Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Ku New York City akhazikitsa lamulo loletsa kusuta fodya kunyanja, m’mapaki komanso m’malo amene mumakonda kukhala anthu ambiri. Aliyense wophwanya lamuloli azilipira madola 50. Akuluakulu a boma akukhulupirira kuti anthu azitsatira lamuloli chifukwa azifuna “kupulumutsa ndalama zawo.”—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.

“Amayi ambiri apakati ku India akumachotsa mimba akadziwa kuti abereka mwana wamkazi. Nthawi zambiri zimenezi zikumachitika ngati mwana woyamba amene mayiyo anabereka ndi wamkazi.” Mu 1990, pa ana 1,000 alionse aamuna amene ankabadwa m’mabanja omwe mwana wawo woyamba ndi wamkazi, pankabadwa ana aakazi 906. Koma mu 2005, pa ana 1,000 alionse aamuna amene ankabadwa, pankabadwa ana aakazi 836.—THE LANCET, BRITAIN.

Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti mphamvu zimene zimatulutsidwa ndi zinthu monga mafoni a m’manja “zikhoza kuyambitsa matenda a khansa.”—INTERNATIONAL AGENCY FOR RESEARCH ON CANCER, FRANCE.

Bungwe la United Nations likukondwerera kuti lakwanitsa kuthetsa matenda enaake oopsa kwambiri a ng’ombe. Imeneyi ndi “nthenda yoyamba ya ziweto imene anthu akwanitsa kuithetsa . . . koma ndi yachiwiri kuthetsedwa chifukwa nthenda yoyamba inali nthomba imene imagwira anthu.”—FOOD AND AGRICULTURE ORGANIZATION OF THE UNITED NATIONS, ITALY.

Buku Latsopano la Malamulo

Nyuzipepala ya New York Times inalemba nkhani yamutu wakuti: “Buku la Malamulo Othandiza Pangozi ku New York.” Ponena za bukuli, nyuzipepalayi inati bukuli latulutsidwa kuti lizithandiza oweruza milandu komanso maloya kudziwa zimene angadzachite ngati “zigawenga zitadzachitanso chiwembu mumzindamo kapena ngati mutadzachitika zinthu zoopsa monga kuwonongeka kwa madzi kapena mpweya chifukwa cha mankhwala apoizoni kapena ngati mumzindawo mutagwa mliri.” Bukuli linafalitsidwa ndi bungwe loona za makhoti ku New York ndipo lili ndi malangizo a mmene makhoti angadzagwiritsire ntchito malamulo amene alipo panopa pa nkhani monga kulekanitsa anthu amene akudwala matenda opatsirana, kusamutsa anthu onse mumzinda, kukafufuza m’nyumba ya munthu popanda chilolezo chake, kupha nyama zimene zili ndi matenda komanso kusankha kusiya kugwiritsa ntchito lamulo linalake.

Zimene Zimakhala Mkati mwa Pilo

Dokotala wina wa pachipatala cha St. Barts ku London, dzina lake Art Tucker, anati: “Ngakhale kuti mapilo amaoneka okongola kunja, mkati mwake mumakhala zinthu zonyansa.” Nyuzipepala ya The Times ya ku London, yomwe inafalitsa zimene dokotalayu anafufuza, inanena kuti, mapilo akagwiritsidwa ntchito kwa zaka ziwiri, zinthu zambiri zimene zimakhala mkati mwake ndi “tizilombo tamoyo komanso takufa, ndowe za tizilomboti, litsiro komanso mabakiteriya.” Tizilombo ting’onoting’ono komanso majeremusi zimakonda kukhala m’mapilo. Kodi mungathetse bwanji vutoli? Nyuzipepala ija inanenanso kuti “tizilomboti timafa mukayanika mapilowo padzuwa ndipo njira imeneyi ndi yothandiza ngakhale kuti ndi yachikale.” Tizilomboti sitifa ndi sopo, pokhapokha ngati mwachapa mapilowa m’madzi otentha kwambiri.