Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tingatani Kuti Tizichitira Ena Zachilungamo?

Tingatani Kuti Tizichitira Ena Zachilungamo?

Tingatani Kuti Tizichitira Ena Zachilungamo?

MLENGI wathu amafuna kuti tizisangalala, tizikhala ndi mtendere wamumtima komanso tisamasokoneze mtendere wa anthu ena. Iye amafuna kuti ‘tizichita chilungamo komanso tikhale okoma mtima.’ (Mika 6:8) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kukhala ndi makhalidwe amene angathandize kuti tizichitira ena zachilungamo ndipo Baibulo lingatithandize pa nkhaniyi.

KUTHANA NDI MTIMA WADYERA. Njira yabwino kwambiri yothanirana ndi mtima wadyera ndi kukhala ndi chikondi chenicheni, osati kungokonda anthu ndi pakamwa. Munthu amene ali ndi chikondi choterechi amalolera kuvutika n’cholinga choti athandize ena. Lemba la 1 Akorinto 13:4, 5 limati: “Chikondi . . . n’chokoma mtima. Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.” Munthu wachikondi choterechi sikuti amangokonda abale ake okha kapena anzake okha. Yesu anafunsa kuti: “Mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani?” Iye anafotokoza kuti ngakhale anthu amene salambira Mulungu amakonda anthu okhawo amene amawakonda.—Mateyu 5:46.

KUTHANA NDI TSANKHO. Lemba la Machitidwe 10:34, 35 limati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” Mulungu saweruza anthu potengera mtundu wawo, chuma chawo kapena chifukwa chakuti ndi aamuna kapena aakazi. Kwa Mulungu, “palibe Myuda kapena Mgiriki, palibe kapolo kapena mfulu, palibenso mwamuna kapena mkazi.” (Agalatiya 3:28) Tikamatsanzira Mulungu timapewa kuchita zinthu mwatsankho. Taganizirani zimene zinachitikira Dorothy, yemwe amakhala ku United States.

Dorothy anakhumudwa kwambiri ndi tsankho moti anaganiza zoti alowe m’gulu la anthu ogalukira boma, omwe cholinga chawo chinali kuthandiza anthu akuda amene ankaponderezedwa. Koma tsiku lina anapita ku misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo anachita chidwi kuona kuti azungu ndi anthu akuda anamulandira ndi manja awiri. Pasanapite nthawi iye anazindikira kuti ndi Mulungu yekha amene angathe kusintha mitima ya anthu. Poyamba iye anali “wokonzeka kupha mzungu aliyense pofuna kuti zinthu zisinthe.” Koma anakhudzidwa mtima kwambiri ataona mmene azungu a Mboni za Yehova ankamusonyezera chikondi, moti anasintha maganizo.

KUTHANA NDI MAKHALIDWE OIPA. Otsatira ena a Yesu asanalowe Chikhristu anali zidakwa, olanda ndiponso olalata. Koma mothandizidwa ndi Mulungu, anasiya makhalidwe oipawa n’kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi ndi chifundo. (1 Akorinto 5:11; 6:9-11; Agalatiya 5:22) Masiku anonso, anthu mamiliyoni ambiri anasiya makhalidwe oipa chifukwa anayamba kulambira Mulungu. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi Firuddin, yemwe amakhala ku Azerbaijan.

Firuddin anakulira kumalo osungira ana amasiye ndipo ankakonda kumenyana ndi anzake. Atakula, ankagwira ntchito yophunzitsa anyamata kamenyedwe ka ndewu. Iye anati: “Ndinali munthu wamwano, wankhanza komanso ndinkapanga zachiwawa. Nditakwatira ndinkachitira nkhanza mkazi wanga Zakhara. Mwachitsanzo pa nthawi yachakudya, iye akaiwala chinachake ngakhale kamtengo kotokosera m’mano, ndinkamumenya. Ndipo tikamayenda, mwamuna wina n’kumayang’anitsitsa mkazi wangayo, ndinkam’menya munthuyo pomwepo.”

