Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI KWA . . . Kaini ndi Abele?

KODI MUNAYAMBA MWAPSAPO MTIMA MPAKA KUFUNA KUMENYA M’BALE WANU?

• Kongoletsani zithunzizi ndi chekeni. • Werengani mavesiwa ndipo muwafotokoze pomalizitsa mawu amene akusoweka. • Pezani zinthu zimene zikusoweka: (1) apulo ndi (2) bakha.

GENESIS 4:2

GENESIS 4:3

MULUNGU ANASANGALALA NDI ABELE NDIPO ANALANDIRA NSEMBE YAKE.—GENESIS 4:4

GENESIS 4:5

GENESIS 4:8 ․․․․․

KENAKO, MULUNGU ANAFUNSA KAINI KUTI: “ ․․․․․ ?”​—GENESIS 4:9

GENESIS 4:10-12

N’chifukwa chiyani muyenera kupewa kupsa mtima kwambiri?

ZOKUTHANDIZANI: Miyambo 14:29; Aefeso 4:26, 27, 31.

N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamapse mtima kwambiri?

ZOKUTHANDIZANI: Miyambo 14:30; 19:11; Aefeso 4:32.

Kodi mwaphunzirapo chiyani mu nkhaniyi?

Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Werengani Genesis 4:7. Kodi Kaini anayenera kuchita chiyani Mulungu atamupatsa malangizo?

ZOKUTHANDIZANI: Luka 14:11; 1 Petulo 5:5, 6.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 20 NOWA

MAFUNSO

A. Nowa anakhala ndi moyo kwa zaka ․․․․․.

B. Tchulani mayina a ana Nowa.

C. Malizitsani mawu a m’Baibulo awa: “Nowa anachita zonse motsatira . . . ”

[Tchati]

4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

1 C.E.

Anabadwa mu 2970 B.C.E.

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

“Chingalawacho chinaima pamapiri a Ararati.” —Genesis 8:4

MAPIRI A ARARATI

NOWA

ANALI NDANI?

Anaphunzitsa anthu a m’banja lake kuti azimvera malangizo a Yehova. Iye anamvera Mulungu ndipo anamanga chingalawa kuti apulumutse banja lake ndi zinyama panthawi ya chigumula. (Genesis 6:5-22) Ngakhale kuti ankanyozedwa, iye anapirira ndipo anapitirizabe kugwira ntchito monga “mlaliki wa chilungamo.”—2 Petulo 2:5; Aheberi 11:7.

MAYANKHO

A. 950.—Genesis 9:29.

B. Semu, Hamu ndi Yafeti.—Genesis 6:10.

C.“. . . zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.”—Genesis 6:22.

Anthu ndi Mayiko

3. Mayina athu ndi Andres ndi Ana ndipo tonse tili ndi zaka 11. Timakhala ku El Salvador. Kodi mukudziwa kuti ku El Salvador kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 10,000; 20,700, kapena 37,000?

4. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la El Salvador.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti, “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 12

Mayankho A Mafunso A Patsamba 30 Ndi 31

1. Patsogolo pa guwa la nsembe, lomwe lili pachithunzi chachitatu, pali apulo.

2. Pachithunzi chachinayi, bakha ali pakati pa Abele ndi nkhosa.

3. 37,000.

4. A.