Ndinkakonda Kuchita Zachiwawa
Ndinkakonda Kuchita Zachiwawa
Yosimbidwa ndi Salvador Garza
NDILI mwana ndinkakonda kwambiri kuchita zachiwawa, moti ndinkamenyana ndi wina aliyense amene wandiputa. Kenako munthu winawake ananditenga n’kuyamba kundiphunzitsa nkhonya. Pasanapite nthawi, ndinakhala katswiri moti ndinkakamenya nkhonya m’madera osiyanasiyana m’dziko la United States. Kenako ndinayamba kugwira ntchito yoteteza munthu wina yemwe anali mkulu wa zigawenga.
Ndinakwatira n’kukhala ndi ana 6 koma ndinapitirizabe kuchita zachiwawa. Pa nthawiyi ndinali ndi bizinezi yogulitsa mowa. Ngakhale kuti anthu ena anayesa kundipha kangapo konse chifukwa chochita zachiwawa, ndinapitirizabe khalidwe limeneli. Ndimakumbukira kuti tsiku lina ndinayamba kumenyana ndi anthu ena ndipo ndinawombera anthu awiri moti anavulala kwambiri. Nthawi inanso ine ndi anzanga tinakonza zoti tigwire munthu winawake wandale yemwe anali wotchuka kwambiri. Koma apolisi anadziwa zimene tinkafuna kuchita ndipo anandimanga. Koma atapita kuti akagwire anzanga aja, anayamba kuomberana moti anzanga onse anaphedwa. Panopa ndimasangalala chifukwa ndimadziwa kuti akanapanda kundigwira ndikanafera limodzi ndi anzangawo.
Ananditulutsa patapita zaka zingapo ndipo ndinapeza ntchito. Pa nthawiyi n’kuti mkazi wanga, Dolores, akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anandiuza kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. (Salimo 83:18) Tsiku lina nditaweruka, ndinayamba kudwala mutu waukulu ndipo ndinachita mantha kwambiri. Kenako ndinakumbukira kuti mkazi wanga anali atandiuzapo kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Choncho ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize.
Nditachira, mkazi wanga anandilimbikitsa kuti ndipite nawo ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Kumisonkhanoko, ndinaona kuti a Mboni za Yehova anandilandira bwino moti zinandikhudza mtima kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kuphunzira Baibulo ndipo ndinayamba kusintha. Ndinkasangalala kwambiri ndi zimene ndinkaphunzira.
Komabe zinanditengera nthawi kuti ndiyambe kuchita zinthu moleza mtima. Mwachitsanzo, tsiku lina tikulalikira nyumba ndi nyumba ndi mnzanga Antonio, tinakumana ndi munthu wina amene anatinyoza. Ndinakwiya kwambiri moti ndinayamba kumulondola kuti ndimumenye. Mwamwayi, Antonio anandigwira. Ndiyeno nthawi ina, Antonio anandikumbutsa mokoma mtima zimene Petulo, yemwe anali wophunzira wa Yesu ananena. Petulo ananena kuti: “Pamene [Yesu] anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe.” (1 Petulo 2:23) Mawu amenewo anandikhudza kwambiri.
Ndikakumbukira mmene ndinalili kale, nthawi zonse ndimathokoza Yehova chifukwa chondipatsa mzimu wake woyera womwe wandithandiza kuti ndizidziletsa komanso kuti ndizikonda kuchita zinthu mwamtendere. (Agalatiya 5:22, 23) Panopa m’banja mwathu timasangalala ndiponso ndife ogwirizana. Ndimagwiranso ntchito yolalikira nthawi zonse ndipo ndimasangalala kuthandiza anthu kuti apeze mtendere wochokera kwa Mulungu.
[Chithunzi patsamba 9]
Salvador anayamba kuchita zinthu mwamtendere chifukwa chophunzira Baibulo