Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Posachedwapa Aliyense Azidzadya Zakudya Zosamalidwa Bwino

Posachedwapa Aliyense Azidzadya Zakudya Zosamalidwa Bwino

Posachedwapa Aliyense Azidzadya Zakudya Zosamalidwa Bwino

MWINA mukhoza kuyesetsa kuti zakudya zanu zizikhala zosamalidwa bwino, komabe pali zinthu zina zimene simungazikwanitse. Mwachitsanzo, simungakwanitse kufufuza bwinobwino zakudya zonse zomwe mumagula kapena kuphika. Nthawi zina mungafunike kugula zakudya zochokera kumayiko akutali. Ndiponso zina mwa zakudya zimene mumagula zingakhale ndi mankhwala oipa ochokera mumpweya, m’madzi kapena m’nthaka.

Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linatulutsa lipoti lonena za kuthetsa matenda oyamba chifukwa cha zakudya zosasamalidwa bwino. Mu lipotili, akuluakulu a ku bungweli ananena kuti matenda ena amene amabwera chifukwa cha zakudya zosasamalidwa bwino, “akhoza kutha pokhapokha ngati mayiko onse atagwirizana kuthetsa vutoli.” Zimenezi zikusonyeza kuti vuto la matenda obwera chifukwa cha zakudya lili padziko lonse.

Choncho, n’zomveka kuti anthu ena amadabwa tikamanena kuti posachedwapa aliyense azidzadya zakudya zosamalidwa bwino. Koma “Yehova, Ambuye wa dziko lonse lapansi,” walonjeza kuti adzathetsa vuto limeneli. (Yoswa 3:13) Koma anthu ena anganene kuti chifukwa chakuti masiku ano anthu ambiri amadya chakudya chosasamalidwa bwino, umenewu ndi umboni wakuti Yehova sangathetse vutoli. Koma tayerekezerani izi: Wophika wakonza chakudya chabwinobwino ndipo wachipereka kwa woperekera zakudya kuti akapatse anthu. Woperekerayo sakusamala chakudyacho ndipo chikulowa tizilombo toyambitsa matenda. Kodi pamenepa munganene kuti amene walakwitsa ndi wophikayo? N’zachidziwikire kuti simungatero.

Mofanana ndi zimenezi, anthu osati Mlengi, ndi amene achititsa kuti padziko lapansi pazipezeka chakudya chosasamalidwa bwino. Koma Mulungu walonjeza kuti ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’—Chivumbulutso 11:18.

Zimene Mulungu anachita kale m’mbuyomu zimasonyeza kuti amafuna kuti anthu azidya chakudya chabwino. Mwachitsanzo, Iye ndi amene analenga dziko lapansi ndiponso mitengo ‘yooneka bwino’ komanso ya “zipatso zabwino kudya.” (Genesis 2:9) Komanso ngakhale pamene anthu anachimwa n’kuyamba kudwala, Yehova Mulungu anawapatsa malangizo oteteza matupi komanso zakudya zawo.—Onani bokosi lakuti, “Malamulo pa Nkhani Yaukhondo.”

Koma kodi Mulungu amafuna kuti tizidya zakudya zotani? Baibulo limatiuza kuti: “[Mulungu] amameretsa msipu kuti nyama zidye, ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito. Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke m’nthaka, komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu. Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta, komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.” (Salimo 104:14, 15) Baibulo linanenanso kuti: “Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu.”—Genesis 9:3.

Ponena za zimene zidzachitike m’tsogolo, Mawu a Mulungu amati: “Mulungu adzabweretsa mvula pa mbewu zanu zimene munabzala munthaka, ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala chakudya chopatsa thanzi. M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.” (Yesaya 30:23) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene nkhani zomvetsa chisoni za anthu amene adwala kapena kumwalira chifukwa cha chakudya chosasamalidwa bwino sizidzamvekanso. Panthawi imeneyi aliyense azidzadya chakudya chabwino komanso chopatsa thanzi.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Mlengi wathu watilonjeza kuti m’tsogolo muno tizidzadya chakudya chabwino komanso chokwanira

[Bokosi patsamba 8]

“MALAMULO PA NKHANI YAUKHONDO”

Zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, Aisiraeli anapatsidwa Chilamulo cha Mose. Chilamulocho chinkawateteza ku matenda ambiri omwe amabwera chifukwa cha chakudya chosasamalidwa bwino. Taonani ena mwa malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli:

● Azipewa chiwiya chilichonse chodetsedwa chimene chakhudza nyama yakufa: “Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziikidwa m’madzi, koma chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo, kenako chizikhala choyera.”—Levitiko 11:31-34.

● Asamadye nyama imene yafa yokha: “Musadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.”—Deuteronomo 14:21.

● Azidya zakudya zotsala pasanapite masiku ambiri: ‘Mungathenso kudya imene yatsala pa tsiku lotsatira. Nyama ya nsembeyo, imene yatsala kufika tsiku lachitatu, muyenera kuitentha ndi moto.’—Levitiko 7:16-18.

Dokotala wina, dzina lake A. Rendle Short, anadabwa kuti Chilamulo cha Mose chinali ndi “malamulo anzeru komanso othandiza kwambiri pa nkhani ya ukhondo,” poyerekezera ndi malamulo a zaukhondo amene mitundu ina inkayendera.