Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandimvetsa?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandimvetsa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandimvetsa?

YEREKEZERANI KUTI MUKUONA ZOCHITIKA IZI:

Ndi Lachisanu madzulo ndipo nthawi ndi 2 koloko. James, yemwe ndi wazaka 17, akutuluka m’nyumba ndipo akutsanzika makolo ake kuti: “Tionanatu.” Iye akuganiza kuti makolo akewo samufunsa funso limene amakonda kumufunsa akamachoka.

Koma akanadziwa, sakanaganiza zimenezo.

Mayi ake akumufunsa kuti: “Kodi ubwerako nthawi yanji?”

James akuima, kenako akuyankha kuti: “Aaa, musadandaule za ine, ndibwera mochedwa.” Kenako akutsegula chitseko mofulumira kuti atuluke, koma bambo ake akumuitana kuti: “Iwe, taima pompo.”

James akuima ndipo bambo ake akumuuza ndi mawu a mphamvu akuti: “Paja lamulo la pakhomo pano ukulidziwa eti? Isafike 6 koloko uli koyenda, tikumvana?”

James akuyankha monyinyirika kuti: “Koma bambo, mukudziwa kuti zimachititsa manyazi ukamauza anzako kuti makolo ako amafuna kuti uzifika panyumba mwansanga?”

Bambo akewo sakusintha maganizo ndipo akumuuza mwamphamvu kuti: “Ndati isafike 6 koloko uli koyenda, palibe zokambirana.”

MWINA zoterezi zinakuchitikiranipo. Mwina munasemphanapo maganizo ndi makolo anu pa nkhani ya nthawi yofikira panyumba, nyimbo zimene mumamvera, anthu ocheza nawo komanso zimene mumavala. Mwina makolo anu anakhazikitsa malamulo okhwima kwambiri pa nkhani zimenezi ndipo safuna kuti aphwanyidwe. Mwachitsanzo tamvani zimene achinyamata ena ananena:

Mayi anga atakwatiwa ndi bambo anga ondipeza, bambowo anayamba kundiletsa kumvera nyimbo zimene ndinkazikonda kwambiri moti ananditayitsa ma CD anga onse.”—Anatero Brandon. *

Mayi anga amandinena kuti sindikonda kucheza ndi anthu. Koma nthawi zina ndikawauza kuti ndikufuna kukacheza ndi winawake amandiletsa, akuti chifukwa choti samudziwa. Zimenezi zimandipweteketsa mtima kwambiri.”—Anatero Carol.

Bambo anga komanso mayi anga ondipeza amafuna kuti ndizivala zimatisheti zikuluzikulu ndipo siketi iliyonse imene ndingavale, bambo angawo amandiuza kuti ndikavule chifukwa chakuti ndiyaifupi.”—Anatero Serena.

Ndiyeno kodi mungatani ngati inuyo simugwirizana ndi makolo anu pa nkhani ngati zimenezi? Mungachite bwino kwambiri kukambirana nawo. Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Joanne ananena kuti: “Ndimaona kuti nthawi zonse makolo anga safuna kumva zimene ndikunena.” Mtsikana winanso wazaka 15, dzina lake Amy, ananena kuti: “Ndikaona kuti makolo anga sakundimvetsa ndimangokhala phee.”

Koma sibwino kukhumudwa mwachangu chifukwa mwina makolo anuwo akufunitsitsa kukumvetserani.

Taganizirani izi: Mulungu amamvetsera anthu akamamudandaulira. Mwachitsanzo, Yehova anamvetsera pamene Mose anamupempha kuti akhululukire Aisiraeli.—Ekisodo 32:7-14; Deuteronomo 9:14, 19.

Nthawi zina mungamaone ngati makolo anu amalephera kukumvetsani ngati mmene Mulungu amachitira. Koma dziwani kuti zimene Mose ankadandaulira Yehova kuti asawononge mtundu wonse wa anthu, n’zosiyana kwambiri ndi zimene inuyo mungadandaulire bambo kapena mayi anu kuti azikulolani kufika mochedwa panyumba. Komabe, pali mfundo yofanana m’zochitika ziwirizi. Mfundo yake ndi yakuti:

Ngati pali chifukwa chomveka choti mudandaulire kwa anthu amene ali ndi udindo, mwachitsanzo makolo anu, iwo angakhale ofunitsitsa kukumvetserani.

Zimenezi zingatheke pokhapokha ngati mwapereka dandaulo lanulo moyenerera ndipo njira zotsatirazi zikusonyeza mmene mungachitire zimenezi.

1. Dziwani pamene pagona vuto. Lembani m’munsimu nkhani imene inuyo ndi makolo simukugwirizana.

․․․․․

2. Dziwani mmene mukumvera. Lembani m’munsimu mawu ofotokoza mmene mumamvera pa nkhani imene simugwirizana ndi makolo anu. Mwachitsanzo, mungalembe kuti zimakupwetekani mumtima, mumakhumudwa, mumachita manyazi kapena mumaona kuti makolo anu sakukhulupirirani. (Chitsanzo: Chochitika chimene tachifotokoza kumayambiriro kwa nkhani ino chikusonyeza kuti James amachita manyazi akamauza anzake nthawi imene makolo ake amafuna kuti azifikira pakhomo.)