Tsiku lina, Firuddin anakhudzidwa mtima kwambiri ataphunzira kuti Yesu anapempha Mulungu kuti akhululukire asilikali amene anam’pachika. (Luka 23:34) Iye atadziwa mfundo imeneyi, anaganiza kuti, ‘Mwana wa Mulungu yekha ndi amene akanatha kuchita zimenezi.’ Kuyambira nthawi imeneyi, Firuddin ankafunitsitsa kudziwa Mulungu. Iye sanazengereze a Mboni za Yehova atamupempha kuti ayambe kumuphunzitsa Baibulo kwaulere. Pasanapite nthawi, khalidwe lake linayamba kusintha. Anayamba kuchita zinthu mwachifundo moti mkazi wake nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Panopa Firuddin ndi mkazi wake Zakhara akutumikira Mulungu mogwirizana.

N’zoona kuti kusintha kwa munthu mmodzi sikungachititse kuti zinthu zopanda chilungamo zitheretu padzikoli. Komatu, dziwani kuti Mulungu akufuna kuti chilungamo chidzakhale padziko lonse. Izi zidzatheka chifukwa iye ali ndi mphamvu yochitira zimenezi. Komanso kumbukirani kuti pa lemba la 2 Timoteyo 3:1-4, limene taligwira mawu kumayambiriro kwa nkhani yapita ija, tinaona kuti Baibulo linanena mosapita m’mbali kuti anthu ambiri adzakhala ndi makhalidwe oipa. Ulosi umene uja ukukwaniritsidwa ndendende, ngati mmene zakhalira ndi maulosi ena a m’Baibulo. Choncho, tikamanena kuti Mulungu watsala pang’ono kuthetsa zinthu zopanda chilungamo, sikuti tikunena zongolota. Iye adzakwaniritsadi kuchita zimenezi. Koma kodi adzazikwaniritsa bwanji?

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

HEIDE ANKAFUNITSITSA CHILUNGAMO

Mayi wina dzina lake Heide, yemwe amakhala ku United States, ananena kuti: “Ndinkakhumudwa kwambiri ndi kusankhana mitundu, nkhondo, umphawi ndi zinthu zina zopanda chilungamo ndipo ndinkafunitsitsa njira yothetsera zimenezi. Ndinalowa m’gulu lomenyera ufulu wa anthu kenako ndinayamba ndale, koma zonsezi sizinathetse mavuto amenewa.

“Ndinkaona kuti zinthu ziyenera kusintha mwachangu, choncho ndinalowanso m’gulu lina la achinyamata ndipo ndinkakhulupirira kuti gululi lingasinthe zinthu. Koma zimenezinso sizinathetse mavutowo. Ndinaona kuti achinyamata ambiri a m’gululi analibe chidwi chofuna kusintha zinthu. M’malomwake ankakonda zachiwerewere, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso nyimbo zolimbikitsa chiwawa. Zimenezi zinangondikhumudwitsanso kwambiri. Kenako ndinakumana ndi mayi wina wa Mboni za Yehova amene anandionetsa m’Baibulo zimene Mulungu adzachite pofuna kusintha zinthu. Mwachitsanzo, anandionetsa lemba la Chivumbulutso 21:3, 4, lomwe limafotokoza kuti Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwa anthu ndipo adzathetsa imfa, kulira, komanso zopweteka zomwe kawirikawiri zimabwera chifukwa cha kupanda chilungamo. Komabe ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma zimenezi zidzathekadi?’

“Ndinayamba kukhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi nditawerenga malemba amene amafotokoza za mphamvu komanso chikondi chimene Mulungu ali nacho, ndiponso nditaona mmene a Mboni za Yehova anandisonyezera chikondi. Panopa ndikuyembekezera mwachidwi kuti ndidzaone zimene Mulungu analonjeza zikukwaniritsidwa.”

[Chithunzi patsamba 6]

Tikamatsanzira chikondi cha Mulungu timapewa kuchita zinthu mwatsankho

[Chithunzi patsamba 6]

Firuddin ndi mkazi wake, Zakhara