4. Muzisamala Mukamadya Kulesitanti
4. Muzisamala Mukamadya Kulesitanti
Bambo wina wa zaka 38, dzina lake Jeff anapita ndi banja lake kukadya kulesitanti ina pafupi ndi mzinda wa Pittsburgh ku Pennsylvania, m’dziko la United States. Koma patangotha mwezi umodzi, bamboyu anamwalira chifukwa chakuti chiwindi chake chinasiya kugwira ntchito. Koma kodi n’chiyani chinayambitsa vuto limeneli? Mu chakudya chimene anadya kulesitanti chija munali anyezi amene anali ndi tizilombo toyambitsa matenda otupa chiwindi otchedwa hepatitis A.
M’dziko lina la kumayiko a azungu, anthu ambiri amakonda kukadya kulesitanti. Koma amati akadwala ndi zakudya zosasamalidwa bwino, nthawi zambiri zimakhala zoti anazigula kulesitanti.
N’zoona kuti mukamadya kulesitanti, eniake a lesitantiyo ndi amene amakagula zakudyazo, kuziphika komanso kuyeretsa m’kitchini. Komabe, inuyo muli ndi ufulu wosankha lesitanti imene mungakadye, zakudya zimene mungadye komanso mmene mungasamalilire zakudya zotsala.
● Muziona mmene mkati mukuonekera.
Mayi wina wa ku Brazil, dzina lake Daiane, ananena kuti: “Ndikangolowa koyamba mulesitanti, ndimayang’anitsitsa kuti ndione ngati matebulo, nsalu za patebulo, mbale ndi masipuni zili zoyera. Ndikaona kuti ndi zauve, ndimachoka nthawi yomweyo n’kukayang’ana lesitanti ina.” M’mayiko ena, akuluakulu a boma amayendera malesitanti kuti aone ngati ali aukhondo ndipo amalengeza pawailesi, pa TV kapena mu nyuzi zimene apeza zokhudza lesitantiyo.
● Muzisamala zakudya zotsala.
Bungwe lina la ku America loona za zakudya ndi mankhwala linachenjeza kuti: “Ngati mukuona kuti muchedwa kupita kunyumba, mwina ndi maola awiri, kuchokera pamene mwagula zakudya, musatengere kunyumba zakudyazo. [Koma ngati kukutentha kwambiri, mungafunike kupita kunyumba ndi zakudyazo mofulumira maola awiri asanakwane].” (Food and Drug Administration) Choncho ngati mukutenga zakudya zotsala kulesitanti, muzipita nazo mwamsanga kunyumba n’kukaziika m’firiji.
Ngati mutayesetsa kutsatira njira zinayi zimene tazifotokoza mu nkhani ino, chakudya chanu chikhoza kukhala chosamalidwa bwino ndipo sichingakudwalitseni.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
PHUNZITSANI ANA ANU: “Ana athu tinawaphunzitsa kuti azipewa kudya zakudya zomwe zingawadwalitse.”—Anatero Noemi wa ku Philippines