․․․․․

3. Dziyerekezereni kuti ndinu kholo. Yerekezerani kuti ndinu kholo ndipo muli ndi mwana wachinyamata yemwe sakugwirizana nanu pa nkhani imene inuyo mwailemba pamwambapa. Mukanakhala kuti ndinu kholo, kodi n’chiyani chimene chikanakuchititsani kuti muzimudera nkhawa kwambiri mwana wanu? (Chitsanzo: M’chochitika cha kumayambiriro chija, n’kutheka kuti makolo a James amamudera nkhawa kuti akhoza kukumana ndi mavuto ena ake ngati atabwera mochedwa.)

․․․․․

4. Unikaninso bwino nkhaniyo. Yesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi kutsatira zimene makolo anu akunena pa nkhaniyi kungakuthandizeni bwanji?

․․․․․

Kodi mungatani kuti muchepetseko nkhawa zimene makolo anu alinazo pa nkhaniyi?

․․․․․

5. Kambiranani nkhaniyo ndi makolo anu ndipo yesani kupeza njira zothetsera vutolo. Mukamatsatira njira zimene tazifotokoza pamwambapa komanso kutsatira malangizo amene ali m’kabokosi ka “Malangizo Othandiza Kuti Muzilankhulana Bwino,” mudzaona kuti makolo anu ayamba kukumvetsetsani. Mtsikana wina, dzina lake Kellie, amagwirizana ndi makolo ake. Iye ananena kuti: “Kukangana ndi makolo sikuthandiza chilichonse ndipo ngakhale utayesetsa bwanji, kukangana nawo sikungawachititse kusintha maganizo. Tikakhala kuti sitikugwirizana pa nkhani inayake ndimaona kuti njira yabwino ndikukambirana nawo. Kuchita zimenezi kumachititsa kuti makolo anga afewetseko zinthu zina komanso kuti ineyo ndisamangoumirira maganizo anga. Zimenezi zimathandiza kuti pamapeto pake tigwirizane.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Tasintha mayina ena

[Bokosi patsamba 20]

MALANGIZO OTHANDIZA KUTI MUZILANKHULANA BWINO

“Kumvetsera n’kofunika kwambiri kusiyana ndi kumangolalata. Ngati mumamvetsera makolo anu akamalankhula komanso kumvetsa mfundo imene akufotokoza, iwonso angamachite chimodzimodzi.”—Anatero Rianne.

Werengani Afilipi 2:3, 4.

“Musamayankhe makolo anu mwamwano. Ineyo ndinachitapo zimenezi kambirimbiri koma kenako ndinazindikira kuti ndikanapewa kukangana ndi makolo anga (komanso chilango chimene anandipatsa) ndikanakhala kuti sindinkawayankha mwamwano.”—Anatero Danielle.

Werengani Miyambo 17:27; 21:23.

“Muzidikira kaye mpaka nonse mitima yanu ikhale pansi komanso muziyambitsa nkhaniyo pamene mukudziwa kuti makolo anu angafune kuti mukambirane.”—Anatero Collette.

Werengani Miyambo 25:11.

“Makolo anu amafuna kudziwa kuti mumawalemekeza komanso kuti mukumvetsera zimene akunena. Choncho, musanawauze maganizo anu, atsimikizireni kuti mwamva zimene anena.”—Anatero Emily.

Werengani Miyambo 23:22; Yakobo 1:19.

[Bokosi patsamba 20]

DZIWANI IZI

Sikuti muyenera kumakambirana nkhani iliyonse imene simukugwirizana ndi makolo anu. Nthawi zina mungafunike kutsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Lankhulani mumtima mwanu, . . . ndipo mukhale chete.” (Salimo 4:4) Mtsikana wina, dzina lake Beatrice anati: “Nthawi zina ndikaona kuti nkhani yake ndi yaing’ono ndimangoisiya.”

[Bokosi patsamba 21]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi munkathetsa bwanji nkhani imene simunkagwirizana ndi makolo anu? Zitachitika kuti mwakhalanso wachinyamata, kodi pali zinthu zimene simungafune kuzibwereza? Ngati zilipo ndi zinthu ziti?

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 21]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Wyndia​—Ndimayesetsa kuganiza kaye ndisanalankhule. Choyamba ndimaganizira mmene makolo anga akuonera nkhaniyo ndipo ndimapemphera kaye ndisananene maganizo anga. Ndikazindikira kuti zimene ndikufuna kunenazo zikhoza kuyambitsa mkangano, ndimayesetsa kuti ndisalankhule chilichonse mpaka pamene mtima wanga wakhala m’malo.

Ross​—Ndikaona kuti ndatsala pang’ono kupsa mtima, ndimayesetsa kudzigwira. Sindifuna kuti ndikhale wokhumudwa tsiku lonse ndi nkhani yomwe ndikanatha kuipewa. Zimenezi zandithandiza kuti ndisamakwiye kwambiri poyerekeza ndi pamene ndinali mwana.

Ramona​—Nthawi zonse ndimaona kuti ndi nzeru kumvetsera zimene makolo anga akunena. Ndipotu nthawi zina zimapezeka kuti zimene iwo akunena n’zosasiyana kwenikweni ndi zimene ndikufuna, ndipo zikatero sitikangananso.