Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zoyenera Kubera Mayeso?

Kodi N’zoyenera Kubera Mayeso?

Kodi N’zoyenera Kubera Mayeso?

KODI mudakali pasukulu? Ngati ndi choncho muyenera kuti mukudziwa anzanu ena amene amabera kapena kuonera mayeso n’cholinga choti akhoze bwino. Anthu ambiri amakonda kubera mayeso. Mwachitsanzo, mu 2008, bungwe lina ku United States linachita kafukufuku pa ana a sukulu 30,000 a ku sekondale. Bungweli linapeza kuti ana 64 pa ana 100 alionse anabera mayeso a chaka chimenecho. Ena amanena kuti n’kutheka kuti ana amene anabera mayeso chaka chimenecho anali ambiri kuposa amenewa. Iwo amati chiwerengero chenicheni chikhoza kukhala ana 75 pa 100 alionse.

Vuto limeneli lakulanso kwambiri ku Europe ndipo magazini ina inanena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano pa Intaneti pakumapezeka mayeso olembalemba kale oti mwana wasukulu akhoza kugula n’kumakhala ngati walemba ndi iyeyo.”—Digithum.

N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano akubera mayeso? Kodi anthu amene amachita zimenezi amapindula chiyani? Kodi mukuganiza kuti ndi nzeru kupewa kubera mayeso, ngakhale kuti mwina ukapanda kubera simungakhoze bwino?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amabera Mayeso?

Anthu alibenso makhalidwe abwino. Magazini ina inanena kuti: “Aphunzitsi ambiri amanena kuti anthu ambiri masiku ano amakonda kubera mayeso chifukwa chodzikonda komanso chifukwa anthu alibenso makhalidwe abwino.” (American School Board Journal) Mtsikana wina ananena kuti: “Kalasi yathu yonse . . . inabera mayeso chifukwa aliyense ankafuna kuti amusankhire ku yunivesite. Sikuti tinali ana ovuta, koma tinangochita zimenezi kuti tikhoze basi.” Makolo enanso amaona kuti palibe vuto ana awo akamabera mayeso chifukwa amafuna kuti anawo apeze maphunziro abwino. Choncho amawalimbikitsa kuti azibera mayeso kapena amangonyalanyaza osawadzudzula akadziwa kuti abera mayeso. Zimenezi zimawononga khalidwe la ana.

Kufuna kukhoza. Munthu wina, dzina lake Donald McCabe, ananena kuti, ana ena asukulu amabera mayeso chifukwa amaona kuti anzawo amene amabera mayeso amakhoza bwino ndipo sagwidwa. Choncho iwo amayambanso kubera n’cholinga choti akhoze bwino.

Zipangizo zamakono. Kubwera kwa mafoni am’manja ndi Intaneti kwachititsanso kuti anthu asamavutike kubera mayeso. Mwina amatha kukopera mayankho a mayeso pa Intaneti n’kugawana ndi anzawo. Ambiri sagwidwa ndipo zimenezi zimachititsa kuti ena ayambenso kubera mayeso.

Kutengera anthu ena. Si ana okha amene amachita zachinyengo, anthu akuluakulunso amachita zachinyengo pa nkhani za bizinezi, zandale ndi zamasewera. Nthawi zinanso ana amayamba zachinyengo chifukwa choona kuti makolo awo amachita zachinyengo pa nkhani yopereka msonkho. Munthu wina, dzina lake David Callahan, analemba m’buku lake kuti: “Ndikuganiza kuti ngati anthu otchuka kapena amaudindo apamwamba akuchita zachinyengo, ndiye kuti ana akhoza kumaona kuti palibe vuto ndi kubera mayeso.” Koma kodi kubera mayeso kulibedi vuto lililonse? Kodi munthu akabera mayeso n’cholinga choti akhoze bwino, ndiye kuti sanalakwitse chilichonse?

N’chifukwa Chiyani Simuyenera Kubera Mayeso?

Dzifunseni kuti, ‘N’chifukwa chiyani munthu amapita kusukulu?’ Nthawi zambiri munthu amapita kusukulu kuti akaphunzire zinthu zimene zingadzamuthandize m’tsogolo. Mwachitsanzo amakaphunzira zimene angachite akakumana ndi mavuto kuntchito. Koma ana amene amakonda kubera mayeso sangadzathe kuchita zimenezi akadzakula. Choncho, anthu amene amakonda kuchita zachinyengo amaoneka ngati odziwa zinthu koma pambuyo pake zinthu sizimawayendera bwino.

Callahan ananenanso kuti: “Anthu amene anayamba kuchita zachinyengo ali kusukulu, amachitanso zachinyengo ngakhale kuntchito.” Anthu amene amabera mayeso n’cholinga choti azioneka ngati anzeru, tingawayerekezere ndi wotchi yooneka ngati yolimba koma ili ya feki.

Ana amene amabera mayeso akhoza kugwidwa pamapeto pake ndipo akhoza kuchita manyazi, kuchotsedwa sukulu kapena kulandira chilango chowawa. Baibulo limachenjeza kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Komabe munthu ayenera kupewa kuchita zachinyengo osati chifukwa chongoopa kugwidwa. Pali zifukwa zomveka zopewera khalidweli.

Ochita Chilungamo Zinthu Zimawayendera

Achinyamata anzeru amayesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angadzawathandize akadzakula. Choncho amalimbikira sukulu komanso amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino zomwe zimachititsa kuti ena aziwalemekeza. Makhalidwe amenewa angadzawathandize kuntchito zomwenso zingachititse kuti azidzasangalala pa moyo wawo.

Makhalidwe abwino amenewo amapezeka m’Baibulo ndipo achinyamata amene amaphunzira komanso kuchita zimene Baibulo limanena, zinthu zimawayendera. Komanso lemba la 2 Timoteyo 3:16, 17 limanena kuti achinyamata otere amakhala okonzeka “mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.” Mnyamata wina yemwe ali pa sukulu dzina lake Jorge, ananena kuti: “Anthu a m’kalasi mwathu amabera mayeso kuti akhoze bwino. Koma ineyo sindichita nawo chifukwa ndimafuna kukondweretsa Mulungu. Lemba la Miyambo 14:2 limanena kuti: ‘Munthu woyenda mowongoka mtima amaopa Yehova, koma munthu amene amayenda m’njira zokhotakhota amanyoza Mulungu.’ Ndimadziwa kuti Mulungu amaona chilichonse. N’chifukwa chake sindibera mayeso kapena kuthandiza ena kubera mayeso.”

Mwina ana amene amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limanena sangamakhoze kwambiri m’kalasi. Komabe Mulungu amawaona kuti ndi anzeru chifukwa akuchita zimene zingadzawathandize kudzakhala ndi moyo wosangalala. (Salimo 1:1-3; Mateyu 7:24, 25) Komanso Mulungu amakonda ndiponso kuthandiza ana amene amayesetsa kupewa kubera mayeso.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 28]

MFUNDO ZOTI MUZIKUMBUKIRA

● “Mlomo wa choonadi ndi umene udzakhazikike kwamuyaya, koma lilime lachinyengo lidzangokhalapo kwa kanthawi.”—Miyambo 12:19.

● “Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri.”—Miyambo 28:20.

● “Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.”—Mlaliki 12:14.

● “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

Kubwera kwa mafoni am’manja ndi Intaneti kwachititsa kuti anthu azibera mayeso mosavuta

[Chithunzi patsamba 28]

Ana amene amabera mayeso tingawayerekezere ndi wotchi yooneka ngati yolimba koma ili ya feki