Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chikuyenera Kusintha?

Kodi N’chiyani Chikuyenera Kusintha?

Kodi N’chiyani Chikuyenera Kusintha?

“Boma silingathetse mavuto athu chifukwa vuto ndi bomalo.”—Anatero Ronald W. Reagan, yemwe anali pulezidenti wanambala 40 wadziko la United States ndipo analankhula mawu amenewa atangomulumbiritsa kumene ngati pulezidenti wadzikolo.

PADUTSA zaka zoposa 30 kuchokera pamene Ronald Reagan analankhula mawu amenewa. Nthawi imeneyo, dziko la United States linali pa mavuto aakulu azachuma. Pulezidentiyu ananena kuti dzikolo linkakumana ndi “mavuto aakulu azachuma.” Iye anapitiriza kunena kuti: “Mitengo ya zinthu yakwera kwambiri ndipo zimenezi sizinachitikepo m’mbiri ya dziko lathu. Kwa zaka zambiri dziko lathu lakhala likungotenga ngongole m’mayiko ena koma osabweza. Tikuwononga ndalama pofuna kungosangalala ndi moyo, kuiwala kuti zimenezi zidzachititsa kuti ifeyo komanso ana athu adzavutike m’tsogolo. Tikalola kuti zimenezi zipitirire ndiye kuti m’tsogolo muno tidzakumana ndi mavuto a zandale, a zachuma, komanso kusokonekera kwa chikhalidwe.”

Ngakhale kuti iye ankada nkhawa ndi zimenezi, pulezidentiyu ankakhulupirira kuti zinthu zikhoza kuyamba kuyenda bwino. Tikutero chifukwa iye anapitiriza kunena kuti: “Mavuto azachuma amene tikukumana nawowa anayamba kale kwambiri. Tisaganize kuti angotha lero ndi lero. Komabe tisakayikire kuti adzatha ndithu.”

Kodi zinthu zili bwanji masiku ano? Lipoti lina la nthambi yaboma yoona zamalo ndi nyumba ku United States, limene linatuluka mu 2009 linati: “Pali anthu ambiri amene akusowa nyumba, chithandizo chakuchipatala, madzi komanso magetsi. Ndipotu nthambi [ya bungwe la United Nations] yoona za malo okhala ikuganiza kuti pomatha zaka 30 kutsogoloku, pa anthu atatu alionse, munthu mmodzi azidzasowa malo okhala komanso madzi aukhondo. Azidzavutikanso kwambiri chifukwa cha kusintha kwa nyengo, zomwe zingadzachititse kuti matenda komanso miliri ifalikire.”

Aliyense Akuda Nazo Nkhawa

Mosaganizira za kumene mumakhala, kodi mungayankhe bwanji mafunso awa:

● Kodi mukuona kuti zinthu zikukuyenderani bwino kwambiri pa zachuma kuposa mmene zinalili zaka 10 zapitazo?

● Kodi inuyo komanso banja lanu likhoza kupeza chithandizo chamankhwala mosavuta?

● Kodi anthu akukhala malo aukhondo?

● Mukayang’ana zaka 10, 20 kapena 30 kutsogoloku, kodi mukuona kuti zinthu zidzakhala zikuyenda bwino?

Mgwirizano wa Boma ndi Nzika Zake

M’mayiko ambiri boma limasayinirana pangano ndi nzika zake. Panganolo limakhala lokhudza zimene bomalo komanso nzika zake ziyenera kuchita. Mwachitsanzo, nzika zimasayinira kuti zizimvera malamulo a boma, zizikhoma msonkho komanso zizichita nawo zinthu zotukula dziko lawo. Nthawi zambiri boma limalonjeza kuti lizipereka chithandizo chamankhwala chokwanira, lizionetsetsa kuti aliyense akupeza zinthu mofanana komanso kuti liziyendetsa bwino chuma chake.

Koma kodi maboma akwanitsa kuchita zimenezi? Kuti tipeze yankho, tiyeni tione mmene maboma achitira pankhani zitatu zimenezi.

Chithandizo Chamankhwala

Zimene anthu amafuna: Chithandizo chamankhwala chosafuna ndalama zambiri komanso chothandizadi.

Zimene zikuchitika:

● Banki lalikulu la padziko lonse linatulutsa lipoti lonena za ukhondo. Lipotili linasonyeza kuti “tsiku lililonse ana 6,000, amafa chifukwa chomwa madzi omwe si aukhondo, uve komanso matenda oyamba chifukwa chokhala m’malo opanda zimbudzi. Pa masekondi 20 alionse, mwana mmodzi amamwalira chifukwa cha matenda otsegula m’mimba.”

