Mandimu Amagwira Ntchito Zosiyanasiyana
MANDIMU ndi chipatso chofunika kwambiri chifukwa amagwira ntchito zosiyanasiyana monga kutsukira ziwiya, kuphera tizilombo toyambitsa matenda, kupangira mafuta odzola komanso amagwiritsidwa ntchito ngati mankhwala. Mukhoza kuwadya aawisi, kupangira juwisi komanso kuchotsamo mafuta ena ofunikira. Mandimu amaoneka okopa kwambiri ndipo amapezeka m’madera ambiri padziko lapansi komanso ndi otchipa moti anthu ambiri savutika kuwapeza.
Anthu ena amanena kuti mandimu anachokera ku Southeast Asia. Pang’ono ndi pang’ono mbewu ya mandimu inayamba kufalikira m’madera a kufupi ndi nyanja ya Mediterranean. Mitengo ya mandimu imakula bwino m’madera otenthera. N’chifukwa chake imapezeka kwambiri m’madera monga ku Argentina, Italy, Mexico, Spain komanso madera ena a ku Africa ndi Asia. Mtengo umodzi umatha kubereka mandimu 200 kapena 1,500 pa chaka mogwirizana ndi mtundu wake komanso malo amene unabzalidwa. Mitundu yosiyanasiyana ya mandimu imaberekanso panyengo zosiyanasiyana pachaka zomwe zimachititsa kuti mandimu asamasowe.
Mandimu Ndi Odziwika Kwambiri ku Italy
Anthu amasiyana maganizo pa mfundo yakuti anthu a ku Roma ankadzala mandimu kapena ayi. Koma pali umboni woti Aroma ankadziwa bwino za mtundu winawake wa chipatso chomwe chimafanana ndi mandimu. Buku lakuti Natural History limene Pliny Wamkulu analemba, limatchula za chipatso chimenechi. Komabe, akatswiri ena amanena kuti Aroma ankadziwa bwino kwambiri mandimu. Iwo amanena zimenezi chifukwa zithunzi zakale za ku Roma zojambulidwa m’makoma, zimasonyeza mandimu enieni osati chipatso chofanana ndi mandimu. Chitsanzo cha zimenezi ndi zithunzi zomwe zili pakhoma la nyumba ina yakale kwambiri yomwe ili ku Pompeii. Nyumbayi imadziwika kuti ndi nyumba yazipatso ndipo pamakoma ake anajambulapo zithunzi zambiri za zipatso, kuphatikizapo mandimu. Koma zikuoneka kuti poyamba mitengo ya mandimu ankangoigwiritsa ntchito ngati mankhwala. Sitingathe kudziwa kuti ankalima bwanji mandimu komanso ngati ankapezeka mosavuta.
Nyengo ya pachilumba cha Sicily, ndi yotenthera bwino ndipo zimenezi zachititsa kuti azibzala zipatso zambiri ngati malalanje, manachesi ndi mandimu.
Koma mandimu abwino kwambiri amalimidwa m’madera a m’mphepete mwanyanja pachilumba chimenechi.Tauni yokongola kwambiri ya Sorrento ili kum’mwera kwa mzinda wa Naples ndipo kum’mwera kwa mzindawo kuli gombe lotchedwa Amalfi lomwe ndi lalitali makilomita 40. Kufupi ndi gombeli kulinso matauni okongola monga Amalfi, Positano, ndi Vietri sul Mare. Kumagombe a Sorrento ndi Amalfi kumalimidwa mandimu omwe amawaika chizindikiro chosonyeza kuti amalimidwa kumeneko. Anthu akumeneko salakwitsa kuteteza mandimu awowo chifukwa mandimuwo amalimidwa m’mphepete mwa mapiri, zomwe zimachititsa kuti azikhala onunkhira bwino komanso a madzi ambiri.
Mtengo wa mandimu sufuna malo aakulu. Ukhoza kumera ngakhale m’mphepete mwa khonde, momwe mumafika dzuwa. Komanso mtundu wina wa mandimu omwe mtengo wake sutalika kwambiri, ukhoza kukula bwino m’chitini ngati maluwa. Mitengoyi imakula bwino pamalo omwe pamafika dzuwa komanso pomwe sipawomba mphepo yambiri monga pafupi ndi khoma. Koma m’nyengo yozizira, pamafunika kuuphimba ndi chinachake kapena kuuika m’nyumba.
Amagwira Ntchito Zosiyanasiyana
Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito mandimu pa zinthu ziti? Ena amathira mu tiyi pomwe ena amafinyira madzi ake mu keke. Kapenanso mungapangire juwisi. Akatswiri a zophikaphika padziko lonse amaonetsetsa kuti ali ndi mandimu nthawi iliyonse pamene akuphika. Komanso mungagwiritse ntchito madzi a mandimu pophera tizilombo toyambitsa matenda kapena kuchotsera zothimbirira.
Anthu ena amagwiritsa ntchito mandimu potsukira zipangizo zodulira ndiwo. M’malo mogwiritsa ntchito jiki potsukira pasinki, ena amagwiritsa ntchito madzi a mandimu osakaniza ndi soda. Enanso amaika kapisi kamandimu mufiriji kapena m’madzi otsukira mbale kuti zizimveka kafungo kabwino.
Mandimu ali ndi mchere winawake womwe umathandiza kuti zinthu zisawole komanso amathandiza kuti zakudya zina ziziwawasira. M’mandimu mumapezekanso zinthu zina zimene makampani opanga zakudya amazigwiritsa ntchito kuti chakudya chizikhala cholimbirako komanso kuti chisakhale ndi mafuta ambiri. Kuwonjezera pamenepa, makoko a mandimu amakhala ndi mafuta enaake amene amawagwiritsa ntchito popangira mankhwala, zodzoladzola komanso kuthira mu zakudya zina. Titati tinene ntchito zonse za mandimu tikhoza kuchezera. Kunena zoona mandimu ndi chipatso chokongola, chonunkhira bwino komanso chimagwiritsidwa ntchito pa zinthu zosiyanasiyana.