Kodi Zinangochitika Zokha?
Gulu la Nsomba Losambira Mogometsa
Chaka chilichonse, anthu oposa 1 miliyoni amafa magalimoto akawombana ndipo pafupifupi 50 miliyoni amavulala. Koma nsomba zimatha kuyenda pagulu lalikulu osawombana. Kodi nsomba zimatha bwanji kuchita zimenezi ndipo ifeyo tingaphunzire chiyani chomwe chingatithandize kuti ngozi za magalimoto zichepe?
Taganizirani izi: Nsomba ikamayenda m’chigulu imagwiritsa ntchito maso komanso kachiwalo kena kamene kamaithandiza kudziwa ngati yayandikana kwambiri ndi nsomba inzake. Ziwalo zimenezi zimathandiza nsomba m’njira zitatu zotsatirazi:
-
Zimayendera limodzi. Nsomba iliyonse imayesetsa kuti iziyenda paliwiro lofanana ndi nsomba zimene zili pambali pake ndipo imayesetsa kuti isayandikane nazo kwambiri.
-
Sizimathawana. Nsomba iliyonse ikaona kuti ikutsalira kwambiri imayesetsa kuti iyandikane ndi nsomba zinzake.
-
Zimapewa kugundana. Nsomba ikaona kuti igundana ndi inzake imatha kusintha njira.
Potengera mmene nsombazi zimayendera, kampani ina ya ku Japan yopanga magalimoto, inapanga timagalimoto toyerekezera tomwe timayenda tambirimbiri nthawi imodzi koma osawombana. Timagalimototi tili ndi zipangizo zoyendera kompyuta zomwe zimathandiza kuti tisawombane. Kampaniyi inanena kuti zimenezi ziwathandiza kuti apange magalimoto omwe sangamawombane ndi zinzake. Akukhulupiriranso kuti zimenezi “zithandiza kuti apange magalimoto osawononga zachilengedwe komanso zithandiza kuti m’misewu musamadzazane magalimoto.”
Mkulu amene akuyang’anira ntchito yopanga magalimoto amenewa, dzina lake Toshiyuki Andou, ananena kuti: “Tikufuna kupanga magalimoto amakono potengera mmene nsomba zimayendera zikakhala pagulu. Tonse tingaphunzire zambiri poona mmene gulu la nsomba limachitira zinthu.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti gulu la nsomba liziyenda mogometsa chonchi, kapena ndi umboni woti pali wina amene anazilenga?