Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani Genesis 1:21-28. Kenako yang’anani chithunzichi. Tchulani zinthu zimene zikusowekapo. Lembani mayankho anu m’munsimu. Malizitsani kujambula chithunzichi polumikiza timadonthoto, ndipo chikongoletseni ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KAMBIRANANI:

Kodi Mulungu ankalankhula ndi ndani pamene ankanena kuti: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu, kuti akhale wofanana nafe”?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yohane 17:1, 5; Akolose 1:15, 16.

Kodi mawu akuti anthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu amatanthauza chiyani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Akolose 3:10; 1 Petulo 1:16.

Kodi ndi makhalidwe ati a Yehova Mulungu komanso Yesu amene amakusangalatsani kwambiri? Kodi mungatsanzire bwanji makhalidwe amenewa?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Aefeso 4:31, 32; 1 Yohane 4:7, 8.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Tchulani nyama zisanu zimene mumazikonda kwambiri. Ndiyeno ngati mmene Adamu anachitira, muzipatse nyamazo mayina atsopano potengera mmene zimaonekera, kulira kwake komanso mmene zimachitira zinthu. Kenako muzitchula dzina latsopano la nyama iliyonse mokweza kuti anthu a m’banja mwanu anene kuti ndi nyama yanji.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 19

MAFUNSO

A. Kuti adzipeza zofunikira pamoyo, Paulo ankagwira ntchito yopanga ․․․․․.

B. Mtumwi Paulo ankaphunzitsa anthu “poyera komanso . . . ”

C. Paulo anaukitsa mnyamata wina dzina lake ․․․․․.

[Tchati]

4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

1 C.E.

Anakhala ndi moyo m’nthawi ya atumwi

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

Anabadwira ku Tariso. Anagwira ntchito ya umishonale ku Europe ndi Asia Minor

EUROPE

Rome

ASIA MINOR

Tariso

Yerusalemu

PAULO

ANALI NDANI?

Poyamba ankazunza Akhristu koma anasintha n’kukhala mtumwi wolalikira anthu a mitundu ina. Yehova anamugwiritsa ntchito kulemba mabuku 14 a Malemba Achigiriki Achikhristu. Paulo anayenda maulendo ataliatali pa ntchito yake ya umishonale ndipo anayambitsa mipingo yambiri ku Europe ndi Asia Minor.—Aroma 11:13; 1 Timoteyo 1:12-16.

MAYANKHO

A. mahema.—Machitidwe 18:3-5.

B. “. .  kunyumba ndi nyumba.”—Machitidwe 20:20.

C. Utiko.—Machitidwe 20:7-12.

Anthu ndi Mayiko

3. Mayina athu ndi Maté ndi Nia ndipo tili ndi zaka 7 ndi 8. Timakhala m’dziko la Georgia. Kodi mukudziwa kuti ku Georgia kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 10,000; 17,000, kapena 26,000?

4. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Georgia.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti, “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba  26

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Mbalame.

2. Nyama zakutchire.

3. 17,000.

4. B