Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimapweteka Ukamachitiridwa Zopanda Chilungamo

Zimapweteka Ukamachitiridwa Zopanda Chilungamo

Zimapweteka Ukamachitiridwa Zopanda Chilungamo

M’CHAKA cha 2010, Michael wa ku Texas, m’dziko la United States, anatulutsidwa m’ndende atakhalamo zaka 27 pa mlandu womunamizira kuti anagwiririra mkazi. Iye anatulutsidwa pambuyo poti madokotala ayeza DNA yake n’kutsimikizira kuti sanachitedi zimenezo. Pa nthawi imene iye anamangidwa n’kuti kulibe njira zoyezera DNA. M’kupita kwa nthawi, amene anapalamula mlanduwo anapezeka koma zinali zosatheka kuwazenga mlandu chifukwa malamulo a kwawoko salola kuti munthu azengedwe mlandu ngati papita nthawi yaitali chipalamulireni.

Anthu ambiri amene amapalamula milandu ikuluikulu salandira chilango. Mwachitsanzo, magazini ina inanena kuti ku Britain, “pa zaka 10 zapitazi, chiwerengero cha milandu ya anthu amene anapha anzawo koma osagwidwa kapena kulandira chilango chawonjezereka. Zimenezi zachititsa anthu kuganiza kuti apolisi komanso makhoti akulephera ntchito yawo.”—The Telegraph.

Mu August 2011, apolisi ku Britain anali kalikiliki kulimbana ndi anthu omwe ankachita zipolowe ku Birmingham, Liverpool, London, ndi m’madera ena. Anthuwo ankayatsa katundu, kuswa mawindo a masitolo komanso kuba zinthu. Zimenezi zinawonongetsa nyumba, magalimoto ndiponso mabizinezi, zomwe zinachititsa kuti anthu ambiri asowe mtengo wogwira. Kodi n’chifukwa chiyani anthuwa anachita zimenezi? Ambiri ankangofuna chuma basi. Koma zikuoneka kuti ena anachita zimenezi chifukwa chotopa ndi zinthu zopanda chilungamo. Ponena za zipolowezi, ena anati anthu amene ankapanga zipolowewo ndi achinyamata amene amaona kuti boma likuwapondereza. Achinyamatawa ndi ochokera m’madera okhala anthu osauka ndipo amaona kuti alibe tsogolo.

M’Baibulo, Yobu ananena kuti: “Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.” (Yobu 19:7) Masiku anonso, anthu ambiri akuvutika chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo, koma nthawi zambiri palibe munthu amene amamva kulira kwawo. Koma kodi anthu ali ndi mphamvu zothetsa zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitikazi? Kapena kodi anthu amene amakhulupirira kuti zinthu zopanda chilungamo zidzatha, sadziwa chimene akunena? Kuti tidziwe zolondola, choyamba tiyenera kudziwa chimene chimachititsa anthu kuchitira ena zinthu zopanda chilungamo.