Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 1

Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 1

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 1

KODI MUTUWU WAKUKUMBUTSANI ZA MUNTHU WINAWAKE?

INDE → WERENGANI NKHANI INO MWAMSANGA CHIFUKWA INGAKUTHANDIZENI.

AYI → WERENGANIBE NKHANIYI CHIFUKWA INGAKUTHANDIZENI KUTI MUZICHEZA NDI ANYAMATA KAPENA ATSIKANA MOYENERA KOMANSO KUTI PASAMAKHALE MAVUTO ALIONSE.

Chongani ngati chiganizo chotsatirachi chikunena zoona kapena zonama:

Sindiyenera kucheza ndi anyamata kapena atsikana mpaka pamene ndidzakhale wokonzeka kukhala pachibwenzi.

․․․․․ ZOONA ․․․․․ ZONAMA

Taganizirani izi: Yesu ankacheza ndi akazi ngakhale kuti analibe maganizo aliwonse ofuna kukwatira. (Mateyu 12:46-50; Luka 8:1-3) Zikuoneka kuti ndi mmenenso zinalili ndi Timoteyo chifukwa pa nthawi ina mtumwi Paulo anamulangiza kuti: “Akazi achitsikana uwadandaulire ngati alongo ako, ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse oipa.”—1 Timoteyo 5:1, 2.

Paulo ayenera kuti ankadziwa kuti Timoteyo akamayendera mipingo yosiyanasiyana azikumana ndi atsikana. (Maliko 10:29, 30) Kodi panali cholakwika chilichonse kuti Timoteyo azicheza ndi atsikanawo? Ayi. Komabe iye anafunika kukhala ndi malire chifukwa pa nthawiyi analibe mapulani ofuna kukwatira. Zimenezi zikanamuthandiza kuti asayambe kukondana kwambiri ndi atsikanawo, kuwakopa kapena kumachita zinthu zokhala ngati akuwafuna.—Luka 6:31.

Nanga bwanji inuyo? Kodi ndinu wokonzeka kukwatira?

Ngati mwayankha kuti INDE ⇨ Kucheza ndi atsikana kapena anyamata kungakuthandizeni kuti mupeze munthu amene mungadzamange naye banja.—Miyambo 18:22; 31:10.

Ngati mwayankha kuti AYI ⇨ Ndiye kuti muyenera kudziikira malire. (Yeremiya 17:9) Komabe kuchita zimenezi sikophweka. Mwachitsanzo mtsikana wina wa zaka 18, dzina lake Nia, * ananena kuti: “N’zovuta kuti mnyamata ndi mtsikana azingocheza osayamba kukondana ndipo zimavuta kuti mudziikire malire.”

Komano n’chifukwa chiyani muyenera kudziikira malire? Chifukwa choti ngati simungadziikire malire pamapeto pake mungakhumudwe kapena kukhumudwitsa ena. Tiyeni tione chifukwa chake tikunena choncho.

DZIWANI IZI: Ngati mutayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana musanakonzeke kukhala pachibwenzi, mukhoza kukhumudwa kapena kukhumudwitsa mnzanuyo. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Kelli, ananena kuti: “Zimenezi zinandichitikirapo kawiri. Nthawi ina ndinayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata wina ndipo nthawi inanso mnyamata wina anayamba kuchita zinthu zosonyeza kuti amandifuna. Anyamatawa anakhumudwa chifukwa sindinawasonyeze chidwi chenicheni ndipo ineyo mpaka pano zimandikhudza kwambiri ndikakumbukira zimene zinachitikazo.”

Taganizirani izi:

Kodi inuyo mukuona kuti ndi pa zochitika ziti zimene muyenera kucheza ndi anyamata kapena atsikana? Nanga ndi nthawi iti imene mungachite bwino kupewa kucheza ndi anyamata kapena atsikana?

N’chifukwa chiyani mukakhala pa gulu sibwino kuti muzingocheza ndi mnyamata kapena mtsikana mmodzimodzi nthawi zonse? Kodi anthu ena angaganize chiyani? Nanga inuyo mungayambe kuganiza chiyani?

“Nthawi zina ndimadziuza kuti: ‘Palibe vuto lililonse chifukwa ndimangocheza naye komanso ndimangomuona ngati mchimwene wanga basi.’ Koma kenako ndikamuona akucheza ndi mtsikana wina, mtima umandiwawa zedi chifukwa ndimafuna kuti azicheza ndi ineyo basi.”—Anatero Denise.

Baibulo limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”—Miyambo 22:3.

