3. Muziphika Komanso Kusunga Chakudya Pamalo Abwino
3. Muziphika Komanso Kusunga Chakudya Pamalo Abwino
KALE ku Isiraeli, munthu wina wophika zakudya anathyola mphonda zakutchire ngakhale kuti “sankazidziwa bwinobwino.” Munthuyo anachita zinthu mosasamala chifukwa anatenga mphondazo n’kuziduladula kenako n’kuziphikira limodzi ndi zakudya zina. Anthu atayamba kudya zakudyazo anaona kuti ndi zapoizoni moti anakuwa kuti: “Muli poizoni mumphikamu!”—2 Mafumu 4:38-41.
Chitsanzo chapamwambachi chikusonyeza kuti tiyenera kusamala ndi mmene timaphikira zakudya chifukwa ngati sitisamala anthu akhoza kudwala nazo kapena kufa kumene. Choncho, kuti tipewe kudya zakudya zimene zingatidwalitse, tiyenera kudziwa mmene tingaziphikire komanso kuzisunga mosamala. Taonani njira zinayi zotsatirazi:
● Musamasiye nyama ya m’firiji pamtunda kuti isungunuke.
Akuluakulu a nthambi ya za ulimi ku United States ananena kuti: “Mukatulutsa nyama m’firiji n’kuiika pamtunda kuti isungunuke, ikhoza kuwonongeka ngakhale kuti pakati pa nyamayo pamakhala padakali poundana.” Akatswiri a zaumoyo amati nyama ikakhala pamtunda kwa nthawi yaitali, mwina kwa maola awiri kapena kuposerapo, tizilombo toyambitsa matenda timachulukana mofulumira ndipo munthu atadya nyamayo akhoza kudwala nayo. Choncho mukafuna kusungunula nyama muziika m’jumbo yoti singalowe madzi kenako n’kuiika m’madzi ozizira kapena m’firiji mosazizira kwambiri. Mukhozanso kusungunula nyama pogwiritsa ntchito mayikorowevu.
● Muzionetsetsa kuti nyama yapsa bwinobwino.
Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti: “Pafupifupi tizilombo tonse toyambitsa matenda timafa ngati chakudya chakhala pamoto nthawi yokwanira.” Choncho mukamaphika zakudya ngati nyama ndi nsomba muzionetsetsa kuti pali moto wambiri ndipo zizipsa mokwanira. * Koma popeza kuti n’zovuta kudziwa mmene mkati mwa nyama mwatenthera, anthu ena akamaphika nyama amagwiritsa ntchito kachipangizo koyezera temperecha.
● Muzigawa chakudya mukangomaliza kuphika.
Zakudya zophikaphika sizifunika kukhala pamtunda kwa nthawi yaitali musanazigawe. Choncho zikangopsa, muzigawiratu nthawi yomweyo tizilombo toyambitsa matenda tisanalowe. Muzionetsetsa kuti zakudya zimene zimafunika kuzidya zili zotentha zizikhala pamalo otentha ndipo zakudya zimene zimafunika kuzidya zili zozizira, zizikhalanso pamalo ozizira. Mwachitsanzo, ngati mwaphika nyama ndiyeno mukudikirira kuti muigawe, mungaisiye pamoto pompo koma pakhale moto wochepa.
● Muzisamala chakudya chimene chatsala.
Mayi wina yemwe amakhala ku Poland, dzina lake Anita, amakonda kugawa zakudya zikangopsa. Ponena za chakudya chimene chatsala, iye ananena kuti “ndimachiika m’makontena ang’onoang’ono n’kuchisunga m’firiji. Kuika zakudya m’makontena ang’onoang’ono kumathandiza kuti zidzasungunuke mosavuta.” Ngati mwasunga m’firiji zakudya zotsala, muzionetsetsa kuti mwazidya pasanathe masiku atatu kapena anayi.
Ngati mukukadya kulesitanti simungadziwe mmene aphikira zakudyacho. Ndiye mungatani kuti muteteze banja lanu mukamadya kulesitanti?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Zakudya zina monga nkhuku zimafunika zizipsa kwambiri.
[Bokosi patsamba 6]
PHUNZITSANI ANA ANU: “Ana anga akamaphika ndimawakumbutsa kuti awerenge komanso kutsatira malangizo amene ali papepala la zakudyacho.”—Anatero Yuk Ling wa ku Hong Kong