Zachiwawa Zili Paliponse
Zachiwawa Zili Paliponse
MASIKU ano anthu ambiri akukonda zachiwawa. N’zoona kuti kale nyimbo ndi mafilimu ambiri ankakhala achiwawa. Komabe bungwe lina linanena kuti: “Masiku ano zinthu zasintha kwambiri moti pafupifupi chilichonse chimene munthu angaonere kapena kumvera chikumakhala chachiwawa, cholimbikitsa zachiwerewere ndiponso kuchitirana nkhanza.” (Media Awareness Network) Mwachitsanzo, taganizirani izi:
Nyimbo: Bungwe lomwe talitchula kale lija linanenanso kuti: “Oyimba sakuona vuto lililonse ndi nyimbo zolimbikitsa zachiwawa.” Nyimbo zambiri zikumakhala zotukwana, zolimbikitsa anthu kupha anzawo komanso kugwiririra. Ndiponso zikumalimbikitsa amuna kugwiririra akazi awo kapena amayi awo.
Masewera a pa Kompyuta: Magazini ina ya ku Britain inanena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti masewera a pa kompyuta akumasonyeza anthu akuphana. Nthawi zambiri munthu amene akumakonda masewera a pa kompyuta akumakhala woti amakondanso zachiwawa.” Mwachitsanzo, masewera
enaake a pa kompyuta otchuka kwambiri amafuna kuti munthu wosewerayo azimenya azimayi ndi chindodo mpaka kuwapha. Akuluakulu a boma m’mayiko ena akukhulupirira kuti ana amene amakonda masewera a pa kompyuta amakhala achiwawa poyerekezera ndi ana amene amakonda kuonera TV.Mafilimu: Kafukufuku akusonyeza kuti mafilimu ambiri akumakhala achiwawa, osonyeza zachiwerewere komanso otukwana. Mafilimu ena amasonyeza zaka za munthu amene akuloledwa kuonera filimuyo komabe nthawi zambiri mafilimuwa amakhala oipa. Kafukufuku winanso anasonyeza kuti m’mafilimu ambiri anthu amene amawasonyeza kuti ndi abwino amachita zachiwawa.
Nkhani za pa TV: Akatswiri ambiri opanga mapulogalamu a pa TV amayesetsa kuika zachiwawa m’mapulogalamu awo chifukwa amadziwa kuti n’zimene anthu amakonda. Komanso makampani a TV amapanga ndalama zambiri akamaonetsa nkhani zachiwawa. Zimenezi zimachitika chifukwa m’mayiko ena makampani amakonda kutsatsa malonda awo panthawi imene akuonetsa pulogalamu yachiwawa chifukwa amadziwa kuti anthu ambiri akuonera.
Intaneti: Pa Intaneti pamapezeka zithunzi kapena mavidiyo osonyeza anthu akuzunzidwa, akuphedwa komanso akudulidwa ziwalo zosiyanasiyana. N’zomvetsa chisoni kuti ana ambiri amakonda kuonera zimenezi.
Samalani ndi Zimene Mumamvera Komanso Kuonera
Koma kodi zachiwawa zimene amazisonyeza pa TV, m’mafilimu, m’mabuku komanso m’nyimbo zingachititsedi kuti munthu azichita zachiwawa? Anthu amene amapeza ndalama zambiri chifukwa chokonza komanso kuonetsa mafilimu amenewa amadziikira kumbuyo ndipo amanena kuti mafilimu awo alibe vuto lililonse. Koma taganizirani mfundo iyi: Makampani amawononga ndalama zambiri kutsatsa malonda awo, omwe mwina amangotenga masekondi 30 okha. Koma cholinga chawo chachikulu n’chakuti anthu agule katundu wawo ndipo anthu amaguladi. Ngati anthu amachita zimene aona m’masekondi ochepa chonchi, ndiye kuti akhozanso kuchita zachiwawa kapena zoipa zimene aona mu filimu, yomwe nthawi zambiri imatenga mphindi 90. Mafilimu amenewa ndi oipa kwambiri makamaka kwa ana chifukwa sachedwa kutengera zimene amaona.
Mlengi wathu, amatidziwa bwino kwambiri kuposa mmene ifeyo timadzidziwira. N’chifukwa chake anatipatsa malangizo oti tizipewa kucheza ndi anthu achiwawa. Njira imodzi imene munthu angachezere ndi anthu achiwawa ndi kuonera mafilimu achiwawa. Ena mwa malangizo amene Mlengi wathu anatipatsa ndi awa:
● “Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe, ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Salimo 11:5.
● “Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya, ndipo usamayende ndi munthu waukali, kuti usazolowere njira zake ndi kuikira moyo wako msampha.”—Miyambo 22:24, 25.
N’zoona kuti sitingapeweretu kuona zinthu zoipa. Koma tikhoza kusankha nyimbo kapena mafilimu omwe si achiwawa komanso kusankha anthu abwino ocheza nawo. Choncho mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimafuna nditakhala munthu wotani?’ Kenako muzicheza ndi anthu amene ali ndi makhalidwe omwe mumafuna mutakhala nawo.—Miyambo 13:20.
Kuwonjezera pa anthu amene timacheza nawo, zimene timamvera, kuonera komanso kuwerenga, palinso zinthu zina zimene zingatichititse kuti tizikonda zachiwawa. Kodi zinthu zimenezi ndi ziti?
[Chithunzi patsamba 4]
Zimene timamvera, kuonera komanso kuwerenga zingatichititse kuti tizikonda zachiwawa