Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kusamalira Mwapadera Munthu Wodwala Matenda Oti Sachira (July 2011)Ndimagwira ntchito yosamalira anthu ndipo ndinaphunzira mmene ndingathandizire munthu amene akudwala matenda oti sachira. Ndikugwirizana kwambiri ndi zimene munalemba mu Galamukani! ya July 2011. Masiku ano pakufunikiradi malo ambiri osamalirira anthu amene akudwala matenda oti sachira. Koma ineyo ndimayembekezera nthawi imene boma la Mulungu lidzayambe kulamulira, pomwe sipadzakhala amene adzanene kuti: “Ndikudwala.” Nthawi imeneyo Mulungu adzapukuta misozi yathu yonse.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4.

M. R., Italy

Kodi Mungadziwe Bwanji Kuti Muli ndi Matenda a Chithokomiro? (May 2009) Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cholemba nkhaniyi. Ndinazindikira kuti ndili ndi vuto la chithokomiro zaka zingapo zapitazo koma ndinangolinyalanyaza. Kenako nditawerenga nkhaniyi ndinapita kuchipatala komwe anandipeza ndi nthenda ya chithokomiro koma inali isanafalikire kwambiri. Kachiwirinso ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi.

T. K., Japan

Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 1 mpaka 7 (November 2010–May 2011) Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha nkhani zimenezi. Ndikuona kuti zinalembedwa mwaluso ndipo amene anazilemba ayenera kuti anafufuza kwambiri za maufumu amphamvu omwe anatchulidwa m’Baibulo. Ndingasangalale kwambiri mutatulutsa kabuku konena za nkhani zimenezi zokhazokha. Ndikuona kuti nkhanizi zikhoza kuthandiza anthu kuti azilemekeza kwambiri amene ananena maulosi amenewa, yemwe ndi Yehova.

G. H., United States

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Malo Ochezera a pa Intaneti? (July 2011) Zikomo kwambiri chifukwa cholemba nkhani imeneyi. Ndili ndi zaka 26 ndipo m’mbuyomu ndakhala ndikuganiza zoti ndiyambe kucheza ndi anthu pamalo ochezera a pa Intaneti. Ndinkafuna kuchita zimenezi chifukwa chakuti anthu ena ndi amene ankandilimbikitsa. Nkhaniyi yandithandiza kwambiri kudziwa kuti munthu ungathe kupeza anthu ocheza nawo ngakhale kuti sunalembetse pamalo ochezera pa Intaneti.

M. P., Philippines

Ndinkayembekezera kuti nkhani imeneyi inena zoipa zokhazokha zokhudza malo ochezera a pa Intaneti. Koma ndaona kuti yasonyeza ubwino ndi kuipa kwa malo amenewa. Mu nkhaniyi mulinso malangizo a mmene tingadzitetezere tikamacheza ndi anthu pa Intaneti. Kunena zoona nkhaniyi yandithandiza kuona kufunika kokhala osamala tikamaika zinthu pa Intaneti.

C. W., United States

Mfundo Zothandiza Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino (October 2009) Magazini yapadera imeneyi yathandiza kwambiri banja lathu. Ndinasangalala kwambiri ndi timabokosi takuti “Yesani izi” tomwe tili ndi mfundo 7 za m’magaziniyi. Banja lathu layamba kale kugwiritsa ntchito malangizo a m’timabokosi timeneti.

H. H., Korea

Zoti Banja Likambirane Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani zimenezi. Mwana wathu wamkazi wazaka 6 amakonda kwambiri mbali yakuti, “Zithunzi Zoti Ana Apeze,” ndipo amasangalala akamachekenira zithunzizo. Nkhanizi zimathandiza makolo pophunzitsa ana awo adakali aang’ono. Zimene mukuchita pothandiza ana aang’ono ndi zotamandika kwambiri.

M. P., Poland