Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Chiwerengero cha anthu padziko lonse pofika mu 1999 chinali 6 biliyoni koma chakumapeto kwa chaka cha 2011 chinakwera kufika pa 7 biliyoni.—HARVARD SCHOOL OF PUBLIC HEALTH, U.S.A.
“Pafupifupi hafu ya anthu a ku [United Kingdom] amaona kuti zinthu zingamayende bwino kwambiri m’mabanja mwawo zikanakhala kuti nthawi zina amathimitsa mafoni, mawailesi, ma TV, makompyuta ndi zipangizo zina. . . . Munthu mmodzi pa atatu aliwonse ananena kuti nthawi zina zinthu zimenezi zimawatopetsa kwambiri moti amangofuna kusiyiratu kuzigwiritsa ntchito.”—UNIVERSITY OF CAMBRIDGE, BRITAIN.
“Kuyambira mu 1976, mabishopu achikatolika ku America amatulutsa chikalata . . . nthawi ya chisankho cha pulezidenti ikayandikira. Iwo amachita zimenezi n’cholinga choti athandize Akatolika kugwiritsa ntchito zimene amakhulupirira posankha munthu amene akumufuna.”—FORDHAM UNIVERSITY, U.S.A.
“Anthu ophwanya malamulo akatsimikiza mtima, amatha kuchita zinthu zosokoneza m’misewu ngakhale atakhala ochepa. . . . Mwachitsanzo, achinyamata ena ku Britain akuchita zinthu zopanda khalidwe. Ngakhale kuti achinyamatawa ndi ochepa, avutitsa kwambiri anthu komanso achititsa manyazi dziko lonse la Britain.”—THE ECONOMIST, BRITAIN.
Kodi Padzikoli Pali Mitundu Ingati ya Nyama ndi Zomera?
Asayansi ena anachita kafukufuku wofuna kudziwa kuti padziko lapansi pali mitundu ya nyama ndi zomera ingati ndipo anatulutsa lipoti la zimene anapezazo m’magazini ya PLoS Biology. Mu lipotili, iwo anafotokoza kuti: “Sitinganene motsimikiza kuti pali mitundu ingati ya nyama ndi zomera. Ndipo umenewu ndi umboni wosonyeza kuti anthufe timangodziwa zochepa kwambiri za zinthu zamoyo zimene zili padziko lapansili.” Ngakhale kuti asayansiwa akuganiza kuti mwina pali mitundu ya zamoyo pakati pa 7.5 miliyoni ndi 10 miliyoni, akatswiri ena amanena kuti zilipo pakati pa 3 miliyoni ndi 100 miliyoni. Padakali pano mitundu ya zamoyo imene ikudziwika ndi pafupifupi 1.2 miliyoni ndipo akukhulupirira kuti pangatenge zaka zoposa 1,000 kuti adzadziwe bwinobwino mitundu ina yotsalayo. Akatswiri ena ofufuza amanena kuti: “Ntchito yofufuza komanso kudziwa bwinobwino mitundu ya zamoyo ikuchitika pang’onopang’ono ndipo n’kutheka kuti mitundu ina idzafika mpaka potheratu tisanaidziwe bwinobwino.”
Akufufuza Zinthu Zakale Pogwiritsa Ntchito Makamera a Mumlengalenga
Akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza njira yatsopano yofufuzira malo amene angapeze zinthu zakale. Iwo akuchita zimenezi pogwiritsa ntchito makompyuta amene amawathandiza kuzindikira malo a zinthu zakale ojambulidwa ndi makamera a mumlengalenga. Mwachitsanzo, akuti zithunzi zimene zinajambulidwa ndi makamera amene ali pamtunda wa makilomita 700, pamwamba pa dziko la Egypt, zimasonyeza manda a mafumu akale a ku Egypt, amene angowatulukira kumene okwana 17. Zimasonyezanso manda a anthu wamba okwana 1,000 komanso malo okwana 3,000 amene kale kunkakhala anthu. Makamerawa ndi amphamvu kwambiri moti akumajambula ngakhale zinthu zimene zinakwiririka pansi. Zimenezi zikuthandiza kuti anthu adziwe zinthu zakale kwambiri zimene sizionekera pamtunda.