DZIWANI IZI: Ngati mutayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana musanakonzeke kukhala pachibwenzi, mukhoza kudana. Mtsikana wina wa zaka 16, dzina lake Kati, ananena kuti: “Ndinkakonda kulemberana mameseji pafoni ndi mnyamata winawake koma kenako anayamba kundikopa moti tinkatumizirana mameseji pafupifupi tsiku lililonse. Ndiyeno tsiku lina mnyamatayu anandiuza kuti amandikonda kwambiri moti sakufuna kuti zingothera pa chinzake basi. Koma vuto linali loti ineyo sindinkafuna n’komwe kukhala naye pa chibwenzi moti nditamuuza zimenezi tinayamba kulankhulana mwa apo ndi apo ndipo kenako tinangosiyiratu kuchezerana.”

Taganizirani izi:

Kodi ndani anakhumudwa pa zimene zinachitika pakati pa Kati ndi mnyamata uja? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho? Kodi mukuganiza kuti Kati kapena mnyamata uja akanatha kupewa kuti aliyense asakhumudwe? Ngati inde, akanatani?

Polemberana mameseji pafoni, kodi mnyamata kapena mtsikana mosadziwa angachite chiyani chimene wina angaone ngati ndi chizindikiro chakuti akumufuna?

“Nthawi zina ndimachita kudziletsa kuti ndisamacheze kwambiri ndi mnyamata. Kunena zoona anyamata amasangalatsa kucheza nawo, koma sindikufuna kudana ndi mnyamata aliyense chifukwa choyamba kukondana naye kwambiri pomwe ndilibe cholinga chokhala naye pa chibwenzi.”—Anatero Laura.

Baibulo limanena kuti: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miyambo 14:15.

Mfundo yaikulu: Kucheza ndi atsikana kapena anyamata sikulakwa. Koma ngati simunakonzeke kukhala pa chibwenzi, muyenera kudziikira malire.

NKHANI YOTSATIRA YA “ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA” IDZAFOTOKOZA ZA  . . .

Mmene kucheza kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana koma mulibe cholinga chofuna kukhala pa chibwenzi kungawonongere mbiri yanu.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 16]

MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

NKHANI IMENE INACHITIKADI: “Ndinkakonda kutumizirana mameseji a pafoni ndi mnyamata wina kamodzi pa mlungu. Mnyamatayu ankakhala kudera linalake lakutali, mwina makilomita opitirira 1,500, kuchokera kumene ndinkakhala. Sindinkamufuna komanso sindinkaganiza kuti iye amandifuna. Koma tsiku lina ananditumizira meseji yakuti: ‘Yesi chiphadzuwa changa, ndakusowa kwambiri. Umatani lero?’ Ndinadabwa kwambiri. Ndinamuuza kuti ndinkangocheza naye ngati mnzanga moti sindinkaganiza n’komwe kuti ndingakhale naye pa chibwenzi. Nditamuuza zimenezi, iye anangondiyankha kuti: ‘Ngati zili zimenezo ndiye basitu.’ Kungoyambira nthawi imeneyo sananditumizirenso meseji iliyonse.”—Anatero Janette.

● Ngati simunakonzeke kapena ngati simukufuna kukhala pa chibwenzi, kodi mungatani mutalandira meseji ngati imene Janette analandira?

● Ngati ndinu mnyamata, kodi mukuganiza kuti meseji imene mnyamatayo analemba inali yoyenera? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

● Kodi inuyo mumaona kuti kutumizirana mameseji kumachititsa kuti anthu ayambe kukondana kwambiri kuposa mmene zingakhalire atamacheza pamasom’pamaso? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

[Bokosi patsamba 17]

FUNSANI MAKOLO ANU

Funsani makolo anu kuti anene maganizo awo pa mafunso amene ali ndi madontho m’nkhani ino. Kodi maganizo awo akusiyana ndi anu? Ngati akusiyana, akusiyana pati? Kodi mukuona kuti maganizo awowo akhoza kukhala othandiza?—Miyambo 11:14.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 17]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Joshua​—Ukamangocheza ndi munthu yemweyemweyo, mumapezeka kuti mwayamba kufunana.

Natasha​—Ngati mumacheza ndi mnyamata kapena mtsikana ngati mnzanu chabe, koma nthawi zambiri mumafuna kuti muzingocheza ndi iyeyo basi, pamapeto pake mukhoza kuyamba kumufuna kapena mukhoza kuyamba kufunana.

Kelsey​—Ngakhale kuti poyamba mukhoza kumangoonana ngati munthu ndi mnzake, koma ngati nthawi zambiri mumakonda kucheza awiri, mukhoza kuyamba kufunana. N’zotheka kumangocheza ngati munthu ndi mnzake koma pamafunika kuchita zinthu mwanzeru komanso kuganiza bwino.

[Chithunzi patsamba 16]

Kucheza kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana koma mulibe cholinga chokhala naye pa chibwenzi kungabweretse mavuto aakulu