Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

2. Muziyesetsa Kukhala Aukhondo

2. Muziyesetsa Kukhala Aukhondo

2. Muziyesetsa Kukhala Aukhondo

KUTI dokotala wochita opaleshoni ateteze odwala ake ku matenda, amasamba m’manja nthawi zonse, amawiritsa zipangizo zake m’madzi otentha komanso amaonetsetsa kuti m’chipinda chimene akuchitiramo opaleshoni ndi moyera. Mofanana ndi zimenezi, inunso mungateteze anthu am’banja lanu ku matenda ngati mumaonetsetsa kuti mukudzisamalira bwino, mumasamalira bwino chakudya chanu komanso ngati m’khitchini mwanu mumakhala moyera.

Muzisamba m’manja.

Bungwe lina loona za umoyo ku Canada linanena kuti: “Matenda 80 pa 100 aliwonse opatsirana, monga chimfine, amafala chifukwa choti anthu sakonda kusamba m’manja.” Choncho muzionetsetsa kuti mwasamba m’manja ndi sopo musanadye chakudya, mukamachokera kuchimbudzi komanso mukamaphika zakudya.

M’khitchini mwanu muzikhala moyera.

Akatswiri ena ofufuza anapeza kuti ngakhale kuti kubafa kumakhala kosamalidwa bwino kwambiri kuposa malo ena onse panyumba, “zinthu monga zotsukira mbale komanso timataulo topukutira mbale ndi zimene zimakhala ndi tizilombo tambiri toyambitsa matenda.”

Choncho muzisinthasintha timataulo topukutira mbale ndipo muzikolopa m’khitchini mwanu ndi madzi asopo otentha kwambiri kapena muzigwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo. Koma kwa anthu ena zimenezi ndi zovuta. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Bola, amakhala kudera lovuta kupeza madzi. Iye anafotokoza kuti: “N’zoona kuti timavutika kupeza madzi, komabe timayesetsa kukhala ndi madzi komanso sopo nthawi zonse kuti tizikolopera m’nyumba komanso m’khitchini mwathu.”

Muzitsuka kaye zakudya zanu.

Zakudya zisanafike pamsika zimakhala zitathiridwa madzi akuda, zitagwera pandowe kapena zitakhudzana ndi zakudya zina. Choncho muzitsuka zakudya zanu kuti muchotse tizilombo toyambitsa matenda. Muzichita zimenezi ngakhale ndi zakudya zimene zimafunika kusenda monga zipatso komanso ndiwo zina zamasamba. Koma kuchita zimenezi kumafuna nthawi. Mayi wina wa ku Brazil, dzina lake Daiane, ananena kuti: “Ndikamakonza saladi sindipupuluma chifukwa ndimafuna kuonetsetsa kuti masamba ake ayera bwinobwino.”

Musamaphatikize nyama ndi zakudya zina.

Kuti mupewe kufalitsa tizilombo toyambitsa matenda, muziika nyama, nkhuku komanso nsomba m’majumbo osiyana komanso muzionetsetsa kuti zisagundane ndi zakudya zina. Mukamaliza kudula nyama pogwiritsa ntchito thabwa, muzilitsuka kaye ndi sopo komanso madzi otentha musanadulirepo zinthu zina kapena mungachite bwino kungogwiritsa ntchito thabwa komanso mpeni wina.

Ndiyeno, kodi mungatani kuti zakudya zimene mukuphika zikhale zosayambitsa matenda?

[Bokosi patsamba 5]

PHUNZITSANI ANA ANU: “Ana athu tinawaphunzitsa kuti azisamba kaye m’manja asanadye chakudya komanso azitsuka kapena kutaya chakudya chimene chagwera pansi.”—Anatero Hoi, wa ku Hong Kong