kuphunzitsa anthu za kuipa kopha anyaniwa ndipo boma la Borneo linakhazikitsa lamulo loletsa kupha anyani amenewa. Kodi zimenezi zithandiza? Mwina, koma zidzaoneka kutsogoloku. Kunena zoona, anyaniwa akadzatheratu, zidzakhala zomvetsa chisoni chifukwa anyaniwa ndi osangalatsa komanso ochititsa chidwi kuwaona. Komanso kawirikawiri anyaniwa sachedwa kufa munthu akawatenga kuti azikawaweta.

Anyani a mphuno yochititsa chidwi amenewa ali m’gulu la nyama zambirimbiri zimene tsogolo lawo ndi lokayikitsa. Mitundu ina yambirimbiri ya nyama inatheratu. Komabe, Mulungu ali ndi cholinga chodzakonzanso dzikoli, kuchotsa anthu ankhanza komanso kuphunzitsa anthu mmene angasamalire dziko kuphatikizapo nyama zakutchire. (Miyambo 2:21, 22) Yehova Mulungu analonjeza kuti: “Sizidzavulazana kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera, chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”—Yesaya 11:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Anyaniwa amapezeka pachilumba cha Borneo, chomwe chili panyanja ya Pacific. Anthu ambiri kumeneko amawatchula kuti orang belanda, kapena “munthu wa ku Netherlands.”

^ ndime 3 Anyani aakazi nawonso amakhala ndi mphuno zazitali koma siziposa za anyani aamuna.

[Chithunzi patsamba 12]

Anyaniwa amakhala ndi mphuno komanso mimba zikuluzikulu

[Mawu a Chithunzi]

© Peter Lilja/age fotostock

[Chithunzi patsamba 13]

Mphuno ya nyani wamwamuna imakhala yaikulu moti amachita kuikankhira pambali akafuna kudya

[Mawu a Chithunzi]

© Juniors Bildarchiv/Alamy

[Chithunzi patsamba 14]

Anyaniwa amakonda kukhala m’magulu akamadya kapena kupuma

[Mawu a Chithunzi]

© Peter Lilja/age fotostock