Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akufa Angathandize Anthu Amoyo?

Kodi Akufa Angathandize Anthu Amoyo?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Akufa Angathandize Anthu Amoyo?

KUYAMBIRA kale anthu akhala akukhulupirira kuti akufa angathandize anthu amoyo. Umboni wa zimenezi ndi nthano ina imene inalembedwa ndi Homer, yemwe anali wolemba ndakatulo wa ku Greece. Nthanoyi imanena za munthu wina dzina lake Odysseus, yemwe anasochera pochokera ku nkhondo. Akuti munthuyu ankafunitsitsa kupeza njira yobwererera kwawo kuchilumba cha Ithaca, choncho anapita kukawombeza kwa sing’anga wina amene anali atamwalira kalekale ndipo ankakhala kudziko lamidima.

Poganiza kuti akufa angawathandize kupeza mayankho a mafunso osiyanasiyana, anthu ambiri amakaombeza kwa sing’anga, kukagona kumanda kapena kuchita zinthu zina zamizimu. Koma kodi n’zotheka kuti munthu wakufa athandize munthu wamoyo?

Zimene Anthu Ambiri Amakhulupirira

Zipembedzo zina zikuluzikulu zimaphunzitsa kuti anthu akhoza kulankhulana ndi akufa. Mwachitsanzo, buku lina lonena za chipembedzo linanena kuti: “Anthu ambiri amachita zinthu zamatsenga n’cholinga chofuna kupempha mizimu ya anthu akufa kuti iwadziwitse zam’tsogolo.” (Encyclopedia of Religion) Pogwirizana ndi mfundo imeneyi, buku linanso linati: “Pali njira zosiyanasiyana zimene anthu amalankhulirana ndi mizimu ya anthu akufa ndipo zimenezi zikuchitika padziko lonse.” (New Catholic Encyclopedia) Choncho, n’zosadabwitsa kuti anthu a zipembedzo zosiyanasiyana amachita zamizimu. Iwo amaganiza kuti zimenezi ziwathandiza kulankhulana ndi mizimu ya anthu akufa.

Buku la New Catholic Encyclopedia, linanenanso kuti, ngakhale kuti Tchalitchi chinkaletsa anthu kulankhula ndi akufa, zikuoneka kuti anthu ambiri ankachitabe zamizimu m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500. Komano kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

Kodi N’zoyenera Kufunsira kwa Akufa?

Kale, Yehova Mulungu analamula anthu ake kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . aliyense wofunsira kwa akufa.” (Deuteronomo 18:9-13) N’chifukwa chiyani Mulungu anawapatsa lamulo limeneli? Ngatidi zinali zotheka kulankhula ndi akufa, kodi Mulungu sakanangowalola kuti azilankhulana ndi anthu akufa? Pamenepa mfundo ndi yakuti, n’zosatheka kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Tikudziwa bwanji zimenezi?

Malemba mobwerezabwereza amaphunzitsa kuti akufa sadziwa chilichonse. Mwachitsanzo, taganizirani malemba awa: Mlaliki 9:5: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” Salimo 146:3, 4: “Musamakhulupirire anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso. Mzimu wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.” Komanso mneneri Yesaya ananena kuti: “Akufa salinso moyo.”—Yesaya 26:14, Malembo Oyera.

Anthu ambiri amakhulupirira kuti nthawi inayake atachita zamizimu anatha kulankhulana ndi achibale awo amene anamwalira. Zimenezi n’zofala masiku ano ndipo zikupereka umboni wakuti anthuwo amakhaladi atalankhulana ndi winawake. Koma malemba omwe ali pamwambawa akusonyeza kuti n’zosatheka kulankhulana ndi akufa. Ndiyeno kodi amalankhulana ndi ndani?

Kodi Amalankhula ndi Ndani Kwenikweni?

Baibulo limatiuza kuti angelo ena anapandukira Mlengi wawo ndipo anakhala ziwanda. (Genesis 6:1-5; Yuda 6, 7) Ziwandazi ndi zimene zimalimbikitsa mfundo yabodza yakuti munthu akamwalira amakhalabe ndi moyo kwinakwake. Pofuna kuti anthu azikhulupirira zimenezi, ziwandazo zimayerekezera kuti ndi anthu akufa amene akulankhulana ndi anthu amoyo.

M’Baibulo muli nkhani ya mfumu ina ya ku Isiraeli, dzina lake Sauli. Yehova atasiya kuthandiza mfumuyi chifukwa sinamumvere, inapita kukaombeza kwa sing’anga kuti akamuthandize kulankhulana ndi mneneri Samueli, yemwe anali atamwalira. Sauli analandiradi uthenga koma siunali wochokera kwa Samueli chifukwa pa nthawi imene anali moyo, Samueli anakana kukaonana ndi Mfumu Sauli komanso ankadana ndi okhulupirira mizimu. Choncho, uthenga umene Sauli analandira unali wochokera kwa chiwanda chomwe chinkanamizira kuti ndi Samueli.—1 Samueli 28:3-20.

Ziwanda ndi adani a Mulungu ndipo kulankhula nazo ndi koopsa kwambiri. N’chifukwa chake Malemba amatilangiza kuti: “Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo ndi kudetsedwa nawo.” (Levitiko 19:31) Lemba la Deuteronomo 18:11, 12 limatichenjeza kuti: “Aliyense wofunsira kwa akufa . . . ndi wonyansa kwa Yehova.” Ndipotu chifukwa chimodzi chimene Mulungu anaphera Mfumu Sauli chinali chakuti “anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu.”—1 Mbiri 10:13, 14.

Ndiyeno ngati mukufuna thandizo, kupeza mayankho a mafunso enaake kapena kusankha zochita, kodi muyenera kufunsira kwa ndani? Malemba amanena kuti Yehova Mulungu ndi “Mlangizi Wamkulu.” Choncho, ngati inuyo pamodzi ndi achibale anu mutafufuza zimene Baibulo limanena komanso kuchita zimene limaphunzitsa, zidzakhala ngati ‘makutu anu akumva mawu [a Mulungu] kumbuyo kwanu, akuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu anthu inu.”’ (Yesaya 30:20, 21) Akhristu masiku ano sayembekezera kuti angamvedi Mulungu akuwalankhula, koma iwo amadziwa kuti Iye amawatsogolera pogwiritsa ntchito Baibulo. Zili ngati Yehova akuwauza kuti: ‘Ineyo ndi amene ndizikutsogolerani.’

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Mulungu amaona bwanji anthu amene amayesa kulankhula ndi akufa?—Deuteronomo 18:9-13.

● Kodi anthu akufa angatithandize nzeru? N’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?—Mlaliki 9:5.

● Ndani amene tingamudalire kuti atithandize komanso kutipatsa malangizo?—Yesaya 30:20, 21.