Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nthawi Yabwino Yoyambira Kuphunzitsa Mwana Ndi Iti?

Kodi Nthawi Yabwino Yoyambira Kuphunzitsa Mwana Ndi Iti?

Kodi Nthawi Yabwino Yoyambira Kuphunzitsa Mwana Ndi Iti?

● Bambo wina wa m’tauni ya Summerville, ku South Carolina, m’dziko la United States, analemba zimene ankachita mkazi wake ali woyembekezera ndi miyezi itatu. Iye anafotokoza kuti usiku uliwonse ankawerenga buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo atagona pafupi ndi mkazi wake. Bamboyu anafotokoza kuti: “Mwana wathu wamkazi, Bethiah, atabadwa tinkamuwerengera mutu umodzi usiku uliwonse. Tinawerenga bukuli kokwanira katatu.”

Iye ananenanso kuti: “Mwanayu akuphunzira kulankhula ankatha kudziwa anthu osiyanasiyana a m’Baibulo komanso kuyerekezera zochitika zosiyanasiyana za m’Baibulo zomwe anazifotokoza m’bukuli. Ankathanso kufotokoza nkhani za m’Baibulo osaonera.”

Bukuli lili ndi nkhani zokwanira 116 zokhala ndi zithunzi zokongola. Limafotokoza nkhani za anthu a m’Baibulo, kuyambira pa Adamu ndipo zimenezi zimathandiza kuti munthu akamawerenga adziwe nthawi imene anthu osiyanasiyana anakhalapo. Mukhoza kuitanitsa buku la masamba 256 limeneli polemba zofunika m’munsimu n’kutumiza ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.