● Mu 2008, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linachita kafukufuku wofuna kudziwa mmene “mayiko olemera komanso osauka” amayendetsera nkhani zokhudza umoyo. Bungweli linapeza kuti anthu a m’mayikowa “salandira chithandizo chamankhwala chofanana.” Linapezanso kuti njira zimene zikutsatiridwa popereka chithandizocho “sizigwirizana ndi zimene anthu amafunikiradi, ndi zokondera, zofuna ndalama zambiri komanso sizikuthandiza anthu wamba ngakhale pang’ono.”

Patatha zaka ziwiri, bungweli linapezanso kuti, “mayiko ambiri padziko lonse akuvutika kulipira chithandizo chamankhwala cha nzika zawo. Zimenezi zikuchitika chifukwa chakuti chiwerengero cha anthu komanso cha amene akudwala matenda aakulu chikukwera. Chifukwa chinanso n’chakuti njira zatsopano zochizira matenda zomwe akatswiri akutulukira ndi zokwera mtengo kwambiri.”

● Masiku ano, mankhwala amene anthu ankawadalira kwambiri sakugwiranso ntchito. Mwachitsanzo, kale matenda monga khate ndi chifuwa cha TB ankapha anthu mamiliyoni ambiri, komabe munthu ankatha kuchira akapatsidwa mankhwala opha mabakiteriya. Mankhwala oyamba amtunduwu anayamba kugwiritsidwa ntchito cha m’ma 1940. Mu 2011, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linatulutsa lipoti patsiku lokumbukira zaumoyo. Lipotilo linati: “Masiku ano kuli tizilombo toyambitsa matenda tosamva mankhwala moti mankhwala omwe tinkawadalira poyamba sakugwiranso ntchito. Zimenezi zikuchititsa kuti pakhale mankhwala ochepa amene akugwiritsidwa ntchito.”

Chimene chikufunika kusintha: Tikufuna kudzaona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo umene umanena za nthawi imene ‘wokhala m’dziko latsopano sadzanena kuti: “Ndikudwala.”’—Yesaya 33:24.

Chilungamo

Zimene anthu amafuna: Aliyense azichitiridwa zinthu mwachilungamo, azimayi asamachitiridwe nkhanza komanso kuti pasakhale kusiyana kwambiri pakati pa anthu osauka ndi olemera.

Zimene zikuchitika:

● Lipoti lina la bungwe loona za ufulu wa anthu linanena kuti: “Ziwawa zimene anthu amachita monga kuwononga nyumba zopempherera, zipatala komanso masukulu, zikuwonjezereka ndipo zikubweretsa mavuto ambiri m’dziko la United States. Anthu amachita zachiwawazi chifukwa chodana ndi anthu amtundu wina, ochokera dziko lina kapena achipembedzo china. Amachitiranso zachiwawa anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo.”—Leadership Conference on Civil Rights Education Fund.

● Bungwe la United Nations linatulutsa lipoti lonena za ufulu wa azimayi. Lipotili linati: “Azimayi ambiri padziko lonse akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo, nkhanza komanso kusankhidwa. Iwo amakumana ndi mavuto amenewa m’nyumba zawo, kuntchito komanso kulikonse kumene apita.” Mwachitsanzo, ku Afghanistan, azimayi oyembekezera 85 pa 100 aliwonse amabereka popanda mzamba. Komanso ku Yemen, kulibe lamulo loletsa kuchitira nkhanza azimayi. Ndipo ku Democratic Republic of Congo, pa avereji azimayi oposa 1,000 amagwiriridwa tsiku lililonse.

● Mu October 2011, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, a Ban Ki-moon, ananena kuti: “Zimene zimachitika padzikoli n’zovuta kumvetsa. Mwachitsanzo, pali chakudya chambiri koma anthu 1 biliyoni alibiretu chakudya. Anthu ena akukhala moyo wapamwamba kwambiri pomwe ena ali pa umphawi wadzaoneni. Zachipatala zapita patsogolo kwambiri koma tsiku lililonse azimayi ambiri akumamwalira pobereka.  . . Ndalama zambiri zikugwiritsidwa ntchito pogulira zida zankhondo m’malo mothandizira anthu.”

Chimene chikufunika kusintha: Aliyense kuphatikizapo azimayi azichitiridwa zinthu mwachilungamo. Tikufuna kuti pasadzapezekenso ‘anthu amene amalanda chilungamo anthu osautsika.’—Yesaya 10:1, 2.

Zachuma

Zimene anthu amafuna: Aliyense atakhala pa ntchito komanso chuma chikuyenda bwino.

Zimene zikuchitika:

● Bungwe la Worldwatch Institute linanena kuti: “Pali anthu ambiri odziwa ntchito amene angathandize kuti chuma cha mayiko chitukuke, koma vuto ndiloti ntchito zikusowa. Ponena za mmene zinthu zilili pa nkhani ya zachuma, nthambi ya bungwe la United Nations, yoona za anthu a pa ntchito, inanena kuti mu 2010, anthu pafupifupi 205 miliyoni padziko lonse anali pa ulova.”

● Wailesi ya BBC inalengeza kuti: “Bungwe loona za anthu a pa ntchito padziko lonse linanena kuti, kusayenda bwino kwa zachuma kuchititsa kuti anthu ambiri akhale pa ulova komanso ena ayambe kuchita zipolowe. Chifukwa cha kusayenda bwino kwa zachuma m’mayiko osiyanasiyana, anthu omwe akupeza ntchito ndi ochepa kwambiri. . . . Bungweli linanenanso kuti anthu ambiri ndi okwiya chifukwa akuona kuti palibe akuwathandiza kuthetsa mavuto azachuma. Linanenanso kuti anthu m’mayiko ambiri makamaka a ku Europe komanso m’mayiko a Aluya akhoza kuyamba kuchita zipolowe.”

● Buku lina, lomwe linatulutsidwa mu 2009, linanena kuti: “Ku United States, pafupifupi munthu aliyense amakhala ndi ngongole yoposa madola 11,000 ndipo ndalama zimenezi ndi zambiri poyerekezera ndi ndalama zimene anthu ankakongola mu 1990.” Amene analemba bukuli ananenanso kuti anthu ambiri amatenga ngongole zambirimbiri n’cholinga choti azioneka ngati olemera. Iye ananena kuti: “Anthu ena ku America akaona anzawo akugula magalimoto komanso zovala zodula amaganiza kuti ndi olemera. Koma zoona zake ndi zakuti anthuwa siolemera chifukwa zinthuzo amakhala atazitenga pa ngongole.”—The Narcissism Epidemic.

Chimene chikufunika kusintha: Aliyense akhale pa ntchito komanso kuti anthu azigwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. Baibulo limanena kuti, “ndalama zimatetezera” koma limachenjezanso kuti, “kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.”—Mlaliki 7:12; 1 Timoteyo 6:10.

Mukaona zimene tafotokoza pamasamba 4 mpaka 8, mwina mungaganize kuti zinthu sizidzakhalanso bwino m’tsogolomu. Komatu zinthu zidzasintha, kungoti adzasinthe zimenezi si maboma a anthu.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 5]

Kodi achinyamata amafuna atasintha chiyani padzikoli? Webusayiti ina yotchedwa 4children.org, inatulutsa zotsatira za kafukufuku wina yemwe anachitika ku Britain. Pa kafukufukuyu anapeza kuti ana 2,000, azaka zapakati pa 4 mpaka 14, amalakalaka atachita zinthu zotsatirazi:

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

100%

KUTHETSA NJALA

KUTHETSA NKHONDO

KUTHETSA UMPHAWI

75%

KUTHANDIZA KUTI ALIYENSE AZICHITIRIDWA ZINTHU MWACHILUNGAMO

KUTHETSA KUSINTHA KWA NYENGO

50%

25%

0%

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 5]

Mu 2009, bungwe lina la ku Germany, lotchedwa Bertelsmann Foundation, linachita kafukufuku kwa achinyamata pafupifupi 500, azaka zapakati pa 14 ndi 18. Linachita kafukufukuyo pofuna kudziwa zinthu zimene zimadetsa nkhawa kwambiri achinyamatawa.

Iwo ananena kuti sada nkhawa kwenikweni ndi zinthu monga uchigawenga, kuchuluka kwa chiwerengero cha anthu komanso kusayenda bwino kwa zachuma. Bungweli linafotokoza kuti n’kutheka kuti achinyamatawa sada nkhawa ndi zimenezi chifukwa sanakumanepo ndi mavuto amenewa pamoyo wawo.

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

100%

75%

UMPHAWI

KUSINTHA KWA NYENGO KOMANSO KUWONONGEKA KWA MALO OKHALA

KUSOWA KWA CHAKUDYA NDI MADZI

MILIRI NDI MATENDA

50%

25%

0%